Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Imfa

Imfa

Kodi munthu akamwalira amapita kuti?

“Popeza ndiwe fumbi, kufumbiko udzabwerera.”Genesis 3:19.

ZIMENE ANTHU AMANENA

Anthu ena amaona kuti munthu akamwalira amapita kumwamba, kumoto, kupuligatoliyo kapena kumalo ena. Ena amaona kuti munthuyo amakabadwanso kwina monga munthu kapena chinachake. Ndipo anthu amene sakhulupirira zoti kuli Mulungu amaona kuti munthu akamwalira, ndiye kuti basi wathera pompo.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Lemba la Mlaliki 9:10 limanena kuti: “Kulibe kugwira ntchito, kuganiza zochita, kudziwa zinthu, kapena nzeru, ku Manda kumene ukupitako.” Baibulo limanenanso zimene zimachitika munthu kapena nyama ikafa. Limati: “Zonse zimapita kumalo amodzi. Zonse zinachokera kufumbi ndipo zonse zimabwerera kufumbi.”—Mlaliki 3:20.

 Kodi n’chiyani chimachitika munthu akamwalira?

“Mzimu wake umachoka, ndipo iye amabwerera kunthaka. Pa tsiku limenelo zonse zimene anali kuganiza zimatheratu.”Salimo 146:4.

ZIMENE ANTHU AMANENA

Anthu ambiri amaphunzitsidwa kuti zimene zidzawachitikire akadzamwalira zidzadalira zimene akuchita pa nthawi imene ali ndi moyo padziko lapansili. Amauzidwa kuti ngati akuchita zabwino, adzasangalala mpaka kalekale, koma ngati akuchita zoipa adzazunzidwa kumoto mpaka kalekalenso. Ena amakhulupiriranso kuti munthu akamwalira ayenera kuyeretsedwa kaye kuti athe kukaonekera pamaso pa Mulungu.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Anthu amene amwalira samasangalala kapena kuzunzika. Iwo sadziwa chilichonse, choncho sangathandize munthu kapena kumuchitira zoipa. Lemba la Mlaliki 9:5, 6 limanena kuti: “Amoyo amadziwa kuti adzafa, koma akufa sadziwa chilichonse. . . . Komanso chikondi chawo, chidani chawo ndiponso nsanje yawo zatha kale, ndipo alibenso gawo mpaka kalekale pa chilichonse chimene chikuchitika padziko lapansi pano.”

Kodi anthu amene anamwalira adzakhalanso ndi moyo?

“Munthu akafa, kodi angakhalenso ndi moyo? Ndidzadikira masiku onse a ntchito yanga yokakamiza, mpaka mpumulo wanga utafika.”Yobu 14:14.

ZIMENE ANTHU AMANENA

Anthu ambiri amakhulupirira kuti munthu akaweruzidwa kuti apite kumoto, sakhalanso ndi chiyembekezo chilichonse. Amanena kuti anthu amenewo azidzawotchedwa mpaka kalekale. Amakhulupiriranso kuti anthu amene amapita kupuligatoliyo, angapite kumwamba pokhapokha munthu wina atawapempherera kuti ayeretsedwe.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Anthu amene anamwalira Mwana wa Mulungu adzawaukitsa n’kukhalanso ndi moyo padziko lapansi. Baibulo limati: “Musadabwe nazo zimenezi, chifukwa idzafika nthawi pamene onse ali m’manda achikumbutso adzamva mawu ake ndipo adzatuluka.” (Yohane 5:26, 28, 29) Anthu oukitsidwawa akadzamvera Mulungu adzakhala ndi moyo wosatha. *

^ ndime 14 Kuti mudziwe zambiri zokhudza anthu amene adzaukitsidwe, onani mutu 7 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.