Zochitika Padzikoli
Italy
Mu 2011, njinga zinkagulitsidwa kwambiri kuposa magalimoto ku Italy. Anthu ambiri akumagula njinga chifukwa cha mavuto azachuma, kukwera mtengo kwa mafuta komanso chifukwa chakuti kukonzetsa galimoto n’kodula. Koma njinga siimafuna ndalama zambiri pokonzetsa, siivuta kugwiritsa ntchito ndiponso ungapite nayo kulikonse.
Armenia
Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya lagamula kuti boma la Armenia linaphwanya ufulu wa anyamata 17 a Mboni za Yehova chifukwa chowamanga atakana kulowa ntchito zokhudzana ndi usilikali. Bomali likuyenera kuwalipira ndalama chifukwa chowawonongera mbiri komanso liyenera kulipira ndalama zonse zimene anyamatawo anawononga pa mlanduwu.
Japan
Pa ana 100 alionse amene anachitidwa chipongwe pogwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti, ana 63 anali asanachenjezedwepo ndi makolo awo kuti malowa ndi oopsa. Kuti apeze zimenezi anaunika milandu yokwana 599. Anthu 74 pa 100 alionse amene ankaimbidwa mlanduwu anavomereza kuti cholinga chawo pogwiritsa ntchito malowa chinali choti azigona ana.
China
Pofuna kuchepetsa kuchuluka kwa magalimoto m’misewu, maofesi a boma a m’mizinda ikuluikulu achepetsa nambala ya ziphaso zatsopano za magalimoto. Mwachitsanzo, ku Beijing azipereka ziphaso zatsopano zosapitirira 240,000 pa chaka. Mu August 2012, anthu pafupifupi 1,050,000 anachita maere kuti apatsidwe ziphaso ndipo anthu 19,926 ndi amene anapatsidwa ziphasozo. Zimenezi zikutanthauza kuti munthu mmodzi yekha pa anthu 53 ndi amene anapatsidwa chiphaso.