Zochitika Padzikoli
“Kuyambira mu 2004, chiwerengero cha mawu akuti ‘zolaula’ amene anthu amafufuza pa Google chawonjezereka kuwirikiza katatu.”—THE ECONOMIST, BRITAIN.
“[Ku Russia] mtsikana akakwatiwa, . . . amakhala pangozi yoti akhoza kumenyedwa ndi mwamuna wake kapena akhoza kumenyana.”—MOSKOVSKIYE NOVOSTI, RUSSIA.
“Ku United Kingdom dokotala mmodzi pa 7 alionse anaonapo dokotala mnzake akusintha mwachinyengo zotsatira za kafukufuku amene achita.”—BRITISH MEDICAL JOURNAL, BRITAIN.
“Chiwerengero cha anthu amene achira matenda a khansa ku United States chawonjezereka kuwirikiza kanayi kuyambira mu 1971 ndipo chafika pafupifupi 12 miliyoni . . . Zimenezi zatheka chifukwa chotulukira mwamsanga matendawa komanso chifukwa cha njira zamakono zochizira matendawa.”—UC BERKELEY WELLNESS LETTER, U.S.A.
Khirisimasi ya chaka cha 2011 itangotsala pang’ono kuchitika, ansembe ndi atsogoleri pafupifupi 100 azipembedzo zina, anamenyana patchalitchi china ku Bethlehem. Mkulu wa apolisi ananena kuti: “Sikuti zinali zachilendo . . . chifukwa zimachitika chaka chilichonse ndipo palibe amene anamangidwa chifukwa onsewa anali anthu a Mulungu.”—REUTERS NEWS SERVICE, U.S.A.
Ntchito Yaikulu Yodzala Mitengo ku Africa
Mu 2007, bungwe la African Union linayambitsa ntchito yodzala mitengo. Mayiko okwana 11 ndi amene akugwira ntchitoyi ndipo yayambira ku Senegal komwe ndi kumadzulo kwa Africa, mpaka ku Djibouti, kum’mawa kwa Africa. Cholinga cha ntchitoyi ndi kudzala mitengo m’dera lalikulu makilomita 7,600 m’litali ndi makilomita 15 m’lifupi. Pulofesa wa zachilengedwe pa yunivesite ya Cheikh Anta Diop mu mzinda wa Dakar, ku Senegal, dzina lake Aliou Guissé, anati: “Tikudzala mitengo imene anthu sangafune kuidula kuti akapangire matabwa.” Omwe akugwira ntchitoyi akukhulupirira kuti madera onse amene adzale mitengoyi akhalanso malo osungira zinthu zachilengedwe komanso athandiza kwambiri anthu a m’madera amenewo.
N’chifukwa Chiyani Anthufe Timayasamula?
Anthufe timayasamula tsiku lililonse, mwina kangapo patsiku. Koma asayansi amakanika kufotokoza chifukwa chake timayasamula. Chodabwitsa n’chakuti ngakhale mwana amene ali m’mimba mwa mayi ake amayasamula. Komanso nyama monga chisoni, nthiwatiwa, njoka komanso nsomba zimayasamula. Pali zifukwa zambiri zimene anthu amanena pa nkhani ya kuyasamula ngakhale kuti zimene amanenazo zimatsutsana. Asayansi ambiri amanena kuti kuyasamula ndi njira imodzi yowonjezera mpweya muubongo. Magazini ina inanena kuti: “Koma asayansi sanafike povomereza kuti mfundo imeneyi ndi yoona.” Kafukufuku amene wachitika posachedwapa pogwiritsa ntchito makoswe wasonyeza kuti “kuyasamula ndi njira imodzi yoziziritsira ubongo ukagwira ntchito kwambiri.” (Science News) Komabe palibe amene akudziwa zoona zenizeni.