MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | BANJA
Zimene Mwamuna ndi Mkazi Angachite Kuti Asamasiye Kulankhulana Akasemphana Maganizo
VUTO LIMENE LIMAKHALAPO
Kodi zimatheka bwanji kuti anthu amene analonjezana kuti adzakondana nthawi zonse asiye kulankhulana mwina kwa maola kapena kwa masiku angapo? Ena amaona kuti palibe vuto chifukwa sikuti akukangana. Koma nkhani ndiyakuti zimenezi sizimathetsa vuto limene lachititsa kuti asiye kulankhulanako. Komanso onse amakhala osasangalala.
ZIMENE ZIMACHITITSA
Kufuna kubwezera. Anthu ena apabanja amasiya kulankhulana ngati njira yofuna kubwezera. Mwachitsanzo, taganizirani izi: Mwamuna wakonza zoti apite kwinakwake ndi mkazi wake koma sanamuuze. Mkaziyo akukwiya ndi zimenezi ndipo akuuza mwamunayo kuti samuganizira. Mwamunayo akuuza mkaziyo kuti amangodandaula zilizonse. Mkaziyo akutuluka atalusa ndipo akusiya kulankhulana. Kuchita zimenezi kungasonyeze kuti mkaziyo akubwezera zimene mwamuna wakeyo wamuchitira.
Kufuna kuti akuchitireni zimene mukufuna. Anthu ena apabanja amasiya kulankhulana n’cholinga choti apeze zimene akufuna. Mwachitsanzo, taganizirani izi: Mkazi akufuna kuitana makolo ake kuti abwere kunyumba kwawo adzacheze. Mwamuna sakufuna. Kenako mkaziyo akusiya kulankhula ndi mwamuna wake n’cholinga choti mwamunayo alolere zimene mkaziyo akufuna.
N’zoona kuti nthawi zina kusiya kulankhulana kwa kanthawi kumathandiza kuti mtima ukhale m’malo ngati mwasemphana maganizo pa nkhani inayake. N’chifukwa chake Baibulo limati pali “nthawi yokhala chete.” (Mlaliki 3:7) Koma ngati anthu asiya kulankhulana pofuna kubwezera kapena kufuna kuti awachitire zimene akufuna, zimangochititsa kuti anthuwo azingokanganabe komanso kuti asamalemekezane. Ndiye mungatani kuti zimenezi zisakuchitikireni?
ZIMENE MUNGACHITE
Choyamba muyenera kudziwa kuti kusiya kulankhulana chifukwa chakuti mwasemphana maganizo sikuthetsa vuto lililonse. N’zoona kuti nthawi zina kusiya kulankhulana kungachititsedi mnzanuyo kukuchitirani zimene mukufuna kapena kuti mtima wanu uphwe. Koma kodi n’zimene mungafune kuchitira munthu amene munachita kulumbira kuti mudzamukonda? Pali njira zabwino zomwe mungatsatire mukasemphana maganizo m’malo mosiya kulankhulana.
Muzichita zinthu mozindikira. Baibulo limanena kuti chikondi “sichikwiya.” (1 Akorinto 13:4, 5) Choncho, musamafulumire kukwiya mwamuna kapena mkazi wanu akanena mawu monga akuti “Simumamvetsera ndikamalankhula” kapena “Nthawi zonse mumangokhalira kuchedwa.” M’malo mwake muziganizira chimene cham’pangitsa kuti anene mawu amenewo. Mwachitsanzo, ngati mkazi kapena mwamuna wanu atanena kuti “Simumamvetsera ndikamalankhula” angakhale akutanthauza kuti “Ndimaona kuti simumafuna kumva maganizo anga.”—Lemba lothandiza: Miyambo 14:29.
Muziona kuti mkazi kapena mwamuna wanu ndi mnzanu osati mdani wanu
Muzilankhula modekha. Mukamalankhula mokalipirana mkangano umangopitirira. Koma kulankhula modekha kungathandize kuti mkanganowo usapite patali. Buku lina, lakuti Fighting for Your Marriage, linanena kuti: “Kulankhula modekha komanso kuganizira zimene mnzanuyo akunena kungathandize kuti muthetse mkangano.”—Lemba lothandiza: Miyambo 26:20.
Muziganizirana. Baibulo limanena kuti: “Aliyense asamangodzifunira zopindulitsa iye yekha basi, koma zopindulitsanso wina.” (1 Akorinto 10:24) Muyenera kumuona mkazi kapena mwamuna wanu ngati mnzanu osati mdani wanu. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuti musamangokwiya ndi zilizonse, muzipewa kukangana komanso kuti musamasiye kulankhulana mukasemphana maganizo.—Lemba lothandiza: Mlaliki 7:9.
Kusiya kulankhulana mukasemphana maganizo sikugwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. Ilo limati: “Aliyense wa inu akonde mkazi wake ngati mmene amadzikondera yekha, komanso mkazi azilemekeza kwambiri mwamuna wake.” (Aefeso 5:33) Mungachite bwino kugwirizana ndi mkazi kapena mwamuna wanu kuti mukasemphana maganizo musamasiye kulankhulana zivute zitani.