Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MUNGATANI MUTAKUMANA NDI VUTO LALIKULU?

Katundu Wanu Yense Atawonongeka

Katundu Wanu Yense Atawonongeka

Pa March 11, 2011, ku Japan kunachitika chivomezi champhamvu kwambiri. Chivomezichi chinapha anthu oposa 15,000 komanso chinawononga katundu wa ndalama zoposa madola 200 biliyoni a ku America. Bambo wina wazaka 32 dzina lake Kei, atamva kuti chivomezichi chichititsanso kuti kubwere tsunami, anathawira kumalo ena okwera. Kei anati: “Tsiku lotsatira ndinabwerera kunyumba kuti ndikatenge zina ndi zina. Koma nditafika, sindinapeze chilichonse pamalopo. Nyumba komanso katundu wanga yense anali atakokolokera m’nyanja.”

Kei ananenanso kuti: “Zinanditengera nthawi kuti ndivomereze zoti zinthu zanga zonse zapita. Zinthu monga galimoto, makompyuta, matebulo, mipando, zida zanga zoimbira nyimbo ndiponso zogwirira ntchito, zonse zinali zitapita ndi madzi. Palibe ngakhale chinthu chimodzi chimene chinatsala.”

ZIMENE MUNGACHITE

Muziganizira kwambiri zinthu zimene mwatsala nazo, osati zimene zawonongeka. Baibulo limati: “Ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera m’zinthu zimene ali nazo.” (Luka 12:15) Kei ananena kuti: “Poyamba ndinalemba zinthu zonse zimene ndinkafuna nditakhala nazo. Koma ndinaona kuti zimenezi zinkangochititsa kuti ndizikumbukira katundu wanga amene anawonongeka uja. Choncho ndinaganiza zolemba zinthu zofunika kwambiri zokha ndipo ndikapeza chinthu chimodzi, ndinkachichotsa pamene ndinalembapo. Zimenezi zinandithandiza kuti ndiyambirenso kukhala bwinobwino.”

M’malo momangodzimvera chisoni, yesetsani kumathandiza anthu ena. Kei anati: “Ndinalandira zinthu zosiyanasiyana kuchokera ku mabungwe komanso anzanga. Koma kenako ndinayamba kuona kuti kumangolandira zinthu kuchokera kwa anthu kukundichotsera ulemu. Zitatere ndinakumbukira mawu a m’Baibulo a palemba la Machitidwe  20:35 akuti: ‘Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.’ Popeza ndinalibe zinthu zoti ndingapatse anthu ena amene anakhudzidwa ndi tsokali, ndinkangowauza mawu olimbikitsa. Zimenezi zinandithandiza kwambiri.”

Muzipempha Mulungu kuti akuthandizeni pa mavuto anuwo. Kei ankakhulupirira zimene Baibulo limanena zoti Mulungu ‘amamvetsera pemphero la anthu amene alandidwa chilichonse.’ (Salimo 102:17) Inunso lemba limeneli lingakulimbikitseni.

Dziwani izi: Baibulo limanena kuti m’tsogolomu palibe munthu aliyense amene adzadandaule chifukwa choti zinthu zake zawonongeka ndi masoka achilengedwe. *Yesaya 65:21-23.

 

^ ndime 9 Kuti mudziwe za cholinga cha Mulungu chokhudza dziko lapansili, werengani mutu 3 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Bukuli likupezekanso pa webusaiti yathu ya www.pr418.com/ny.