GALAMUKANI! July 2014 | Kodi Mungatani Mutakumana Ndi Vuto Lalikulu?
Kodi mungatani mutakumana ndi vuto linalake lalikulu?
Zochitika Padzikoli
Nkhani zake ndi monga: kudera limene chiwerengero cha akazi omwa mowa mwauchidakwa ndi chokwera kuposa cha amuna, malo amene anapezako zinthu zamoyo komanso dziko limene anthu amalandira ndalama akachepetsa thupi.
NKHANI YAPACHIKUTO
Kodi Mungatani Mutakumana Ndi Vuto Lalikulu?
Baibulo lingakuthandizeni kudziwa zomwe mungachite.
NKHANI YAPACHIKUTO
Katundu Wanu Yense Atawonongeka
Katundu yense wa Kei anawonongeka mu 2011 chifukwa cha tsunami amene anachitika ku Japan. Mabungwe ndi anzake anamuthandiza koma linamuthandiza kwambiri ndi vesi lina la m’Baibulo.
NKHANI YAPACHIKUTO
Atakupezani Ndi Matenda Aakulu
Mabel ankagwira ntchito yothandiza anthu kuchita mafizo. Koma atapangidwa opaleshoni chifukwa cha chotupa cha muubongo, ankafunika kuchita mafizo amene ankachititsa anthu ena odwala omwe ankawasamalira poyamba.
NKHANI YAPACHIKUTO
Munthu wa M’banja Lanu Akamwalira
Zaka 16 zapitazo, anthu 5 a m’banja la Ronaldo anamwalira pa ngozi ya galimoto. Ngakhale kuti imfayi imamupwetekabe, panopa ali ndi mtendere wa mumtima.
MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA
Kodi Mungasonyeze Bwanji Khalidwe Labwino Mukamatumiza ndi Kulandira Mameseji pa Foni?
Kodi mukuona kuti n’kupanda ulemu kusiya kaye kucheza ndi mnzanu kuti muwerenge meseji? Kapena mukuganiza si bwino kumangopitirizabe kucheza ndi mnzanuyo osawerenga kaye meseji imene mwalandira?
KUCHEZA NDI ANTHU
Katswiri Wasayansi Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake
Mfundo ziwiri zomwe zinathandiza Wenlong He kuti ayambe kukhulupirira zoti kuli Mlengi.
KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?
Achule Amene Amaswa Modabwitsa Kwambiri
N’chifukwa chiyani anthu ena amene amakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina, amanena kuti mfundo yakuti achulewa anachita kusintha mwa pang’onopang’ono ndi yosamveka?
Zina zimene zili pawebusaiti
Kodi Ndingafotokoze Bwanji Zimene Ndimakhulupirira pa Nkhani ya Kugonana?
Ngati mutafunsidwa kuti: ‘Kodi sunagonanepo ndi munthu chibadwire?’ kodi mungathe kugwiritsa ntchito Baibulo poyankha?
Kodi Ndingatani Ngati Anthu Ena Akukonda Kunena za Ine?
Kodi mungatani kuti zinthu zabodza zimene anthu akufalitsa zokhudza inuyo zisawononge mbiri yanu?
Kodi Ndingatani Kuti Ndisamachite Zinthu Mozengereza?
Werengani malangizo amene angakuthandizeni kuti musamachite zinthu mozengereza
Zimene Zinachitika Mose Ali Kamwana
Kodi anthu amene ali pachithunziwo ndi ndani? Werengani nkhani ya m’Baibulo yopezeka pa Ekisodo chaputala 2 kuti muwadziwe.