Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO

Kodi Mungatani Kuti Mugwirizanenso Ngati Mwayambana?

Kodi Mungatani Kuti Mugwirizanenso Ngati Mwayambana?

Frank ndi Jerry ankakhala nyumba zoyandikana ndipo ankagwirizana kwambiri. * Koma zinthu zinasokonekera pamene Jerry anali ndi phwando kunyumba kwake. Iye ndi anzake anasangalala mpaka usiku ndipo Frank anadandaula chifukwa choti anthuwa ankasokosa kwambiri. Koma Jerry anakhumudwa Frank atamuuza zimenezi moti anayamba kukangana. Zitatere, ubwenzi wawo unasokonekera ndipo anasiya kulankhulana.

ZIMENE zinachitikira Frank ndi Jerry zimachitikiranso anthu ambiri. Anthu akasemphana maganizo, onse amakwiya ndipo amayamba kulozana zala. Akalephera kukambirana bwinobwino, ubwenzi wawo umasokonekera ndipo sachezanso ngati kale.

Mwina zoterezi zinakuchitikiraniponso inuyo. Ngati ndi choncho, muyenera kuti munakhumudwa ndi zimenezi. Ambirife timafuna kukhala mwamtendere ndi anzathu komanso anthu oyandikana nawo nyumba. Komabe nthawi zina tikhoza kuyambana ndi anthu amenewa. Ndiye kodi tingatani kuti zimenezi zisatilepheretse kukhala nawo mwamtendere? Kodi n’zotheka kunyalanyaza makhalidwe olakwika amene anthuwa angakhale nawo n’kuwakhululukira akatikhumudwitsa? Nanga kodi n’zotheka kukambirana ndi munthu amene watilakwira popanda kukangana?

Tiyeni tionenso nkhani ya Frank ndi Jerry ija. Ubwenzi wawo unasokonekera chifukwa cha zinthu zingapo zolakwika zimene onse anachita. (1) Jerry anachita zinthu zosamuganizira mnzakeyo, (2) Frank atapita kukauza Jerry za nkhaniyi, analankhula mawu amene anakwiyitsa mnzakeyo, (3) onse anapsa mtima, komanso (4) aliyense ankaona kuti mnzake ndi amene walakwa.

Komabe patapita nthawi, onse anayamba kuiganiziranso bwino nkhaniyi. Iwo anayesetsa kukambira bwinobwino ndipo anagwirizananso. Kodi chinawathandiza n’chiyani? Anagwiritsa ntchito mfundo zimenenso zathandiza anthu ambiri kuti akhale mabwenzi ngakhale kuti poyamba sankagwirizana ngakhale pang’ono.

Mfundozi zili m’Baibulo, buku lomwe limapezeka padziko lonse. Baibulo limatithandiza kukhala ndi makhalidwe amene amachititsa kuti tizikhala bwino ndi anzathu komanso kuti tizitha kuwakhululukira akatilakwira. Makhalidwe amenewa ndi monga kuzindikira, kumvetsa zinthu, kukoma mtima, chikondi komanso kudekha.—Miyambo 14:29; 1 Akorinto 13:4, 5.

 Monga taonera, mfundo za m’Baibulo zinathandiza Frank ndi Jerry kuti ayambirenso kugwirizana. Koma palinso anthu ambiri amene Baibulo linawathandiza. Mwachitsanzo mfundo za m’Baibulo zinathandiza Robert, yemwe amakhala ku Australia, kuthana ndi vuto lake losachedwa kupsa mtima. Zinathandizanso Nelson, wa ku Timor-Leste, kuti ayambe kugwirizana ndi munthu amene poyamba ankadana naye kwambiri. Mtolankhani wa Galamukani! anafunsa Robert ndi Nelson kuti adziwe mmene Baibulo linawathandizira.

KUCHEZA 1

Tiuzeniko za mbiri yanu a ROBERT.

Banja lathu linali losasangalala. Bambo anga anali ankhanza ndipo nthawi zambiri ankandimenya. Nthawi zina ankandimenya mpaka kunditulutsa magazi mwinanso kukomoka kumene. Zimenezi zinapangitsa kuti ndikhale wachiwawa komanso wosachedwa kupsa mtima. Ndili ndi zaka 16, ndinakhala zaka ziwiri m’ndende ya ana. Kenako ndinapalamula mlandu waukulu moti ndinatsekeredwa m’ndende ya anthu opalamula milandu ikuluikulu. Nditatuluka ndinasamukira ku Australia, ndipo ndinkaganiza kuti ndikapita kumeneko ndikasintha.

Robert anali munthu wolusa komanso wachiwawa ndipo anakhalapo m’ndende chifukwa cha khalidwe lakeli

Kodi kusamukaku kunakuthandizani kusintha khalidwe lanu?

Ee, kunandithandiza. Koma si kusamuka kokhaku kumene kunandithandiza. Chimene chinandithandiza kwambiri ndi kuphunzira Baibulo ndipo a Mboni za Yehova ndi amene ankandiphunzitsa. Sindinkapsanso mtima ngati poyamba. Komabe nthawi zina ndinkachita zinthu zina chifukwa chopsa mtima ndipo zikatere ndinkakhumudwa komanso ndinkadziona ngati wachabechabe. Tsiku lina ndinaganizira mozama lemba la Miyambo 19:11, lomwe limati: “Kuzindikira kumachititsa munthu kubweza mkwiyo wake, ndipo kunyalanyaza cholakwa kumam’chititsa kukhala wokongola.” Ndinkafunitsitsa kukhala ndi mtima wozindikira, choncho ndinayamba kuganizira zimene zinkandipangitsa kupsa mtima, kulankhula mawu achipongwe komanso kuchita zoipa. Kuchita zimenezi kunandithandiza kwambiri ndipo pang’ono ndi pang’ono ndinaphunzira kukhala womvetsa zinthu, wodekha komanso wokhululuka.

Mungatipatse chitsanzo?

Tsiku lina mosadziwa ndinachita zinthu zomwe zinakhumudwitsa mnzanga ndipo anandilankhula mawu onyoza tili pagulu. Kunena zoona ndinachita manyazi kwambiri. Komabe ndinakumbukira malangizo a m’Baibulo akuti “musabwezere choipa pa choipa,” ndipo nthawi yomweyo ndinamupepesa. (Aroma 12:17) Mtima wake utakhala m’malo, ndinamupempha kuti tikambirane pa awiri. Titakambirana ndinazindikira kuti anachita zimenezi chifukwa choti anali atayambana ndi mkazi wake. Tinathetsa nkhaniyo ndipo tinayambanso kugwirizana moti patapita nthawi anandipatsa malaya okongola. Zinali zodziwikiratu kuti akanandinyoza chonchi poyamba paja ndisanasinthe, nkhaniyi sikanatha mwamtendere.

Kodi mumatani mukakhala ndi mavuto a m’banja?

Tili ndi mwana, mnyamata wa zaka 20 ndipo popeza m’banja simulephera mavuto, ifenso nthawi zina timasemphana maganizo. Koma ndaphunzira zambiri kuchokera m’Baibulo. Mwachitsanzo ndaphunzira ubwino wopepesa ndikalakwitsa. Ndaona kuti kupepesa mochokera pansi pa mtima kumathandiza kuti anthu asiye kukangana kapenanso kuti asakangane n’komwe.

 KUCHEZA 2

A NELSON, ndinutu munthu wochezeka komanso wansangala. Koma ndinamva kuti pa nthawi ina munkadana kwambiri ndi anthu enaake. N’zoona?

Ee n’zoona. Ndili mnyamata ndinalowa m’gulu la chipani chotsutsa boma. Ndinkadananso kwambiri ndi chipani china chimene chinkafuna kuti chizilamulira dera lathu. Pofuna kuti anthu asamandigonjetse, ndinaphunzira karati ndipo ndinkamenya aliyense amene wandikwiyitsa.

Nelson ali mnyamata analowa m’gulu la chipani chotsutsa boma

N’chiyani chinakuthandizani kuti musinthe?

Ndinayamba kuphunzira Baibulo n’kumayesetsa kugwiritsa ntchito zimene ndinkaphunzirazo. Koma pali mavesi awiri amene anandikhudza mtima kwambiri. Loyamba limati: “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zomwezo.” (Mateyu 7:12) Lachiwiri limati: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.” (Mateyu 22:39) Ndinkaona kuti a Mboni amene ankandiphunzitsa Baibulo, ankatsatira zimene lembali likunena ndipo ankakonda anthu onse mosaganizira mtundu wawo kapena dziko limene anachokera. Ndinkafunitsitsa nditakhala ngati iwowo. Zimenezi zinathekadi moti anthu amene ankandidziwa anadabwa kuti ndasintha ndipo sankandiopanso.

Kodi nthawi zina munkalephera kutsatira zimene munkaphunzira m’Baibulo?

Ee, koma makamaka kunyumba osati pagulu. Ndikukumbukira kuti nthawi zina ndinkalephera kuugwira mtima. Tsiku lina ndinapsa mtima kwambiri ndipo ndinamenya mkazi wanga. Koma kenako ndinaona kuti sindinachite bwino. Komabe mkazi wangayu anandikhululukira ndipo zimenezi zinachititsa kuti ndiziyesetsabe kukhala munthu wodekha.

Mwanena kuti anthu anasiya kukuopani, mungatipatse chitsanzo cha zimenezi?

Tsiku lina ndinakumana ndi munthu wina yemwe anali wotchuka m’chipani chimene chinkafuna kuti chizilamulira dera lathu chija, dzina lake Augusto. Poyamba ankaoneka kuti akuchita nane mantha ndipo sanali womasuka. Koma ndinamupatsa moni mwansangala ndipo ndinamuuza kuti tiiwale zakale. Kenako ndinamupempha kuti adzabwere kwathu kuti tidzacheze. Anabweradi ndipo anadabwa kwambiri kuona mmene ndinasinthira moti nayenso anayamba kuphunzira Baibulo. Panopa ine ndi Augusto ndife mabwenzi apamtima komanso ndimamuona kuti ndi m’bale wanga wauzimu chifukwa tonse ndife a Mboni.

 “Khalani Mwamtendere ndi Anthu Onse”

Anthufe timayambana pa zifukwa zosiyanasiyana. Nthawi zina tingayesetse ndithu kuti tigwirizanenso ndi munthu amene tasemphana naye maganizo koma iyeyo angaoneke kuti sakufuna. N’chifukwa chake Baibulo limati: “Ngati ndi kotheka, khalani mwamtendere ndi anthu onse, monga mmene mungathere.”Aroma 12:18.

Zimene zinachitikira anthu amene atchulidwa m’nkhaniyi ndi umboni wosonyeza kuti m’Baibulo muli malangizo othandiza kwambiri. Baibulo lingathandize munthu kuti athetse maganizo olakwika amene wakhala nawo kwa nthawi yaitali. (2 Akorinto 10:4) Ponena za malangizo a m’Baibulo, lemba la Miyambo 3:17, 18 limati: “Njira zake n’zobweretsa chisangalalo ndipo misewu yake yonse ndi yamtendere. Munthu akagwiritsitsa nzeru, zidzakhala ngati mtengo wa moyo kwa iye, ndipo ozigwiritsitsa adzatchedwa odala.”

Nelson ndi Augusto panopa ndi mabwenzi apamtima

Kodi inuyo mukufuna kukhala munthu wodala kapena kuti wosangalala? Kodi mukufunanso kuti muzikhala mwamtendere ndi anthu ena? Nanga kodi mukufuna kuti ubwenzi wanu ndi munthu winawake amene mwayambana naye usathe? Kutsatira malangizo a m’Baibulo kungakuthandizeni kuti zonsezi zitheke.

^ ndime 3 Mayinawa tawasintha.