Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

United States

Tsiku lililonse anthu oposa 20, mwa anthu omwe ankagwira ntchito yausilikali ku United States, amadzipha. Ndipo mwezi uliwonse, anthu pafupifupi 950 mwa anthu amene anapuma pa ntchito yausilikali, omwe panopa amathandizidwa ndi dipatimenti ya boma la United States yosamalira anthu, amapulumutsidwa atatsala pang’ono kudzipha.

China

Nyuzipepala ya ku China, yotchedwa China Daily, inanena kuti: “Pafupifupi hafu ya atsikana omwe sanakwanitse zaka 30, omwe amasamukira kudera lina kuti akagwire ntchito, amakhala ndi mimba asanakwatiwe. Zimenezi zachititsa kuti chiwerengero cha azimayi osakwatiwa chikwere kwambiri.” Komanso zikuoneka kuti anthu ambiri a ku China “akumakhalira . . . limodzi ngati banja asanakwatirane.”

Greece

M’chaka cha 1974, dziko la Greece linayesetsa kuthana ndi matenda a malungo. Koma panopa matendawa ayambiranso ndipo anthu akuganiza kuti ayamba chifukwa cha mavuto azachuma komanso kusowa kwa ndalama zogulira zinthu zofunika m’zipatala.

India

Kafukufuku wina amene anachitika ku India, anasonyeza kuti anthu 74 pa 100 alionse ananena kuti angakonde kukwatirana ndi munthu woti achita kuwasankhira. Zimenezi zili choncho ngakhale kuti dzikolo likusintha pa nkhani ya chikhalidwe. Komanso anthu 89 pa 100 alionse ananena kuti angakonde kuti azikhala ndi achibale awo ambirimbiri kusiyana n’kuti azikhala ndi ana awo ndi makolo awo okha basi.

Italy

“Tchalitchi chathu [Chakatolika] chasauka ndipo zimenezi zili choncho ku Ulaya ndi ku America komwe. Chikhalidwe chathu chayamba kuoneka chachikale, anthu ambiri asiya usisitere, sakutsatira malamulo a tchalitchi ndipo miyambo imene timachita komanso zimene timavala zimakhala zongodzionetsera.  . . Tchalitchichi chatha mphamvu.”—Anatero Kadinala wa tchalitchi cha Katolika, dzina lake Carlo Maria Martini, asanamwalire. Zimene ananenazi zinatuluka m’nyuzipepala ya Corriere della Sera.