KUCHEZA NDI | WENLONG HE
Katswiri Wasayansi Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake
WENLONG HE anaphunzira sayansi yokhudza zinthu zosiyanasiyana mumzinda wa Suzhou m’chigawo cha Jiangsu ku China. Iye analemba nkhani zambiri zasayansi zomwe zinatuluka m’mabuku osiyanasiyana. Panopa Wenlong He amathandiza kulemba nkhani zokhudza sayansi m’magazini inayake yotchuka kwambiri ndipo amagwira ntchito kuyunivesite inayake yotchedwa Strathclyde yomwe ili ku Scotland. Poyamba ankakhulupirira kuti zinthu zamoyo zinangokhalako zokha koma kenako anadziwa kuti zamoyo zinachita kulengedwa. Mtolankhani wa Galamukani! anamufunsa kuti adziwe zambiri za chikhulupiriro chake.
Tiuzeni za mbiri yanu.
Ndinabadwa m’chaka cha 1963 ndipo ndinakulira m’mudzi womwe uli kum’mwera kwa mtsinje wa Yangtze m’chigawo cha Jiangsu, ku China. Kuderali kumakhala chakudya cha mwanaalirenji chifukwa kuli mitsinje ndi madambo ambiri, moti anthu amangonena kuti ndi dera la mpunga ndi nsomba. Ndili mwana, ndinkadzifunsa kuti: ‘N’chifukwa chiyani padzikoli pamapezeka zakudya zambiri zokoma? Kodi zimenezi zinangochitika zokha? Kodi n’chiyani chinayambirira pakati pa nkhuku ndi dzira?’ Anthu ambiri a ku China sakhulupirira kuti kuli Mulungu. Choncho ndili kusukulu, ndinaphunzira kuti zinthu zinakhalako zokha.
Munakulira m’banja lotani?
Makolo anga sankakhulupirira kuti kuli Mulungu. Mayi anga anali mlimi, pomwe bambo anga anali ndi luso la zomangamanga moti anatsegula kampani ya zomangamanga. M’banja mwathu tinalipo ana 5 aamuna okhaokha ndipo ineyo ndi woyamba. Koma ang’ono anga awiri anamwalira adakali ana. Imfa yawo inandikhudza kwambiri moti ndinkadzifunsa kuti: ‘N’chifukwa chiyani anthu amamwalira? Kodi ang’ono anga amene anamwalira ndidzaonana nawonso?’
N’chifukwa chiyani munasankha kuphunzira za sayansi?
Ndinkafuna kudziwa zambiri zokhudza zinthu zachilengedwe monga kuwala. Kuyambira ndili mwana, ndinkachita chidwi kwambiri ndi mmene zinthu zimenezi zimakhudzira anthufe, ndipo ndinali ndi mafunso ambiri.
Kodi mumachita zotani pa ntchito yanu?
Ndimachita kafukufuku wopeza njira zimene zingapangitse kuti mphamvu za zinthu zosiyanasiyana, monga mphamvu za magetsi, zizithamanga ngati mmene kuwala kwa dzuwa kumathamangira. Ndimachita izi kuti ndidziwe mmene zinthu zosiyanasiyana zimapangidwira. Ndimafufuzanso mmene ndingapangire zinthu zowala kwambiri pogwiritsa ntchito mphamvu zochepa. Ngakhale kuti ndimachita zimenezi monga ntchito, cholinga changa china n’kufuna kumvetsa mmene zinthu zosiyanasiyana m’chilengedwechi zinayambira.
N’chiyani chinakupangitsani kuti muyambe kuchita chidwi ndi zimene Baibulo limanena?
Mu 1998, munthu wina wa Mboni za Yehova ndi mkazi wake anabwera kunyumba kwathu. Anthuwa anandiuza kuti angathe kundisonyeza kuchokera m’Baibulo mayankho a mafunso amene ndinali nawo. Mkazi wanga dzina lake Huabi, yemwenso ndi wasayansi, anavomera kukhalapo pamene tinkakambirana zimenezi. Tinali tisanaonepo Baibulo, koma tinachita chidwi ndi malangizo ake othandiza. Tinaonanso kuti a Mboniwo, zinthu zinkawayendera bwino chifukwa chotsatira mfundo za m’Baibulo. Anthuwa ankaoneka kuti akukhala moyo wosangalala ngakhale kuti analibe zinthu zambiri. Koma zimene zinandichititsa chidwi kwambiri ndi zomwe Baibulo limanena zokhudza Mulungu. Zinandipangitsa kuyamba kuganiza kuti mwinadi zinthu zinachita kulengedwa. Pa ntchito yanga, ndimayenera kumvetsa bwino zinthu za m’chilengedwe. Choncho, ndinaona kuti ndi bwino ndiganizirenso mofatsa zinthu zimene ndinkadziwa.
Pa ntchito yanga, ndimayenera kumvetsa bwino zinthu za m’chilengedwe. Choncho, ndinaona kuti ndi bwino ndiganizirenso mofatsa zimene ndinkadziwa
Ndiye ndi zinthu ziti zomwe munaziganizira?
Choyamba, ndinkadziwa kuti zinthu sizingakhale mwadongosolo popanda chinachake kuthandiza kuti zimenezo zitheke. Limeneli ndi lamulo lachiwiri lokhudza mphamvu yopezeka m’zinthu zachilengedwe. Popeza zinthu zamoyo komanso zina zonse zimene zili m’chilengedwechi zimachita zinthu mwadongosolo, ndinayamba kuganiza kuti payenera kuti pali winawake amene amachititsa zimenezi, ndipo ameneyo ayenera kukhala Mlengi. Mfundo ina imene ndinkadziwa ndi yoti mmene dziko lapansili lilili, zimasonyeza kuti linapangidwa mwanjira yoti pazikhala zinthu zamoyo.
Ndiye munapeza zotani zosonyeza kuti dziko lapansili linapangidwa mwanjira yoti pazikhala zamoyo?
Zamoyo zonse zimene zili padzikoli zimadalira mphamvu ya dzuwa kuti zikhale ndi moyo. Kuti mphamvu imeneyi ifike padziko lapansili, imadutsa mlengalenga ngati kuwala. Koma kuwala kumeneku kumakhala kosiyanasiyana ndipo kwina sikuoneka. Komanso kuwala kwina kumakhala koti kungabweretse mavuto pa zamoyo padzikoli. Koma chochititsa chidwi n’chakuti mlengalengamu muli mpweya umene umatchinga kuti kuwala koipaku kusafike padziko lapansi.
N’chifukwa chiyani mfundo imeneyi inakuchititsani chidwi?
Ndi yochititsa chidwi chifukwa ikugwirizana ndi zimene Baibulo limanena zokhudza mmene Mulungu analengera zinthu monga kuwala, zomwe zafotokozedwa m’buku la Genesis. Baibulo limati: “Mulungu anati: ‘Pakhale kuwala.’ Ndipo kuwala kunakhalapo.” * Pa kuwala konse kumene dzuwa limatulutsa, kuwala kochepa kwambiri kokha ndi kumene kumaoneka. Koma kuwala n’kofunika kwambiri kuti padzikoli pakhale zamoyo. Zomera zimagwiritsa ntchito kuwala kuti zipange chakudya, komanso anthufe timafunika kuwala kuti tizitha kuona zinthu. Sizikanangochitika mwangozi kuti kuwala kochokera kudzuwa kuzitha kudutsa mlengalenga. Komanso chochititsa chidwi kwambiri n’choti, pali kuwala kwa mtundu winawake komwe kumafika kochepa kwambiri padziko lapansili.
Kodi zimenezi zimathandiza bwanji?
Kuwala kwa mtundu umenewu kukachuluka kukhozanso kuyambitsa mavuto. Anthufe timafunikira kuwala kochepa kwa mtunduwu kuti tipeze vitamini D, amene amathandiza kuti tikhale ndi mafupa olimba komanso kuti khungu lathu litetezeke ku matenda monga khansa. Komatu kuwala kwa mtundu umenewu kukachuluka kungayambitse khansa ya pakhungu komanso vuto la maso. Koma mpweya umene uli mlengalenga umathandiza kuti kuwala kochepa chabe kuthe kudutsa n’kufika padzikoli. Kuwala kochepa choncho n’kumene kumafunika padzikoli. Kwa ineyo, umenewu ndi umboni woti pali winawake amene anakonza zimenezi.
Patapita nthawi, ine ndi mkazi wanga tinayamba kukhulupirira kuti kuli Mlengi ndiponso kuti Baibulo ndi buku lochokera kwa iye. Mu 2005, tinabatizidwa n’kukhala a Mboni za Yehova ndipo panopa timathandizanso ena kuphunzira Baibulo.