Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Njira Zochizira Popanda Kuika Magazi

Njira Zochizira Popanda Kuika Magazi

PA May 20 mpaka pa 22, 2011, madokotala ochokera m’mayiko oposa 40 anakumana mu mzinda wa Moscow pa mwambo wokondwerera kuti patha zaka 60 chikhazikitsireni bungwe la madokotala loona za opaleshoni ya mtima komanso ya mitsempha. Mtolankhani wa pa TV ya ku Russia ananena kuti: “Mwambo umenewu ndi wofunika kwambiri kwa madokotala ngati mmene mpikisano wa Olympics ulili wofunika kwa akatswiri a zamasewera.”

Msonkhanowu unachitika kwa masiku atatu ndipo anthu ambiri anachita chidwi ndi pamalo ena, pomwe ankafotokozapo za njira zochizira matenda popanda kuika magazi. Pamalowa panali a Mboni za Yehova a mu Dipatimenti Yopereka Chidziwitso cha Zachipatala. Madokotala ambiri anatenga mabuku, ma DVD ndi timapepala tofotokoza njira zimenezi. Koma madokotala ambiri anakonda DVD yonena za njira zochizira popanda kuika magazi ya mutu wakuti Transfusion-Alternative Strategies—Simple, Safe, Effective. *

Madokotala ambiri amene anapita pamalowa anavomereza kuti popanga opaleshoni m’pofunika kusamala kuti magazi ambiri asamatayike. Dokotala wina wa ku Italy, amene amapanga maopaleshoni a mtima, ananena kuti akudziwa bwino zimene a Mboni za Yehova amakhulupirira pa nkhani ya magazi ndipo wapangapo maopaleshoni anthu a Mboni pafupifupi 70, popanda kuwaika magazi. Iye ananenanso kuti nthawi zambiri pachipatala chake amapanga opaleshoni popanda kuika magazi. Pulofesa wina wophunzitsa madokotala opaleshoni ya mtima ku Germany anatenga ma DVD awiri, ina yake ina ya mnzake wogwira naye ntchito. Iye anauza anthu amene anafika pamsonkhanowo kuti anali atangopanga kumene opaleshoni yamtima yosaika magazi mwana wina wakhanda, yemwe ankalemera makilogalamu awiri ndi hafu okha. Anafotokozanso kuti wakhala akuchita opaleshoni yamtima kwa ana aang’ono kwambiri kuposa ameneyu popanda kuwaika magazi.

Patatha mwezi umodzi chichitikire msonkhano umenewu, madokotala ochokera m’mayiko osiyanasiyana anakumananso, m’tauni ya Belomorsk yomwe ili mu mzinda wa Arkhangel’sk m’dziko la Russia. Madokotalawa anali pa msonkhano wanambala 4 wokambirana za kuchita opaleshoni pogwiritsa ntchito mankhwala ochititsa dzanzi komanso mmene angasamalirire anthu odwala mwakayakaya. A Mboni ajanso analipo pa msonkhano umenewu ndipo anthu ambiri anachita chidwi ndi zimene anabweretsa. Dokotala wina wa ku St. Petersburg ataona zimene a Mboniwo anabweretsa ananena kuti: “Madokotala timafunika zinthu ngati zimenezi.” Iye anadandaula kuti madokotala anzake anazolowera kuika magazi anthu odwala ngakhale opsa ndi moto omwe. Dokotalayu anapitiriza kunena kuti: “Zinthu zimene mwandipatsazi zikatithandiza kwambiri pa msonkhano wina womwe ukachitikire ku St. Petersburg wokambirana za mmene tingathandizire anthu amene apsa ndi moto.”

Padziko lonse madokotala ayamba kuona ubwino wothandiza anthu popanda kuwaika magazi. Mwina mtsogolo muno madokotala onse azidzathandiza anthu popanda kuwaika magazi.

^ ndime 3 Yopangidwa ndi Mboni za Yehova.