Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzisamalira Thanzi Lanu

Muzisamalira Thanzi Lanu

Kusamalira thanzi lanu kungathandize kuti muzikhoza ku sukulu komanso kuti muzikhala osangalala.

N’ZOYENERA kuti tizisamalira thupi lathu chifukwa ndi mphatso imene Mulungu anatipatsa. (Salimo 139:14) Mwachitsanzo, tayerekezerani kuti muli ndi galimoto koma simupeza nthawi yoti muziisamalira. Sipangapite nthawi yaitali isanawonongeke. N’chimodzimodzinso thupi lanu. Kodi ndi zinthu ziti zimene mungachite kuti muzilisamalira?

Muzigona mokwanira.

Ngati simugona mokwanira mukhoza kumasokonezeka maganizo, kukhala wofooka, komanso wotopa. Koma munthu amene amagona mokwanira amakhala ndi mphamvu, thupi lake limakula bwino, ubongo wake umagwira bwino ntchito, chitetezo cha m’thupi mwake chimakhala champhamvu komanso amakhala wosangalala. Choncho, kugona mokwanira kungakuthandizeni kuti mupeze zonsezi.

Mfundo yothandiza: Ngati n’zotheka muzigona nthawi imodzimodzi tsiku lililonse.

Muzidya zakudya zopatsa thanzi.

Achinyamata amakula mwamsanga. Mwachitsanzo, anyamata akafika zaka zapakati pa 10 ndi 17, thupi lawo limayamba kusintha. N’chimodzimodzinso atsikana. Munthu akamakula thupi lake limafunika chakudya chokwanira komanso chopatsa mphamvu. Choncho, muziyesetsa kudya zakudya zopatsa thanzi.

Mfundo yothandiza: Muzionetsetsa kuti mwadya chakudya cham’mawa. Kudya musanapite kusukulu kungathandize kuti muzikamvetsera bwino m’kalasi komanso kuti muzitha kukumbukira bwino zinthu.

Muzichita masewera olimbitsa thupi.

Baibulo limanena kuti: “Kuchita masewera olimbitsa thupi n’kopindulitsa.” (1 Timoteyo 4:8) Kuchita masewera olimbitsa thupi kungathandize kuti musanenepe kwambiri ndiponso kuti mukhale ndi thupi komanso mafupa amphamvu. Kungathandizenso kuti ubongo wanu uzigwira bwino ntchito, chitetezo cha m’thupi mwanu chikhale champhamvu komanso kuti musamakhale ndi nkhawa. Komanso kuchita masewera olimbitsa thupi n’kosangalatsa chifukwa umakhala ukuchita zinthu zimene zimakusangalatsa.

Mfundo yofunika kuikumbukira: Kugona mokwanira, kudya chakudya chopatsa thanzi komanso kuchita masewera olimbitsa thupi kungathandize kuti thupi lanu likhale lathanzi. Zimenezi zingachititse kuti muzikhoza m’kalasi. *

Yambani kutsatira malangizo amenewa. Khalani ndi ndandanda yabwino yochitira masewera olimbitsa thupi. Kwa mwezi umodzi, fufuzani kuti mudziwe nthawi imene mukumagona komanso zakudya zimene mukudya. Kenako onani zimene mungafunike kusintha.

“Ndimaona kuti ndikapita kokayenda ndimapeza mphamvu.”​—Anatero Jason, wa ku New Zealand.

“Ndimaona kuti Mulungu analenga chakudya kuti chizitipatsa mphamvu, choncho ndikufuna kuti ndizidya chakudya chopatsa thanzi.”​—Anatero Jill, wa ku United States.

“Ndimapita kothamanga katatu pa mlungu ndipo ndimakwera njinga kapena kupita koyenda kawiri pa mlungu. Kuchita masewera olimbitsa thupi kwandithandiza kuti ndizikhala ndi mphamvu komanso kuti ndisamakhale ndi nkhawa.”​—Anatero Grace, wa ku Australia.

^ ndime 9 Kuti mudziwe zambiri zokhudza mmene mungasamalilire thanzi lanu, werengani mutu 10 m’buku lachingelezi lakuti Questions Young People Ask​—Answers That Work, Volume 1, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.