Zochitika Padzikoli
Padziko Lonse
Ngakhale kuti alimi akumalima zakudya zambiri, njala siikutha padziko lonse. Zikuoneka kuti alimi akumakolola chakudya choti chikhoza kukwanira anthu 12 biliyoni. Chakudya chimenechi n’chokwanira chifukwa padziko lonse pali anthu pafupifupi 7 biliyoni. Koma njala siikutha chifukwa cha mavuto a zachuma komanso chifukwa choti chakudya china chikumangotayidwa. Vuto linanso ndi loti chakudyachi sichigawidwa mwachilungamo.
Britain ndi United States
Kafukufuku amene anachitika m’dziko la United States ndi Britain anasonyeza kuti anthu 24 pa 100 alionse ogwira ntchito yoona za ndalama “akhoza kuba kapena kuswa malamulo n’cholinga choti zinthu ziwayendere bwino.” Anthu 16 pa 100 alionse ananena kuti akhoza kuswa malamulo ngati “atadziwa kuti sagwidwa.”
Argentina
Ku Argentina, aphunzitsi atatu pa 5 alionse amapempha tchuthi chifukwa chopanikizika maganizo kapena chifukwa chothawa zachiwawa zomwe zimachitika kusukulu.
South Korea
Zikuoneka kuti m’zaka zikubwerazi ku South Korea kuzipezeka anthu ambiri okhala okha.
China
Boma la China likufuna kuti kuyambira m’chaka cha 2016, m’mizinda ya m’dzikolo mudzakhale mpweya wabwino. Koma zimenezi zikuoneka kuti m’mizinda yambiri sizidzatheka. Komanso m’dzikolo madzi a m’zitsime omwe anthu amamwa ndi oipa kwambiri.