Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 KUCHEZA NDI | IRÈNE HOF LAURENCEAU

Dokotala wa Mafupa Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake

Dokotala wa Mafupa Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake

Dokotala wina, dzina lake Irène Hof Laurenceau, amapanga maopaleshoni amafupa ku Switzerland. Poyamba ankakayikira zoti kuli Mulungu. Koma kenako anasintha maganizo ndipo anayamba kukhulupirira zoti kuli Mulungu komanso kuti analenga zinthu zonse. Mtolankhani wa Galamukani! anacheza naye kuti adziwe za chikhulupiriro chake komanso za ntchito yake.

Munayamba bwanji kuchita chidwi ndi zasayansi?

Ndili mwana ndinkakonda zinthu zachilengedwe. Ndinakulira kumudzi wokongola wotchedwa Richterswil, womwe uli m’mphepete mwa nyanja ya Zurich, ku Switzerland. Makolo komanso azibale anga ankakonda kunditenga koyenda ndipo ankandiuza zokhudza nyama komanso zomera zomwe tinkaziona.

N’chifukwa chiyani munaphunzira za mafupa?

Nthawi inayake, bambo anga ankagwira ntchito yothandizira m’chipinda chopangira opaleshoni pachipatala china cha m’dera lathu. Zimenezi zinawachititsa kuti azitiuza zinthu zokhudza maopaleshoni. Zimene ankatiuzazo zinkandisangalatsa kwambiri moti nditakula ndinasankha kuphunzira za opaleshoni ya mafupa. Ndinkafunitsitsa kudziwa mmene mafupa amagwirira ntchito. Munthu wopanga opaleshoni ya mafupa amafunika kudziwa mmene zinthu zosiyanasiyana zimapangidwira kuti athe kukonzanso mafupa, minyewa komanso minofu yolumikiza mafupa.

Ndimasangalala kwambiri ndikaona kuti anthu amene ndawathandiza akuchira. Komanso ndimakonda kugwira ntchito yothandiza anthu.

Munayamba bwanji kukayikira zoti kuli Mulungu?

Ndinayamba kukayikira zoti kuli Mulungu ndili wachinyamata ndipo panali zinthu ziwiri zomwe zinkandipangitsa kuti ndizikayikira. Choyamba, ndinkaona kuti akuluakulu ena a tchalitchi ankachita makhalidwe oipa ndipo zimenezi zinkandikhumudwitsa. Chachiwiri, aphunzitsi athu a Biology ankakhulupirira kuti zamoyo zonse zinachita kusintha kuchokera ku zamoyo zina. Choncho nanenso ndinayamba kukhulupirira zimenezi makamaka nditapita ku yunivesite.

N’chifukwa chiyani munkakhulupirira zimenezi?

Ndinkakhulupirira kuti zimene aphunzitsi anga amanena n’zoona. Komanso ndinkaona kuti mitundu  ina ya nyama imafanana ndipo zimenezi zinali ngati umboni wakuti mitundu ya nyama inachita kusintha kuchokera ku zamoyo zina. Zinandipangitsanso kukhulupirira maganizo oti kusintha kwa maselo kumapangitsa kuti kubadwe mitundu ina ya zamoyo.

Ndiye n’chiyani chinakupangitsani kusintha maganizo?

Mnzanga wina anandiuza kuti ndipite naye ku misonkhano ya Mboni za Yehova. Ndinachita chidwi kwambiri ndi mmene anandilandilira komanso nkhani zimene zinakambidwa kumeneko. Kenako mayi wina wa Mboni anabwera kunyumba kwanga ndipo ndinamufunsa kuti: “Kodi ndingadziwe bwanji kuti zimene Baibulo limanena ndi zoona?”

Mayiyo anandisonyeza maulosi a m’Baibulo omwe akukwaniritsidwa masiku ano. Mwachitsanzo, anandionetsa ulosi umene Yesu ananena wokhudza zimene zizidzachitika m’masiku otsiriza monga nkhondo padziko lonse, zivomezi zamphamvu, miliri komanso njala. * Anandionetsanso maulosi omwe ankasonyeza kuti m’masiku otsiriza anthu sazidzakondana, adzakhala adyera komanso oipa. * Kenako, ndinayamba kuphunzira Baibulo ndipo ndinaona kuti nthawi zonse zimene Baibulo limalosera zimachitikadi. Ndinayambanso kuganizira mofatsa zimene ndinkakhulupirira zoti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zamoyo zina.

Kodi ntchito yanu yakuthandizani kudziwa kumene kunachokera zamoyo zonse?

Eya yandithandiza. Pa nthawi imene ndinkaphunzira Baibulo, ndinkaphunziranso za opaleshoni ya pabondo. Kuyambira cha m’ma 1960, asayansi anayamba kumvetsa bwino mmene bondo limagwirira ntchito. Anatulukira kuti bondo silimapindikira mbali imodzi yokha ngati mmene amakhotera mahinjesi a chitseko. M’mwalomwake limazungulira mbali zonse ndipo zimenezi n’zimene zimathandiza kuti munthu azitha kuchita zinthu monga kuyenda komanso kuvina.

Kwa zaka zambiri asayansi ayesapo kupanga bondo lochita kuikirira. Koma n’zovuta kwambiri kupanga chinthu chokhala ngati bondo lenileni la munthu. Komanso nthawi zambiri zipangizo zomwe amapangira ziwalo zochita kuikirira, sizikhalitsa. Ngati zalimba zimafika zaka 20 basi. Koma bondo la munthu lili ndi maselo ndipo maselo akale akafa, maselo ena atsopano amalowa m’malo. Zimene ndinaphunzira zokhudza bondo la munthu zinandithandiza kudziwa kuti zamoyo sizinachite kusintha koma zinalengedwa ndi Mulungu yemwe ndi wanzeru.

Nanga zoti mitundu ina ya nyama imafanana mungazifotokoze bwanji?

Kufanana kwa mitundu ya nyama ndi umboni woti zonse zinalengedwa ndi Mulungu. Anthu amene amakhulupirira kuti zamoyo zinachokera ku zamoyo zina amanena kuti maselo akasintha n’kupangitsa kuti pakhale chamoyo china chatsopano, chamoyo chatsopanocho chimakhala chabwino kuposa choyambacho ndipo zimenezi zimangochitika mwangozi. Koma zoona zake n’zakuti, kusintha kwa maselo kumapangitsa kuti ena awonongeke. Chifukwa cha zimenezi, chamoyo chatsopanocho sichingakhale chabwino kwambiri kuposa choyambacho. N’zoona kuti nthawi zina zinthu zikasokonekera zimachititsa kuti zinthu zina ziyende bwino. Komabe kusintha kwa maselo sikungathandize kuti pakhale mitundu ina ya zamoyo yabwino kwambiri kuposa yoyambayo. Ndipo n’zosamveka kunena kuti bondo la munthu lomwe linapangidwa modabwitsa kwambiri linachita kusintha kuchokera ku bondo la chamoyo china. N’chimodzimodzinso ndi ziwalo zina za thupi lathu.

N’zosamveka kunena kuti bondo la munthu lomwe linapangidwa modabwitsa kwambiri linachita kusintha kuchokera ku bondo la chamoyo china

N’chifukwa chiyani munasankha kukhala wa Mboni za Yehova?

Nditayamba kugwiritsa ntchito zimene ndinkaphunzira, ndinasintha zinthu zambiri pa moyo wanga. Komanso mu 2003, ndinapita ku msonkhano wa mayiko wa Mboni za Yehova ndipo ndinaona kuti anthu ake ankakondana ngati a banja limodzi. Ankasonyezana chikondi ngakhale kuti anali atangokumana komweko. Choncho ndinkafuna kukhala m’banja lachikondi limeneli.