Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Anthu Masiku Ano Sakumaleza Mtima?

N’chifukwa Chiyani Anthu Masiku Ano Sakumaleza Mtima?

KUYAMBIRA kale anthu akhala akuchita zinthu mosaleza mtima. Mwachitsanzo anthu amapsa mtima chifukwa chodikira nthawi yaitali pamzere wamagalimoto kapena malo alionse ofunika kuima pamzere. Koma akatswiri akunena kuti masiku ano m’pomwe zafika poipa kwambiri ndipo mungadabwe ndi zomwe zimawachititsa zimenezi.

Akatswiri ena amanena kuti anthu sakumaleza mtima chifukwa cha zipangizo zamakono. Mwachitsanzo nyuzipepala ina ya mumzinda wa Montreal ku Canada, inanena kuti akatswiri ofufuza apeza kuti: “Zinthu ngati mafoni am’manja ndi makamera zapangitsa kuti moyo wa anthu usinthe kwambiri. . . . Chifukwa chakuti zipangizozi zimachita zimene munthu akufuna mofulumira, zachititsa kuti anthu ambiri aziyembekezera kuti chilichonse pa moyo wawo chizichitikanso mofulumira.”—The Gazette.

Dr. Jennifer Hartstein, ananena mfundo yochititsa chidwi kwambiri. Iye anati: “Chifukwa chozolowera kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono, timayembekezera kuti chilichonse chizichitika mwamsanga komanso mmene tikufunira. Ndiye zimenezi zikapanda kuchitika, timayamba kunyinyirika komanso kukwiya, zomwe zimasonyeza kusaleza mtima. Masiku ano anthu aiwaliratu zoti munthu akamachita zinthu modekha amasangalala.”

Masiku ano anthu sakumakondanso kulemberana maimelo ndipo ena akuganiza kuti posachedwapa zolemberana maimelo zitheratu. Zili choncho chifukwa anthu safuna zoti akalembera munthu wina imelo azidikirira kwa maminitsi kapena maola ambirimbiri asanayankhidwe. Komanso nthawi zambiri munthu akamalemba imelo amafunika kulemba mawu amalonje komanso omalizira. Choncho anthu ambiri akuona kuti zimenezi zimangotayitsa nthawi. N’chifukwa chake anthu akukonda kulemberana mameseji oyankha nthawi yomweyo chifukwa safunika mawu oyamba kapena omalizira. Zikuoneka kuti anthu alibe nthawi yolemba mawu amalonje komanso omalizira. Komanso akalemba, sawerenga kuti aone ngati zimene alembazo zikumveka. N’chifukwa chake makalata komanso maimelo ambiri amakhala ndi mawu ambiri olembedwa molakwika.

Anthu ambiri safuna kuwerenga buku kapena magazini akaona kuti nkhani yake ndi yaitali

Koma sikuti anthu saleza mtima pogwiritsa ntchito zipangizo zamakono pokha. Mwachitsanzo, kodi nthawi zina inuyo mumapezeka kuti mwawononga ndalama chifukwa chogula zinthu mopupuluma? Kapena kodi nthawi zina mumalankhula, kudya ndiponso kuyendetsa galimoto mothamanga kwambiri? Anthu ambiri safuna kudikira ngakhale kanthawi kochepa akakhala kuti akufunika kuima pamzere kuti apeze zimene akufuna.

Akatswiri ena ofufuza apeza kuti anthu ambiri safuna kuwerenga buku kapena magazini akaona kuti nkhani yake ndi yaitali. Amachita zimenezi chifukwa choti azolowera kuwerenga zinthu pa Intaneti mofulumira n’cholinga choti apeze mwamsanga mfundo imene akufuna.

Ndiyeno kodi n’chifukwa chiyani anthu masiku ano sakumaleza mtima? Zikuoneka kuti akatswiri sakudziwa zifukwa zonse zimene zimachititsa kuti anthu asamaleze mtima. Koma zikuoneka kuti munthu wosaleza mtima amakumana ndi mavuto ambiri. Nkhani zotsatirazi zifotokoza mavuto amene anthu osaleza mtima amakumana nawo komanso zimene mungachite kuti muzichita zinthu moleza mtima.

Anthu ambiri azolowera kuwerenga zinthu pa Intaneti mofulumira n’cholinga choti apeze mwamsanga mfundo imene akufuna