Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Kum’mwera kwa Chipululu cha Sahara

Lipoti lina la bungwe la UNICEF lonena za mayiko a kum’mwera kwa chipululu cha Sahara linati, “ana 38 okha pa 100 alionse amene sanakwanitse zaka 5, ndi amene ali ndi khadi lakuchipatala losonyeza tsiku limene anabadwa.” Komabe mogwirizana ndi zimene wachiwiri kwa mkulu wa bungwe la UNICEF, dzina la Elke Wisch, ananena, m’madera ena a kuderali, “kuti ana alandire thandizo lachipatala, maphunziro komanso chuma cha makolo awo, pamafunika umboni wa kuchipatala wosonyeza kubadwa kwa anawo.”

Italy

Zotsatira za kafukufuku wina zinasonyeza kuti achinyamata ambiri a ku Italy amaopa kwambiri kuvutitsidwa komanso kuopsezedwa pa Intaneti. Achinyamata 72 pa 100 alionse a zaka zapakati pa 12 mpaka 17 ananena kuti amaopa kwambiri kuvutitsidwa komanso kuopsezedwa pa Intaneti kuposa chilichonse. Chiwerengero chimenechi ndi chokwera kwambiri kuposa cha achinyamata amene amaopa kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, kugwiriridwa komanso kutenga matenda opatsirana pogonana.

Japan

Nyuzipepala ya ku Japan inanena kuti achinyamata ambiri safuna kukwezedwa pa ntchito. Achinyamata 40 pa 100 alionse amanena kuti amachita zimenezi chifukwa amaona kuti anthu ambiri satsatira malamulo pa ntchito komanso amachita chinyengo. Achinyamatawa amaona kuti ndi zovuta kuti azinena maganizo awo kapena kukambirana momasuka ndi mabwana awo. Anthu akuluakulu amakhalabe pa ntchito, pamene achinyamata 60 pa 100 alionse amagwira ntchito yawo pongoyembekezera kuti apeze ina yabwino.

Brazil

Kuchokera mu 1980 kufika mu 2010, pafupifupi anthu 800,000 anaphedwa mochita kuwomberedwa ndi mfuti ku Brazil. Pa anthu amenewa, anthu oposa 450,000 anali a zaka za pakati pa 15 ndi 29. Kafukufuku waposachedwapa wasonyeza kuti ambiri mwa anthuwa, anaphedwa pa zifukwa ngati kukangana m’banja, kukangana ndi aneba, nsanje komanso kukangana kwa madalaivala.