Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

United States

Zotsatira za kafukufuku wina zinasonyeza kuti anthu ambiri oyenda pansi amasokonezeka akamawoloka msewu wodutsa magalimoto ambiri chifukwa choti akumvetsera nyimbo, kuyankha foni kapena kuchita zinthu zina. Zotsatira za kafukufukuyu zinasonyezanso kuti chimene chimawasokoneza kwambiri ndi kulemba mameseji pafoni. Anthu amene amalemba mameseji amatenga nthawi yotalikirapo akuwoloka msewu, satsatira malamulo a pamsewu monga kudutsa pamalo oyenera, satsatira maloboti komanso sayang’ana mbali zonse asanawoloke.

Nigeria

Akazi amene oba anthu amawatenga kuchoka ku Nigeria kupita nawo ku Ulaya, akumakawalumbiritsa kwa asing’anga kuti azisunga chinsinsi. Kuti akaziwa azimvera komanso kuti azitha kuwagwiritsa ntchito za uhule, oba anthuwa amawaopseza kuti mizimu ikhoza kuwalanga akamapanda kumvera.

Spain

Anthu 5 kapena 10 pa 100 alionse amene akhala osalembedwa ntchito kwa nthawi yaitali, akamafunsira ntchito salemba zaka zimene anagwirapo ntchito komanso kuti ali ndi digirii. Iwo amaopa kuti zimenezi zingachititse kuti mabwana asawalembe ntchito powaona kuti ndi ophunzira kwambiri.

Dziko Lonse

Anthu ambiri amene amakhala m’mayiko osauka amafa chifukwa cha utsi wochokera m’mbaula kapena makala amene amagwiritsa ntchito pophika. Utsi umenewu umayambitsa matenda a m’mapapo ndipo umapha anthu 4 miliyoni chaka chilichonse. Akatswiri amanena kuti mbaulazi zimatulutsa utsi wapoizoni wofanana ndi umene umapezeka mundudu ya fodya.