Nzeru Zomwe Zimateteza
“Moyo wa munthu udzawomboledwa ndi chuma chake, koma munthu wosauka sadzudzulidwa.”
CHUMA ndi chothandiza koma nthawi zina chimabweretsa mavuto, makamaka masiku ano. (2 Timoteyo 3:1-5) M’mayiko ambiri, akuba amakonda kubera anthu amene amaoneka kuti ali ndi ndalama zambiri. Komanso zigawenga zimakonda kuba anthu oterewa n’cholinga choti apeze ndalama, abale awo akawawombola.
Lipoti la m’dziko lina losauka linati: “Zinthu monga uchigawenga, kuba mwachinyengo komanso kuba anthu, zikuchititsa kuti anthu olemera azikhala ndi chitetezo chokhwima. Mwachitsanzo, m’malo ambiri odyera muli alonda a mfuti komanso nyumba za anthu olemera zili ndi mipanda yawaya waminga, magetsi paliponse, makamera komanso alonda. Zoterezi zimachititsa kuti osauka asamathe kufika m’malo oterewa komanso kuti olemera ndi osauka asamachezerane.” Umu ndi mmene zililinso m’mayiko ambiri.
Koma lemba la Miyambo 13:8 limanena kuti “wosauka sadzudzulidwa.” Mawu amenewa akutanthauza kuti akuba salimbana ndi kubera munthu wosauka ngati mmene amachitira ndi wolemera. Kodi kudziwa mfundo imeneyi kungakuthandizeni bwanji? Ngati mumakhala kudera komwe kumachitika zaumbava kapena ngati mukupita kumalo oterewo, pewani kuvala kapena kunyamula zinthu zimene zingapangitse akuba kuganiza kuti muli ndi ndalama zambiri. Lemba la Miyambo 22:3 limati: “Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala, koma anthu osadziwa zinthu amangopitabe ndipo amalangidwa.”
Malangizo anzeru amene ali m’Baibulo amasonyeza kuti Mlengi wathu amatifunira zabwino ndipo amafuna kuti tikhale otetezeka. Baibulo limanena kuti “nzeru zimateteza” chifukwa “zimasunga moyo wa eni nzeruzo.”—Mlaliki 7:12.