Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MUNGATANI MUTAKUMANA NDI VUTO LALIKULU?

Atakupezani Ndi Matenda Aakulu

Atakupezani Ndi Matenda Aakulu

Mabel, yemwe amakhala ku Argentina, anali mzimayi wolimbikira ntchito ndipo ankathandiza anthu kuchita mafizo. Koma mu 2007, mutu wake unayamba kumamupweteka kwambiri tsiku lililonse, komanso ankamva kutopa kwambiri. Iye anati: “Ndinapita kuzipatala zosiyanasiyana ndipo ndinamwa mankhwala ambirimbiri koma sizinathandize.” Kenako atapita kuchipatala china, anakamuunika m’mutu ndipo anamupeza kuti ali ndi chotupa mu ubongo. Mabel ananena kuti: “Adokotala atandiuza, sindinakhulupirire. Sindinkayembekezera kuti ndingapezeke ndi matenda oopsa chonchi.”

Iye ananenanso kuti: “Atandichita opaleshoni, m’pamene ndinazindikira kuti vutoli linali lalikulu kwambiri. Nditatsitsimuka, sindinkatha kutakataka moti ndinangogona chagada. Ndisanayambe kudwala, ndinali munthu wakhama pa ntchito komanso ndinkapanga zinthu pandekha. Koma matendawa anachititsa kuti zinthu zisinthe kwambiri pa moyo wanga moti sindinkathanso kuchita chilichonse. Nthawi yonse imene ndinakhala m’chipatala zinthu sizinkandiyendera. Ndinkangomva phokoso la zipangizo za m’chipatala, kulira kwa maambulansi komanso kubuula kwa anthu odwala. Kulikonse kumene ndinkayang’ana, ndinkangoona zinthu zomvetsa chisoni.”

Mabel anawonjezera kuti: “Panopa, ndingati ndikupezako bwino. Ndimatha kuyenda ndekha komanso nthawi zina ndimatha kukayendako panja. Komabe ndimavutika kuona, moti ndimaona zinthu ziwiriziwiri komanso nthawi zambiri ndimakhala wofooka.”

ZIMENE MUNGACHITE

Musamangoganizira kwambiri za mavuto anuwo. Lemba la Miyambo 17:22 limati: “Mtima wosangalala ndiwo mankhwala ochiritsa, koma mtima wosweka umaumitsa mafupa.” Mabel anati: “Nditayamba kuchira, ndinkafunika kuchita mafizo amene ndinkachititsa odwala omwe ndinkawasamalira poyamba paja. Ndikamachita mafizowa, ndinkamva kuwawa kwambiri, moti nthawi zina ndinkaganiza kuti ndi bwino ndingosiya. Komabe, ndinkayesetsa kuchotsa maganizo amenewa chifukwa ndinkadziwa kuti mafizowa angandithandize kuti ndipezeko bwino.”

Muziganizira kwambiri za zinthu zosangalatsa zomwe zidzachitike m’tsogolo. Mabel ananenanso kuti: “Baibulo linandithandiza kudziwa chifukwa chake anthufe timavutika. Ndinkadziwanso kuti tsiku lililonse likadutsa, ndiye kuti tikuyandikira nthawi imene mavuto onse adzathe.” *

Muzikumbukira kuti Mulungu amakuderani nkhawa. (1 Petulo 5:7) Mabel anafotokoza mmene kudziwa zimenezi kunamuthandizira. Iye anati: “Pamene ankanditenga kuti akandipange opaleshoni, ndinamvetsa bwino tanthauzo la lemba la Yesaya 41:10. Palemba limeneli Mulungu amati: ‘Usachite mantha, pakuti ndili nawe.’ Ndinkamvako bwino ndikaganizira kuti Yehova akuona zimene zikundichitikira ndipo akundidera nkhawa.”

Dziwani izi: Baibulo limaphunzitsa kuti posachedwapa anthu sazidzadwalanso.—Yesaya 33:24; 35:5, 6.