Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 KUCHEZA NDI | DAVEY LOOS

Wasayansi Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake

Wasayansi Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake

Davey Loos ndi wa ku Belgium ndipo ndi katswiri wasayansi ya mmene zinthu zinapangidwira. Pa nthawi ina sankakhulupirira kuti kuli Mlengi, m’malomwake ankakhulupirira kuti zinthu zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina. Koma kenako anasintha maganizo ake. Kodi n’chiyani chinachititsa katswiriyu kusintha zimene ankakhulupirira pa nkhani ya mmene moyo unayambira? Mtolankhani wa Galamukani! anacheza naye kuti adziwe za chikhulupiriro chake komanso za ntchito yake yasayansi.

Kodi munayamba bwanji ntchito imeneyi?

Nditapita ku yunivesite ndinasankha kuphunzira za mmene zinthu zinapangidwira. Ndinkachita chidwi kwambiri ndi mapulotini komanso zinthu zina zomwe zimapezeka mkati mwa maselo. M’kupita kwa nthawi, ndinayamba kuchita chidwi ndi zimene tinthu tina tomwe timapezeka m’maselo timachita tikakhala padzuwa.

Kodi munkakhulupirira Mulungu?

Ee, ndili mwana ndinkakhulupirira kuti kuli Mulungu. Koma nditayamba kuphunzira pa yunivesite ya Leuven, yomwe ndi ya Katolika, ndinaphunzira kuti zinthu zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina. Zimene aphunzitsi a pasukuluyi ankatiphunzitsa zinali zovuta kumva koma chifukwa ndinkaona kuti anali odziwa bwino ntchito yawo, ndinayamba kuzikhulupirira. Kenako, ndinasiya kukhulupirira kuti kuli Mulungu.

N’chiyani chinakupangitsani kuyambanso kuganizira mmene moyo unayambira?

Mu 1999 ndinakumana ndi mnzanga amene ndinaphunzira naye sukulu kalekale, yemwe pa nthawiyi anali wa Mboni. Anandiitanira ku misonkhano yawo ndipo ndinapita. Pa nthawiyi n’kutinso nditacheza ndi wa Mboni wina yemwe anandipatsa buku lakuti Is There a Creator Who Cares About You? *

Kodi bukulo linakuthandizani bwanji?

Ndinachita chidwi ndi mmene olemba bukuli anafufuzira nkhani zosiyanasiyana moti ndinayamba kukayikira zoti zinthu zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina.

N’chiyani chimakuchititsani chidwi m’chilengedwe?

Ntchito yanga inkaphatikizapo kufufuza kapangidwe ka tinthu tina topezeka m’maselo a zomera zina za pansi pa madzi, zomwe sizimadalira zamoyo zina kuti zipeze  zakudya. Akatswiri ena asayansi amanena kuti zomera zimenezi ndi zimene zinali zoyambirira kukhalapo m’dzikoli. Zomerazi zimagwiritsa ntchito kuwala kwa dzuwa posintha madzi ndi mpweya woipa kuti zikhale chakudya chake. Mpaka pano asayansi sadziwa bwinobwino mmene zimenezi zimachitikira. Koma china chimene chimandichititsanso chidwi kwambiri ndi mmene zomerazi zimapezera kuwala kwa dzuwa.

Poti masamba amagwiritsanso ntchito kuwala kwa dzuwa popanga chakudya, ndiye n’chifukwa chiyani zomerazi zinakuchititsani chidwi kwambiri?

Kuwala kwa dzuwa sikufika kwambiri pansi pa madzi akuya. Chifukwa chakuti zomera zimenezi zimapezeka pansi kwambiri zimalandiranso kuwala kwa dzuwa kochepa kwambiri. Komabe zimatha kugwiritsa ntchito kuwala kochepa komweko kupangira chakudya. Ndipo kuti zipeze kuwalako zimagwiritsa ntchito tizinthu tina tokhala ngati ulusi. Timaulusiti timatumiza mphamvu ya kuwalako ku mbali zosiyanasiyana zopangira chakudya. Akatswiri opanga magetsi ochokera ku dzuwa amachita chidwi kwambiri ndi mmene timaulusiti timagwirira ntchito ndipo ayesera kupanga makina ogwira ntchito ngati timaulusiti koma akanika.

Ndiye kudziwa zimenezo kunakuthandizani bwanji?

Ndinayamba kuganizira kuti akatswiri ambiri amapanga zinthu potengera mmene zinthu zina zamoyo zimagwirira ntchito ndipo zimenezi zinandithandiza kuona kuti zinthu zonse zamoyo zinalengedwa ndi Mulungu

Ndinayamba kuganizira kuti akatswiri ambiri amapanga zinthu potengera mmene zinthu zina zamoyo zimagwirira ntchito. Zimenezi zinandithandiza kuona kuti zinthu zonse zamoyo zinalengedwa ndi Mulungu. Si nkhani ya sayansi yokhayi ayi, koma kuphunzira Baibulo kunandithandizanso kwambiri.

N’chiyani chinakutsimikizirani kuti Baibulo ndi buku lochokera kwa Mulungu?

Chinthu chimodzi chimene chinandithandiza ndi kukwaniritsidwa kwa maulosi a m’Baibulo. Mwachitsanzo, kudakali zaka zambiri, Yesaya anafotokoza zimene zidzachitike pa imfa ya Yesu komanso mmene adzaikidwire m’manda. Timadziwa kuti zimenezi zinalembedwa Yesu asanafe chifukwa mpukutu wa Yesaya umene unapezeka ku Qumran, unalembedwa zaka mahandiredi ambiri Yesu asanabadwe.

Ulosiwo umanena kuti: “Manda ake adzakhala limodzi ndi a anthu oipa, ndipo adzakhala limodzi ndi anthu olemera pa imfa yake.” (Yesaya 53:9, 12) Ndipo zinachitikadi kuti Yesu anaphedwa pamodzi ndi zigawenga koma anaikidwa m’manda a anthu olemera. Chimenechi ndi chitsanzo cha maulosi a m’Baibulo amene anakwaniritsidwa omwe amanditsimikizira kuti Baibulo linalembedwadi ndi Mulungu. (2 Timoteyo 3:16) Patapita nthawi ndinakhala wa Mboni za Yehova.

N’chifukwa chiyani mumasangalala kukhala wa Mboni za Yehova?

Sitimangokhulupirira zinthu zopanda umboni ndipo zimene timakhulupirira zimagwirizana ndi sayansi

Sitimangokhulupirira zinthu zopanda umboni ndipo zimene timakhulupirira zimagwirizana ndi sayansi. Komanso mfundo zimene timatsatira pa moyo wathu zimachokera m’Baibulo. Monga wa Mboni za Yehova, ndimasangalala kuuzako ena uthenga wabwino wa m’Baibulo komanso kuwathandiza kupeza mayankho a mafunso amene amakhala nawo.

^ ndime 9 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.