Zochitika Padzikoli
United States
Lipoti lina la bungwe loona za chakudya linasonyeza kuti mu 2012, anthu 49 miliyoni a ku United States pa nthawi ina “sankadziwa ngati angakwanitse kupeza chakudya chokwanira banja lonse, mwinanso sankachipeza n’komwe.”
Spain
Kafukufuku amene ophunzira a pa yunivesite ina anachita anasonyeza kuti akazi 56 pa 100 alionse komanso amuna 41 pa 100 alionse, anavomera kuti anapapirapo mowa mpaka kuledzera. Izi zikusonyeza kuti amuna anamwa mabotolo a mowa oposa 8 a mamililita 250 nthawi imodzi, ndipo akazi anamwa mabotolo a mowa oposa 6 a mamililita 250 nthawi imodzi.
Pacific Ocean
Akatswiri ena asayansi anatenga zinthu zina pamalo otchedwa Mariana Trench. Malowa ndi akuya mamita 11,000 ndipo ali m’nyanja ya Pacific. Atayeza zinthuzi, anapeza kuti munali mabakiteriya ndiponso tizinthu tina tamoyo tambirimbiri. Iwo sankayembekezera kuti m’malo amenewa mungapezeke zinthu zamoyo chifukwa ndi a mdima, opanikizika komanso ozizira kwambiri.
United Arab Emirates
Pofuna kuthana ndi vuto la kunenepa kwambiri, chaposachedwapa akuluakulu a mumzinda wa Dubai anayamba kupereka ndalama kwa munthu aliyense amene wachepetsa thupi. Akuluakuluwa ankapereka ndalama zokwana madola 45 a ku America pa kilogalamu iliyonse imene munthu wachotsa. Kuti munthu alandire ndalamazi, ankayenera kulembetsa kenako n’kuchepetsa thupi ndi makilogalamu awiri m’mwezi wa Ramadan.