Kodi Munaonapo Ng’ombe Ngati Iyi?
PALI mtundu winawake wa ng’ombe zokhala ndi nyanga zotambalala. Ng’ombezi zimakhala ndi ubweya wautali pamutu, womwe umachita kuphimba maso ake. Zilinso ndi ubweya wambiri womwe umangoti nyankhalala thupi lonse moti anthu amachita nazo chidwi kwambiri.
Ng’ombezi ndi zamphamvu kwambiri ndipo ndi mtundu umodzi wa ng’ombe zakale kwambiri zomwe zakhala zikupezeka kumadera am’mapiri ndi kuzilumba za ku Scotland. Kumadera amenewa ndi kozizira kwambiri. Poyamba ng’ombe zimene zinkapezeka m’madera am’mapiri zinkakhala zazikulu komanso za ubweya wofiira, pomwe zimene zinkapezeka m’zilumba zinkakhala zing’onozing’ono ndiponso za ubweya wakuda. Koma masiku ano anthu amangoona kuti ng’ombe zimenezi zili m’gulu limodzi ngakhale kuti zina zimakhala zofiira, zakuda, zachikasu ndipo zina zimakhala zoyera.
Ubweya wa ng’ombezi umathandiza kuti zizimva kutentha kunja kukamazizira komanso umathandiza kuti zisamanyowe kwambiri kunja kukamagwa mvula kapena chipale chofewa. M’nyengo yotentha, ubweyawu umateteza ng’ombezi kuti zisalumidwe ndi tizilombo toyambitsa matenda.
Kale alimi a m’madera amenewa ankatsekera ng’ombe zawo m’khola lamiyala kunja kukada. Ankachita zimenezi pofuna kuteteza kuti ziweto zawo zisagwidwe ndi nkhandwe.
Ubweya Wake
Ng’ombezi ndi zosiyana ndi ng’ombe zina chifukwa zili ndi ubweya wamkati ndi wakunja. Ubweya wakunja umakhala wautali kwambiri ndipo sulowa madzi kapena chipale chofewa. Ubweya wamkati umathandiza kuti ng’ombeyo izimva kutenthera.
Mlimi wina dzina lake Jim yemwe wakhala akuweta ng’ombezi kwa zaka zambiri, ananena kuti: “Ng’ombezi zimavuta kuzisambitsa chifukwa ubweya wake sulowa madzi.” Mosiyana ndi ng’ombe zina, ng’ombezi zimatha kukhala bwinobwino komanso kuswana m’madera am’mapiri komwe kumazizira ndiponso kugwa mvula yambiri.
M’nyengo yotentha, ubweya wa ng’ombezi umathothoka ndipo umadzameranso m’nyengo yozizira.
Ubwino wa Ng’ombe Zimenezi
Nthawi zambiri nkhosa zimawononga zomera chifukwa zimadya masamba ndi mizu yake. Koma ng’ombe, kuphatikizapo ng’ombe za ubweya wambirizi siziwononga zomera. M’malo mwake zimathandiza kuti udzu komanso mitengo ziphukire. Kuti zimenezi zitheke, ng’ombezi zimakokolola udzu wosafunika umenenso ng’ombe za mitundu ina sizingadye. Pochotsa udzu umenewu ng’ombezi zimagwiritsa ntchito nyanga, mlomo ndi mphuno. Zimenezi zimathandiza kuti udzu ndi mitengo ziphukire bwino.
Nthawi zambiri ng’ombe zomwe zili ndi ubweya wochepa, nyama yake imakhala ndi mafuta ambiri. Mafuta amenewa amathandiza kuti ng’ombeyo izimva kutenthera. Koma chifukwa choti ng’ombe za ku Scotland zimakhala ndi ubweya wambiri womwe umathandiza kuti zizimva kutenthera, nyama yake imakhala ndi mafuta ochepa. Komanso ngakhale kuti ng’ombezi sizidya zakudya zofuna ndalama zambiri, nyama yake ndi yabwino komanso yopatsa thanzi.
Zofunika Kusamala
Kuyambira kale anthu akhala akuweta ng’ombezi moti zinazolowera kukhala ndi anthu. Anthu akale a ku Scotland ankasunga ng’ombezi m’chipinda cha pansi pa nyumba zawo. Zimenezi zinkathandiza kuti m’chipinda chapamwamba pa nyumbayo muzitenthera.
Ngakhale kuti ng’ombe zimakhala zofatsa, nthawi zina ng’ombe za ku Scotland zimalusa. Mwachitsanzo ng’ombe imene ili ndi mwana, imakhala yolusa kwambiri chifukwa imafuna kuteteza mwanayo. Komanso nthawi zambiri zimalusa ngati munthu atadutsa pakati pa gulu la ng’ombezo.
Anthu ambiri padziko lonse amakonda kuweta ng’ombe zimenezi chifukwa amaona kuti ndi zapadera kwambiri. Ng’ombezi zimapezeka m’madera ozizira monga ku Alaska ndi Scandinavia. Zimapezekanso kumapiri a ku Andes, pamalo okwera mamita 3,000. Komanso ng’ombezi zimatha kukhala m’madera otentha.
Dziko la Scotland limadziwika kwambiri ndi zitoliro, nsalu ndi zovala zachikhalidwe cha dzikolo. Komanso limadziwika kwambiri chifukwa cha ng’ombe za ubweya wambiri zimenezi. Kodi kumene mumakhala kumapezeka ng’ombe za ubweya wambiri ngati zimenezi?