Zoti Banja Likambirane
Kodi Chithunzichi Chalakwika Pati?
Werengani Luka 17:11-19. Tchulani zinthu zitatu zimene zalakwika pachithunzichi. Lembani mayankho anu m’mizere ili m’munsiyi, ndipo malizitsani kujambula zithunzizi pozikongoletsa ndi chekeni.
KAMBIRANANI:
Kodi munthu m’modzi wakhate anachita chiyani chomwe anzake sanachite?
ZOKUTHANDIZANI: Werengani Luka 17:15, 16.
Kodi mungatsatire bwanji chitsanzo chake?
ZOKUTHANDIZANI: Werengani Akolose 3:15; 1 Atesalonika 5:18.
Kodi muyenera kuthokoza ndani tsiku ndi tsiku?
ZOKUTHANDIZANI: Werengani Salimo 107:8; Yakobo 1:17.
ZOTI BANJA LICHITIRE PAMODZI:
Pemphani anthu onse a m’banja mwanu kuti alembe chifukwa chimodzi chimene amathokozera Yehova Mulungu, munthu wa m’banjamo komanso mnzake yemwe si wa m’banjamo. Kenako lembani zimene mungachite posonyeza kuti mumayamikira anthu amene mwawalembawo.
Sungani Kuti Muzikumbukira
KHADI LA BAIBULO 21 MOSE
MAFUNSO
A. Kodi Yehova anauzira Mose kulemba mabuku a m’Baibulo ati?
B. Makolo a Mose anali a ․․․․․ ndi a ․․․․․. Analeredwa ndi ․․․․․ ․․․․․.
C. Malizitsani mawu a m’Baibulo akuti: Mose “anapitiriza kupirira moleza mtima . . . ”
ANALI NDANI
Anali munthu woyamba m’Baibulo kupatsidwa mphamvu zochita zozizwitsa, anali mneneri wa Mulungu, ankaweruza Aisiraeli, kuwapatsa malamulo komanso kuwatsogolera. Aisiraeli ankaona kuti Mose anachita zinthu zambiri zodabwitsa.—Deuteronomo 34:10-12; Ekisodo 4:1-9.
MAYANKHO
A. Genesis, Ekisodo, Levitiko, Numeri, Deuteronomo, Yobu ndi Salimo 90 mwinanso Salimo 91.
B. Amuramu, Yokebedi, mwana wamkazi wa Farao.—Ekisodo 1:15–2:10; 6:20.
C. “. . . ngati kuti akuona Wosaonekayo.”—Aheberi 11:27.
Anthu ndi Mayiko
4. Dzina langa ndine Mampionona. Ndili ndi zaka 8 ndipo ndimakhala ku Madagascar. Kodi mukudziwa kuti ku Madagascar kuli Mboni za Yehova zingati? Kodi ziliko 10,000; 24,000 kapena 62,000?
5. Kodi ndi kadontho kati kamene kakusonyeza dziko limene ineyo ndimakhala? Lembani mzere wozungulira kadonthoko. Kenako jambulani kadontho kosonyeza kumene inuyo mumakhala kuti muone kuyandikana kwa dziko lanu ndi la Madagascar.
Zithunzi Zoti Ana Apeze
Pezani zithunzi izi m’magazini ino. Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.
MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 30 NDI 31
-
Payenera kukhala akhate 10 osati 11.
-
Nkhaniyi imasonyeza kuti akhatewo anali amuna okhaokha.
-
Wakhate amene anabwerera “anagwada pamaso pa Yesu n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi, ndipo anamuthokoza.”
-
24,000.
-
B.