Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | KULERA ANA

Zimene Mungachite Ngati Mwana Wanu Amanama

Zimene Mungachite Ngati Mwana Wanu Amanama

VUTO LIMENE LIMAKHALAPO

Mwana wanu wazaka 5 akusewera kuchipinda china. Kenako mukumva phokoso la kusweka kwa chinthu. Mukuthamanga kuti mukaone ndipo mukupeza magalasi a choikamo maluwa ali mbwee, mwana wanuyo ataima poteropo. Nkhope ya mwanayo ikuchita kusonyezeratu kuti waswa chinthucho ndi iyeyo.

Kenako mukumufunsa mokalipa kuti: “Waswa ichi ndi iwe eti?”

Iye akuyankha kuti “ayi amayi, ndaswatu si ine.”

Mukukumbukira kuti aka si koyamba kuti mwanayo aname. Kodi mwana wotereyu mungamuthandize bwanji?

ZIMENE MUYENERA KUDZIWA

Bodza lililonse ndi loipa. Baibulo limanena kuti Yehova Mulungu amadana ndi “lilime lonama.” (Miyambo 6:16, 17) Chilamulo chomwe Mulungu anapatsa Aisiraeli chinkanena kuti munthu amene wanama azilandira chilango chokhwima.—Levitiko 19:11, 12.

Bodza limasiyanasiyana. Anthu ena amanama n’cholinga chofuna kupweteketsa anzawo kapena kuwaipitsira mbiri. Pomwe ena amanama chifukwa choti apanikizika, akuopa kuchita manyazi kapenanso akuopa kulandira chilango. (Genesis 18:12-15) Ngakhale kuti bodza lililonse ndi loipa, mabodza ena sakhala aakulu kwambiri. Mwana wanu akanama, muziganizira msinkhu wake komanso chimene chamupangitsa kuti aname.

Kuwongola mtengo n’kulinga uli waung’ono. Wolemba mabuku wina, dzina lake David Walsh, ananena kuti: “Mwana amafunika kum’phunzitsa kuti azinena zoona nthawi zonse. Ayenera kunena zoona ngakhale pomwe akudziwa kuti kuchita zimenezi kupangitsa kuti alandire chilango. Anthu amakhulupirira munthu amene amanena zoona. Koma munthu wabodza anthu samukhulupirira.” *

Musataye mtima. Mwana wanu akanama, sizitanthauza kuti akadzakula adzakhala munthu woipa. Kumbukirani kuti Baibulo limati: “Uchitsiru umakhazikika mumtima mwa mwana.” (Miyambo 22:15) Ana ena amaonetsa uchitsiru umenewu ponena bodza ndipo amachita izi n’cholinga choti asalandire chilango. Choncho muyenera kudziwa zoyenera kuchita zoterezi zikachitika.

ZIMENE MUNGACHITE

Ganizirani zimene zachititsa mwanayo kuti aname. Kodi akuopa kupatsidwa chilango kapena akuopa kukukhumudwitsani? Ngati mwana wanu amapeka bodza n’cholinga choti asangalatse anzake, kodi amachita zimenezi chifukwa choti ndi mwana ndipo sadziwa kusiyana kwa nkhani yoona ndi yongoyerekezera? Mukadziwa chifukwa chake akunama, zingakhale zosavuta kumuthandiza.—Lemba lothandiza: 1 Akorinto 13:11.

Nthawi zina muzipewa kumufunsa funso. M’chitsanzo chili kumayambiriro chija, mayi ankadziwa kuti mwanayo ndi amene waswa choikamo maluwa, koma anamufunsa mokalipa kuti: “Waswa ichi ndi iwe eti?” Mwanayo ananama kuti sanaswe, mwina chifukwa choona kuti mayi akewo alusa kwambiri. M’malo mofunsa funso lomuimba mlandu, mwina mwanayo sakananama ngati mayiyo akanangonena kuti: “Zimene wachitazi si zabwino!” Kunena mawu ngati amenewa kungathandize kuti mwanayo asapeze mpata wonama. Kungamuthandizenso kuti aphunzire kumanena zoona.—Lemba lothandiza: Akolose 3:9.

Akalankhula zoona muzimuyamikira. Mwachibadwa, ana amafuna kusangalatsa makolo awo. Choncho, muziwauza kuti mumasangalala akanena zoona. Muziwauzanso kuti mumafuna kuti mwana aliyense m’banjamo azilankhula zoona.—Lemba lothandiza: Aheberi 13:18.

Muzimuuza kuti munthu akanama, anthu amasiya kumukhulupirira ndipo zimatenga nthawi kuti ayambenso kumukhulupirira. Muzimuyamikira akanena zoona ndipo zimenezi zingapangitse kuti akule ndi khalidwe labwino. Mwachitsanzo, mungamuuze kuti, “Ndimasangalala kwambiri chifukwa umanena zoona.”

Muzipereka chitsanzo chabwino. Musaganize kuti mwana wanu anganene zoona ngati nthawi zambiri inuyo mumanena zinthu zabodza monga, “Uwauze kuti ndachokapo,” pamene mulipo. Kapena, “Sindipita kuntchito chifukwa ndikudwala,” pomwe mukungofuna kupuma.—Lemba lothandiza: Yakobo 3:17.

Muzigwiritsa ntchito Baibulo. M’Baibulo muli mfundo zabwino komanso nkhani zothandiza kuti munthu azinena zoona. Buku lakuti, Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova, lingakuthandizeni kuphunzitsa mwana wanu mfundo za m’Baibulo. Mutu 22 wa bukuli ndi woti, “Chifukwa Chake Tiyenera Kupewa Bodza.” (Onani bokosi lakuti, “ Buku Lomwe Lingathandize Mwana Wanu.”)

^ ndime 11 Mawu amenewa achokera m’buku lakuti, No: Why Kids—of All Ages—Need to Hear It and Ways Parents Can Say It.