Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Maloto Ochokera kwa Mulungu

Maloto Ochokera kwa Mulungu

Kodi Mulungu ankalankhula ndi anthu kudzera m’maloto?

[Mneneri wa Mulungu] Danieli analota maloto . . . atagona pabedi lake. Pa nthawi imeneyo, analemba zimene analotazo, ndipo anafotokoza nkhani yonseyo.”Danieli 7:1.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Mulungu wakhala akuuza anthu uthenga wofunika pogwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana. Kale iye ankauza anthu uthenga powalotetsa ngakhale kuti sankachita zimenezi kawirikawiri. Ndiponso malotowo ankakhala odziwika bwino tanthauzo lake. Mwachitsanzo, mneneri Danieli analota za zilombo zosiyanasiyana zimene zinkaimira maufumu amphamvu padziko lonse, kuyambira ufumu wa Babulo mpaka ufumu wamphamvu padziko lonse wa nthawi yathu ino. (Danieli 7:1-3, 17) Pa nthawi inanso, Mulungu analankhula ndi Yosefe wa ku Nazareti kudzera m’maloto, ndipo anamuuza kuti atenge Yesu ndi mayi ake n’kuthawira ku Iguputo. Zimenezi zinachititsa kuti Yesu asaphedwe ndi Herode yemwe anali mfumu yankhanza. Herode atamwalira, Mulungu anadziwitsanso nkhaniyi Yosefe kudzera m’maloto ndipo anamuuza kuti atenge banja lake n’kubwerera kwawo.—Mateyu 2:13-15, 19-23.

 Kodi Mulungu amalankhulabe ndi anthu kudzera m’maloto masiku ano?

“Musapitirire zinthu zolembedwa.”Akorinto 4:6.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Maloto amene analembedwa m’Baibulo ndi mbali ya Malemba opatulika amene Mulungu akufuna kuti anthu awadziwe. Lemba la 2 Timoteyo 3:16, 17 limati: “Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu ndi kulangiza m’chilungamo, kuti munthu wa Mulungu akhale woyenerera bwino ndi wokonzeka mokwanira kuchita ntchito iliyonse yabwino.”

Tingati Baibulo limatithandiza kukhala ‘okonzeka mokwanira’ chifukwa limatiuza za Mulungu, makhalidwe ake, komanso zimene amafuna. Limatithandizanso kudziwa cholinga chimene Mulungu anatilengera anthufe. Koma masiku ano Mulungu sagwiritsanso ntchito maloto akafuna kupereka uthenga kwa anthu. Sitikufunika kuchita ‘kupitirira zinthu zolembedwa,’ kapena kuti zomwe zili m’Baibulo kuti tidziwe zam’tsogolo komanso cholinga cha Mulungu chokhudza anthufe. Ndipo pafupifupi aliyense akhoza kupeza Baibulo n’kuphunzira zinthu zambiri zimene Mulungu waululira anthufe, kuphatikizapo maloto amene Mulungu analotetsa anthu akale.

N’chifukwa chiyani muyenera kukhulupirira nkhani zonena za maloto ndi masomphenya zomwe zinalembedwa m’Baibulo?

“Anthu analankhula mawu ochokera kwa Mulungu motsogoleredwa ndi mzimu woyera.”Petulo 1:21.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Nkhani zambiri zokhudza maloto komanso masomphenya zimene zinalembedwa m’Baibulo, zinali maulosi chifukwa zinkanena za zinthu zimene zidzachitike m’tsogolo. Munthu akamawerenga Baibulo amaona kuti ena mwa maulosi amenewa anakwaniritsidwa kale. Izi zimamuthandiza kudziwa kuti anthu amene analemba Baibulo analemba zolondola. Zimenezi zimachititsa kuti azikhulupirira Baibulo. Kodi pali umboni woti nkhani zokhudza maloto komanso masomphenya zomwe zili m’Baibulo ndi zolondoladi? Inde. Tiyeni tione zokhudza masomphenya opezeka pa Danieli 8:1-7 amene analembedwa ufumu wa Babulo utatsala pang’ono kutha.

M’masomphenya a ulosi amenewa, Danieli anaona mbuzi yamphongo ikupondaponda nkhosa yamphongo. Danieli sanadziwe payekha tanthauzo la malotowa. Mngelo wa Mulungu ndi amene anamuuza kuti: “Nkhosa yamphongo ya nyanga ziwiri . . . ikuimira mfumu ya Mediya ndi mfumu ya Perisiya. Mbuzi yamphongo yaubweya wambiri ikuimira mfumu ya Girisi.” (Danieli 8:20, 21) Mbiri imasonyeza kuti ufumu wa Mediya ndi Perisiya unakhala ufumu wamphamvu padziko lonse ndipo unalowa m’malo mwa ufumu wa Babulo. Kenako patatha zaka pafupifupi 200, ufumu wa Mediya ndi Perisiya unagonjetsedwa ndi Alekizanda Wamkulu, mfumu ya Girisi. Kukwaniritsidwa kwa ulosi umenewu ndi umboni woti nkhani zonse zimene zili m’Baibulo n’zolondola. Zimenezi zimasonyeza kuti Baibulo ndi losiyana ndi mabuku ena onse achipembedzo ndipo tiyenera kulikhulupirira.