Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Dziko Lapansi

Dziko Lapansi

Kodi Mulungu analengeranji dzikoli?

“Yehova, . . . amene anaumba dziko lapansi, . . . amene sanalilenge popanda cholinga, amene analiumba kuti anthu akhalemo.”—Yesaya 45:18.

ZIMENE ANTHU AMANENA

Anthu ena amanena kuti dzikoli silinachite kulengedwa. Komanso zipembedzo zina zimaphunzitsa kuti dziko lapansili ndi malo odikirira, amene Mulungu amayesera anthu kuti aone ngati ali oyenera kupita kumwamba kapena kukalangidwa kumoto.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Baibulo limati: “Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.” (Genesis 1:1) Mulungu anauza anthu oyambirira kuti: “Muberekane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, ndipo muliyang’anire. Muyang’anirenso . . . cholengedwa chilichonse chokwawa padziko lapansi.” (Genesis 1:28) Sichinali cholinga cha Mulungu kuti anthuwa adzafe. Anthu anayamba kufa chifukwa cha kusanamvera. (Genesis 2:17) Choncho, Mulungu analenga dziko lapansili kuti anthu azikhalamo mpaka kalekale. Iye ankafuna kuti anthu omvera adzaze padzikoli ndipo azilisamalira mpaka kalekale.

Kodi dziko lapansili lidzawonongedwa?

“Mwakhazikitsa dziko lapansi pamaziko olimba. Silidzagwedezeka mpaka kalekale, mpaka muyaya.”—Salimo 104:5.

ZIMENE ANTHU AMANENA

Asayansi amanena kuti pali zinthu zosiyanasiyana zomwe zingadzawononge dzikoli kapena zomwe zidzapangitse kuti padzikoli pasakhalenso anthu. Iwo amati mwina dziko lapansili lidzawombana ndi miyala ya mlengalenga kapena nyenyezi inayake. Amatinso mwina dzikoli lidzawonongeka chifukwa cha kutentha kwa padziko lonse, kuphulika kwa mapiri kapena dzuwa lidzasiya kuwalira padzikoli. Asayansiwa amanenanso kuti zinthu zina zomwe zingadzawononge dzikoli ndi monga nkhondo ya mabomba a nyukiliya kapena zigawenga zidzagwiritsa ntchito tizilombo todwalitsa.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Cholinga cha Mulungu chokhudza dziko lapansili sichinasinthe. Baibulo limati: “Dziko lapansi lidzakhalapobe mpaka kalekale.” (Mlaliki 1:4) Komanso limanena kuti anthu adzakhala padziko lapansili mpaka kalekale. Limati: “Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”—Salimo 37:29.

N’CHIFUKWA CHIYANI KUDZIWA ZIMENEZI N’KOFUNIKA?

Maganizo akuti dziko lapansili lidzawonongedwa achititsa kuti anthu aziwononga zinthu zachilengedwe. Apangitsanso anthu ena kukhala ndi moyo wosaganizira za mawa, chifukwa chosadziwa zinthu zabwino zomwe zidzachitike m’tsogolo. Koma munthu amene akudziwa kuti tidzakhala padzikoli mpaka kalekale, amachita zinthu zimene zingathandize iyeyo ndi banja lake, panopa komanso m’tsogolo.

Kodi kwathu si padzikoli koma kumwamba?

“Kunena za kumwamba, kumwamba ndi kwa Yehova. Koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.”—Salimo 115:16.

ZIMENE ANTHU AMANENA

Ambiri amakhulupirira kuti anthu onse abwino amapita kumwamba.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Kumwamba ndi kwa Mulungu, anthu kwawo ndi padziko lapansi. Baibulo limanena za “dziko lapansi lokhalamo anthu limene likubweralo.” (Aheberi 2:5) Yesu ndi amene anali munthu woyamba kupita kumwamba, ndipo Baibulo limasonyeza kuti kagulu kochepa ka anthu osankhidwa kadzapita kumwamba. Kodi anthuwa adzapita kumwamba kukatani? Baibulo limanena kuti iwo limodzi ndi Yesu “adzakhala mafumu olamulira dziko lapansi.”—Chivumbulutso 5:9, 10; Luka 12:32; Yohane 3:13.

N’CHIFUKWA CHIYANI KUDZIWA ZIMENEZI N’KOFUNIKA?

Chikhulupiriro choti anthu onse abwino adzapita kumwamba n’chosagwirizana ndi zimene Baibulo limanena. Mulungu atatenga anthu onse abwino n’kupita nawo kumwamba, zingasonyeze kuti walephera kukwaniritsa cholinga chake chokhudza dziko lapansi. Zingasonyezenso kuti zimene analonjeza zoti anthu adzakhala ndi moyo padziko lapansi kwamuyaya, sizidzachitika. Koma tikudziwa kuti Mulungu adzakwaniritsa cholinga chake chokhudza dziko lapansi komanso anthu. Baibulo limati: “Yembekezera Yehova, ndi kusunga njira zake, ndipo adzakukweza kuti ulandire dziko lapansi.”—Salimo 37:34.