Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

United States

Nyuzipepala ina inanena kuti: “Munthu amene amasuta fodya amawononga madola 5,816 a ku America pa chaka kusiyana ndi munthu amene sasuta.” (New York Times) Mogwirizana ndi zimene ofufuza a pa yunivesite ya Ohio anapeza, anthu osuta amawononga ndalamazi chifukwa amafunika kusiya kaye kugwira ntchito kuti akasute, amawononga ndalama zambiri kulipirira ku chipatala chifukwa amadwaladwala komanso chifukwa choti amajomba kuntchito. Chinthu chinanso n’choti anthuwa sagwira ntchito mokwanira chifukwa amakhala ndi mavuto osiyanasiyana amene amayamba chifukwa chosuta.

Italy

“Atsogoleri a tchalitchi komanso anthu otsatira kwambiri tchalitchi, amachita zinthu zosiyana kwambiri ndi zimene amaphunzitsa, ndipo zimenezi zikupangitsa kuti anthu asamakhulupirire tchalitchichi.”—Pope Francis.

Malaysia

Akuluakulu a boma la ku Malaysia anagwira magalimoto awiri omwe ananyamula minyanga ya njovu yolemera matani 24. M’magalimotowa munali minyanga yopitirira 1,000. Akuluakuluwa ananena kuti aka kanali koyamba kugwira magalimoto atanyamula minyanga ya njovu yochuluka chonchi. Katunduyu ankachokera ku Togo ndipo ankapita ku China.

Africa

Mogwirizana ndi lipoti limene Bungwe Loona za Umoyo Padziko Lonse linatulutsa mu 2012, anthu 63 pa 100 alionse amafa chifukwa cha matenda opatsirana monga Edzi, kutsekula m’mimba, malungo, TB komanso matenda amene amagwira ana.

Australia

Ana ambiri akumatchova juga pa mafoni a m’manja komanso zipangizo zina zamakono. Masewerawa akumakhala osavuta kuwina ndipo sakusiyana kwenikweni ndi amene amachitika pamalo otchovera juga. Akuluakulu a boma achenjeza kuti zimenezi “zikhoza kupangitsa ana kumaona kuti kutchova juga si koletsedwa, ndipo izi zingachititse kuti anawo akadzakula azidzangokhalira kutchova juga.”