Zimene Achinyamata Amadzifunsa
Kodi Ndiziyembekezera Chiyani M’banja?—Gawo 2
MU GAWO 1, tinakambirana zinthu zabwino komanso mavuto amene mungayembekezere m’banja.
MU NKHANI INO, tikambirana mfundo zimene zingakuthandizeni ngati mwakumana ndi zinthu zimene simumaganizira kuti zingachitike.
Chongani chonchi ✔ pa kabokosi kali ndi zinthu zimene mumafuna, kenako lembani nambala pambali pa kabokosi kamene mwachongako, kuyambira ndi zimene mukuona kuti ndi zofunika kwambiri kwa inu.
Ndimafuna kuti amene ndidzakwatirane naye adzakhale . . .
-
wooneka bwino
-
woti azidzandiyamikira
-
ndi zolinga zofanana ndi zanga
-
woti azidzakonda zosangalatsa zomwe inenso ndimakonda
Ngati mukufuna munthu woti mudzakwatirane naye, palibe cholakwika chilichonse kufuna munthu amene adzakhale ndi zina mwa zinthu zimene tazifotokoza patsamba lapitali. Mwinanso mukhoza kudzapeza munthu amene ali ndi zonse zimene tazifotokozazi. Koma mfundo yosatsutsika ndi yakuti m’kupita kwa nthawi anthu amasintha komanso zinthu zimatha kusintha.
Mfundo yaikulu: Kuti mudzakhale ndi banja losangalala, muyenera kuyembekezera kuti mudzakumana ndi zinthu zimene simumaganizira kuti zingachitike.
Nkhani yabwino. Zina mwa zinthu zimene simumaziyembekezera, zimatha kukhala zabwino.
“Titakwatirana ndi pomwe ndinayamba kukonda kwambiri nthabwala zimene mkazi wanga Maria * ali nazo kuposa nthawi imene tinali pa chibwenzi. Chifukwa sitidandaula ndi zambiri, tikakumana ndi mavuto timangoona kuti ndi zazing’ono.”—Anatero Mark.
Nkhani yosasangalatsa. Zina mwa zinthu zimene simumaziyembekezera m’banja zimakhala zosasangalatsa. Mwachitsanzo:
Mwina inuyo ndi chibwenzi chanu mumafuna mutadzatumikira monga amishonale kudziko lina. Koma kodi mungatani ngati mutakwatirana iye wapezeka kuti ali ndi matenda enaake omwe angakulepheretseni kuti mukatumikire monga amishonale? Zimenezi zikhozadi kuchitika chifukwa Baibulo limanena kuti: “Zinthu zosayembekezereka zimagwera” aliyense. (Mlaliki 9:11) N’zoona kuti mungakhumudwe kwambiri chifukwa cha matenda a mkazi kapena mwamuna wanuyo ndiponso chifukwa choti zimene mumafuna sizinachitike. Ngati mutakumana ndi zimenezi, ndi bwino kungovomereza kuti zachitika. Ndi bwino kukumbukira kuti chinthu chofunika kwambiri ndi mkazi kapena mwamuna wanuyo osati kukwaniritsa zolinga zanu.
Mfundo yaikulu: Baibulo limanena kuti anthu amene ali pa banja amakumana ndi “nsautso.” (1 Akorinto 7:28) Nthawi zina nsautso zimenezo zimakhala zinthu zimene simumaziyembekezera.
Ndiye kodi ndi mfundo ziti zimene muyenera kuziganizira panopa, zomwe zingadzakuthandizeni mukadzakumana ndi zinthu zimene simumaganizira kuti zingachitike? Mukadzalowa m’banja mudzafunika kuchita zinthu ziwiri zotsatirazi:
1. KUONA ZINTHU MOYENERERA
Ngakhale mutakhala kuti ndinu ogwirizana, muziyembekezera kuti
-
simuzidzagwirizana pa zinthu zina.
-
nthawi zina muzidzasiyana maganizo pa zinthu zimene mumaona kuti ndi zofunika.
-
nthawi zina simuzidzakonda zosangalatsa zofanana.
-
nthawi zina simuzidzakondana ngati mmene munkachitira poyamba.
Zimene tazitchula pamwambazi zimachitika m’mabanja ambiri. Zinthuzi pazokha sizingasokoneze banja lanu koma zikhoza kusokoneza ngati mutangozilekerera. Mungachite bwino kutsatira mfundo ya m’Baibulo yakuti chikondi “chimapirira zinthu zonse” komanso “sichitha.”—1 Akorinto 13:4, 7, 8.
Dziwani izi: Zimene mumachita mukakumana ndi mavuto zingachititse kuti banja lanu liziyenda bwino kapena lisokonekere.—Akolose 3:13.
2. KUKHALA WODZIPEREKA
Ngati nonse awiri muli ndi mtima wodzipereka sizidzakhala zovuta kuti muthane ndi mavuto alionse amene mungakumane nawo.—Mateyu 19:6.
Anthu ena amaona kuti kukhala wodzipereka m’banja n’kovuta kwambiri. Koma zimenezi sizoona. Kudzipereka n’kumene kumathandiza kuti muzidalirana. Mukakumana ndi mavuto, nonse awiri mumayesetsa kupeza njira zothetsera mavutowo m’malo mongothetsa banjalo.
Kuti mukhale odzipereka muyenera kuona kuti banja ndi chinthu chomwe chimakhudza moyo wanu wonse osati ngati zosangalatsa zomwe mungachite kwa nthawi yochepa. Kuti timvetse kusiyana pakati pa zinthu ziwirizi, tayesani kuchita zotsatirazi.
1. Tayerekezerani kuti mwapatsidwa tikiti ya ndege yoti mukhoza kupita kulikonse komwe mungafune. Kodi mungasankhe kupita kuti ndipo n’chifukwa chiyani?
Komwe mungasankhe kupita:
Chifukwa:
-
n’kokongola
-
chikhalidwe chake
-
nyengo yake
-
zosangalatsa
-
zifukwa zina
2. Tiyerekeze kuti akupatsaninso tikiti ya ndege koma kumalo kumene mutasankhe kupitako muzikakhala konko.
Kodi mungasankhe kupita kuti?
-
Komwe mungasankhe kupita:
-
kapena
kuli bwino ndingokhala konkuno.
N’zachidziwikire kuti malo amene munasankha poyamba ndi osiyana ndi achiwiri. Mwina munasankha malo ofanana koma munafunika kuganiza bwino poyankha funso lachiwiri. Poyankha funso lachiwiri munaganizira mfundo yoti muzikakhala komweko osati kuti mwangopita ku holide.
Ndi mmene muyenera kuonera nkhani ya banja. Muyenera kukumbukira kuti zinthu zimatha kusintha pakapita nthawi ndipo zidzakhudza mmene mumachitira zinthu. Kuti banja lanu lidzayende bwino, muyenera kukonzekera kudzakumana ndi zinthu zimene simumaziyembekezera komanso muyenera kudziwiratu zimene mungachite zimenezo zikadzachitika.
Taganizirani izi: Kodi panopa, pamene simunalowe m’banja, mumatani mukakumana ndi zinthu zimene simumaziyembekezera?
^ ndime 15 Tasintha mayina ena m’nkhani ino.
FUNSANI MAKOLO ANU
Afunseni makolo anu kuti kodi ndi mavuto komanso zosangalatsa zosayembekezereka ziti zimene anakumana nazo atangokwatirana kumene? Kodi ndingatani kuti ndizikonzekera kukumana ndi zosayembekezereka ndikadzalowa m’banja?