Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | KULERA ANA

Kodi Mungayankhe Bwanji Mwana Wanu Atakufunsani za Imfa?

Kodi Mungayankhe Bwanji Mwana Wanu Atakufunsani za Imfa?

VUTO LIMENE LIMAKHALAPO

Mwana wanu wazaka 6 akukufunsani kuti: “Kodi tsiku lina inuyo mudzafa?” Mukudabwa kwambiri ndi funsoli ndipo mukuganiza kuti: ‘Kodi mwana ameneyu nditamuuza zokhudza imfa angazimvetse? Nanga ndingamuuze bwanji nkhani imeneyi?’

ZIMENE MUYENERA KUDZIWA

Ana amadziwa za imfa. Mwachitsanzo ana ena akamasewera, wina amayerekezera kuti wafa. Choncho musamaganize kuti nkhani ya imfa ndi youmitsa pakamwa. Ndipo ana anu akafunsa za nkhaniyi muyenera kuwafotokozera bwinobwino. Zimene mungamuuze mwana wanu, zingamuthandize kuti wachibale akadzamwalira asadzavutike kwambiri.

Kuuza mwana wanu zokhudza imfa, sikungamupangitse kuganiza zoti nkhaniyi ndi yosangalatsa. M’malomwake zingamuthandize kuti asamaope kwambiri imfa. Komanso ngati ali ndi maganizo olakwika pa nkhaniyi, muyenera kumuthandiza kudziwa zoona. Mwachitsanzo, akatswiri ena amati ana osakwana zaka 6 amaganiza kuti munthu akafa akhoza kudzukanso. Moti akamasewera mwana wina amayerekezera kuti wafa ndipo kenako amadzukanso.

Koma anawo akasinkhuka, amayamba kudziwa kuti imfa ndi yowawa. Izi zimapangitsa kuti azikhala ndi mafunso ambiri, nkhawa komanso kuti aziopa, makamaka wachibale akamwalira. Choncho ndi bwino kukambirana nawo. Katswiri wina wa za maganizo, dzina lake Marion Haza, anati: “Mwana amene makolo ake sakambirana naye zokhudza imfa, amayamba kukhala ndi mantha pa nkhaniyi.”

Koma mwina mungadzifunse kuti: ‘Ndiye ndiziti chiyani pomuuzapo?’ Kafukufuku wina anasonyeza kuti ana amangofuna “kuuzidwa zoona mokoma mtima.” Dziwani kuti ngati mwana wafunsa funso pa nkhani inayake, ndiye kuti ndi wokonzeka kumva yankho lake.

ZIMENE MUNGACHITE

Muzigwiritsa ntchito mpata umene wapezeka. Mwachitsanzo, chiweto chikafa kapena mwana wanu akaona mbalame yakufa, mufunseni mafunso omwe angathandize kuti muyambe kukambirana. Mwina mungafunse kuti: “Kodi nyama ikafa imavutika? Kodi imamva kuzizira komanso njala? Ungadziwe bwanji kuti nyama kapena munthu wafa?—Lemba lothandiza: Mlaliki 3:1, 7.

Muzimuuza zoona. Ngati wachibale kapena munthu wina wamwalira, pewani kuuza mwana zabodza monga kunena kuti munthuyo wachokapo. Zimenezi zingapangitse mwanayo kuganiza kuti munthuyo adzabweranso. M’malomwake muuzeni zoona koma musachulutse gaga m’diwa. Mwachitsanzo mungamuuze kuti: “Agogo ako atamwalira, thupi lawo linasiya kugwira ntchito. Sitingathe kulankhula nawo, komabe sitidzawaiwala.”—Lemba lothandiza: Aefeso 4:25.

Ana ena amaganiza kuti imfa ndi yopatsirana, choncho muuzeni kuti zimenezi si zoona ndipo sayenera kuopa kuti nayenso afa

Muzimulimbikitsa. Nthawi zina mwana amaganiza kuti zimene iyeyo wachita ndi zomwe zachititsa kuti munthuyo amwalire. M’malo mongomuuza kuti zimenezo si zoona, mufunseni kuti, “N’chifukwa chiyani ukuganiza kuti wachititsa ndi iweyo?” Akamayankha, muzimvetsera mwatcheru ndipo muzisonyeza kuti mukumvetsa zomwe akunenazo. Komanso ana ena amaganiza kuti imfa ndi yopatsirana, choncho muuzeni kuti zimenezi si zoona ndipo sayenera kuopa kuti nayenso afa.

Muthandizeni kuti azilankhula nanu momasuka. Muzikambirana naye momasuka zokhudza achibale anu amene anamwalira, kuphatikizapo omwe mwanayo sanawaone. Kambiranani zinthu zosangalatsa zomwe anthu monga amalume, azakhali komanso agogo ake ankachita asanamwalire. Kuchita zimenezi kungathandize mwana wanuyo kudziwa kuti si kulakwa kunena kapena kuganiza za anthuwo. Koma ngati mwanayo sakufuna kuti mukambirane zokhudza achibale amene anamwalira, si bwino kumukakamiza. Mungathe kudzakambirana pa nthawi ina pamene ali womasuka.—Lemba lothandiza: Miyambo 20:5.

Mungathenso kugwiritsa ntchito mutu 34 ndi 35 m’buku lakuti, Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso, pophunzitsa mwana wanu zimene Baibulo limanena pa nkhani ya imfa. . Pitani pamene palembedwa kuti MABUKU > MABUKU