Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungatani Kuti Zizikuyenderani ku Sukulu?

Kodi Mungatani Kuti Zizikuyenderani ku Sukulu?

Pa mawu ali m’munsiwa, kodi ndi mawu ati amene akufotokoza mmene inuyo mumaonera sukulu?

  • Yotopetsa kapena yosangalatsa?

  • Yovuta kapena yopindulitsa?

  • Yosafunika kapena yothandiza?

Ngati inuyo mumaona kuti sukulu ndi yosasangalatsa, kodi mungatani kuti muyambe kuikonda? Ngati mumaikonda, kodi mungatani kuti mupindule nayo kwambiri? Patsamba 3 mpaka 7, pali mfundo zisanu za m’Baibulo, zomwe zingakuthandizeni kuti zinthu zizikuyenderani bwino ku sukulu.