Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

  ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Yesu

Yesu

Kodi Yesu ndi Mulungu?

“Palibe munthu anaonapo Mulungu ndi kale lonse.”Yohane 1:18.

ZIMENE ANTHU AMBIRI AMANENA

Anthu ambiri amakhulupirira kuti Yesu si Mulungu. Komabe ena amatchula mavesi ena a m’Baibulo amene amaganiza kuti akusonyeza kuti Yesu ndi wofanana ndi Mulungu.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Baibulo silisonyeza kuti Yesu ndi Mulungu Wamphamvuyonse kapena kuti ndi wofanana ndi Mulungu. Koma limanena momveka bwino kuti Yesu ndi wamng’ono poyerekeza ndi Mulungu. Mwachitsanzo, pa nthawi ina Yesu ananena kuti: “Atate ndi wamkulu kuposa ine.” (Yohane 14:28) Baibulo limanenanso kuti: “Palibe munthu anaonapo Mulungu ndi kale lonse.” (Yohane 1:18) Choncho Yesu si Mulungu chifukwa anthu ambiri anamuonapo.

Otsatira a Yesu oyambirira sankanena kuti Yesu ndi Mulungu. Mwachitsanzo, Yohane ponena za zimene analemba anati: “Zalembedwa kuti mukhulupirire kuti Yesu alidi Khristu Mwana wa Mulungu.”Yohane 20:31. *

 Kodi Yesu anabadwa liti?

“M’dzikomo munalinso abusa amene anali kugonera kubusa akuyang’anira nkhosa zawo usiku wonse.”Luka 2:8.

ZIMENE ANTHU AMBIRI AMANENA

Anthu ambiri amasangalalira Khirisimasi pa 25 December ndipo amaganiza kuti tsikuli ndi limene Yesu anabadwa. Ena amakumbukira kubadwa kwa Yesu chakumayambiriro kwa January.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Baibulo silinena tsiku lenileni limene Yesu anabadwa. Komabe limanena kuti pa nthawi ya kubadwa kwa Yesu, panali “abusa amene anali kugonera kubusa akuyang’anira nkhosa zawo usiku wonse.” (Luka 2:8) N’zosatheka kuti abusawa ankagona kunja n’kumayang’anira nkhosa zawo usiku m’mwezi wa December kapena January. N’chifukwa chiyani tikutero?

Kudera limene Yesu anabadwira kumazizira kwambiri m’mwezi wa December ndi January. Ponena za nthawi imeneyi, Baibulo limanena kuti anthu ‘ankanjenjemera . . . chifukwa kunali kugwa mvula yamvumbi.’ (Ezara 10:9, 13; Yeremiya 36:22) Choncho imeneyi sinali nthawi yoti abusa angakhale ‘akugonera kubusa’ kuyang’anira nkhosa zawo.

Kodi Yesu anaukitsidwadi?

“Mulungu anamuukitsa [Yesu] kwa akufa.”—Machitidwe 3:15.

ZIMENE ANTHU AMBIRI AMANENA

Anthu ena amakhulupirira kuti n’zosatheka kuti munthu aliyense, kuphatikizapo Yesu, amene wafa akhalenso ndi moyo.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Yesu anauza otsatira ake kuti anayenera ‘kuzunzidwa kwambiri . . . ndiyeno n’kuphedwa, koma pa tsiku lachitatu n’kuukitsidwa.’ (Mateyu 16:21) Baibulo limanena kuti Yesu ataphedwa anaukitsidwa ndipo anaonekera kwa anthu oposa 500. (1 Akorinto 15:6) Anthu amenewa sankakayikira ngakhale pang’ono kuti Yesu anaukitsidwadi moti anali okonzeka kufa chifukwa cha chikhulupiriro chimenechi.—Machitidwe 7:51-60; 12:1, 2.

CHIFUKWA CHAKE KUDZIWA ZIMENEZI KULI KOFUNIKA

Baibulo limaphunzitsa kuti imfa ndiponso kuuka kwa Yesu zidzachititsa kuti anthu onse adzasangalale ndi moyo m’Paradaiso amene Baibulo limalonjeza. (Salimo 37:11, 29; Chivumbulutso 21:3, 4) Tili ndi chiyembekezo chodzasangalala ndi moyo wosatha m’Paradaiso chifukwa cha chikondi chimene Yesu ndi Atate wake, Yehova, yemwe ndi Mulungu Wamphamvuyonse, anasonyeza.—Yohane 3:16; Aroma 6:23.

^ ndime 7 Baibulo silinena kuti Mulungu ali ndi mkazi weniweni amene anabereka naye ana. Koma limati Yesu ndi “Mwana wa Mulungu” chifukwa choti Yesuyo analengedwa mwachindunji ndi Mulungu ndipo ali ndi makhalidwe ofanana ndi a Atate wake.