Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 ANTHU NDI MAYIKO

Dziko la El Salvador

Dziko la El Salvador

ANTHU a ku Spain anafika m’dziko limene masiku ano limatchedwa El Salvador, pafupifupi zaka 500 zapitazo. Pa nthawiyo mtundu wa anthu amene anali ambiri m’dzikoli unkatchula dziko lawoli kuti Cuscatlán, kutanthauza, “Dziko la Zinthu Zamtengo Wapatali.” Masiku ano anthu amene amapezeka ku El Salvador ndi mbadwa za mitundu ya anthu a m’dzikoli komanso anthu amene anachokera ku Ulaya.

Anthu a ku El Salvador ndi olimbikira ntchito, ansangala komanso aulemu. Asanayambe kucheza kapena kukambirana ndi munthu amayamba apatsana kaye moni. Ukakhala m’mawa amanena kuti “Buenos días” (kutanthauza, mwadzuka bwanji) ndipo akakhala masana amati “Buenas tardes” (kutanthauza, mwaswera bwanji). Ndipotu anthu a m’madera akumidzi amaona kuti kungomudutsa munthu popanda kupereka moni, ndi mwano.

Dziko la El Salvador limadziwika bwino chifukwa cha ulimi wa khofi

Anthu a ku El Salvador amakonda chakudya chotchedwa pupusa. Chakudya chimenechi amachipanga pogwiritsa ntchito ufa wa chimanga kapena wa mpunga ndipo amaphatikiza ndi tchizi, nyemba, nyama ya nkhumba kapena zinthu zina. Nthawi zambiri pakudya chakudyachi amadyera limodzi ndi msuzi wa tomato kapena wopangidwa pophatikiza kabichi, kaloti, anyezi ndi viniga. Ngakhale kuti anthu ena amadya chakudyachi pogwiritsa ntchito mpeni ndi foloko, anthu ambiri amakonda kudya ndi manja.

Chakudya chimene anthu a ku El Salvador amakonda kudya chotchedwa Pupusa

Mathithi otchedwa Los Tercios ku Suchitoto

 KODI MUKUDZIWA? M’dziko la El Salvador mumaphulika mapiri. M’dzikoli muli mapiri 20 amene amakonda kuphulika, ndipo ena mwa mapiri amenewa ndi oti angathe kuphulika nthawi ina iliyonse. Mathithi a Los Tercios ndi aatali kwambiri ndipo anabwera chifukwa cha mapiri amene anaphulika.

M’dziko la El Salvador muli a Mboni za Yehova oposa 38,000 ndipo a Mboniwa ali m’mipingo pafupifupi 700. Iwo amaphunzitsa Baibulo anthu pafupifupi 43,000 ndipo amaphunzira nawo m’Chisipanishi, Chingelezi komanso chinenero chamanja cha ku El Salvador.