ZIMENE BAIBULO LIMANENA
Chigololo
Ngakhale kuti anthu ambiri amaona kuti kukhulupirika m’banja n’kofunika, mabanja ambiri akutha chifukwa cha chigololo.
Kodi chigololo n’chiyani?
ZIMENE ANTHU AMANENA
M’mayiko ambiri anthu amaona kuti kugonana ndi munthu yemwe suli naye pabanja si kulakwa, makamaka ngati amene wachita zimenezo ndi mwamuna. Ndipo ena saona kuti anthu okwatirana ayenera kukhala limodzi mpaka imfa.
ZIMENE BAIBULO LIMANENA
Baibulo limanena kuti munthu amakhala kuti wachita chigololo akagonana ndi munthu yemwe si mwamuna kapena mkazi wake atachita kugwirizana. (Yobu 24:15; Miyambo 30:20) Mulungu amadana ndi anthu omwe amachita chigololo ndipo kale munthu akachita chigololo ankayenera kuphedwa. (Levitiko 18:20, 22, 29) Komanso Yesu anaphunzitsa kuti otsatira ake sayenera kuchita chigololo.—Mateyu 5:27, 28; Luka 18:18-20.
N’CHIFUKWA CHIYANI KUDZIWA ZIMENEZI N’KOFUNIKA?
Munthu akachita chigololo amakhala kuti waphwanya lonjezo lomwe anachita pomwe ankakwatira kapena kukwatiwa. Komanso chigololo “n’kuchimwira Mulungu.” (Genesis 39:7-9) Kuwonjezera apo, chigololo chingapangitse kuti banja lithe zomwe zingachititse kuti ana asamakhale ndi makolo awo onse awiri. Ndipotu Baibulo limati “Mulungu adzaweruza . . . achigololo.”—Aheberi 13:4.
“Ukwati ukhale wolemekezeka kwa onse, ndipo pogona pa anthu okwatirana pakhale posaipitsidwa.”—Aheberi 13:4.
Kodi ukwati uyenera kutha wina akachita chigololo?
ZIMENE BAIBULO LIMANENA
Baibulo limalola munthu kuthetsa ukwati ngati mnzakeyo wachita chigololo. (Mateyu 19:9) Zimenezi zikutanthauza kuti wina akachita chigololo, wosalakwayo ali ndi ufulu wosankha kukhalabe ndi mnzakeyo kapena kuthetsa banja. Koma munthu aliyense sayenera kukakamiza wosalakwayo kuti athetse banjalo kapena kuti akhalebe ndi mnzakeyo.—Agalatiya 6:5.
Mulungu amaona kuti anthu okwatirana ayenera kukhala limodzi moyo wawo wonse. (1 Akorinto 7:39) Iye sasangalala ngati munthu akuthetsa banja pa zifukwa zosamveka monga chifukwa choti mnzakeyo sakumusangalatsa. Choncho, munthu wosalakwayo ayenera kuganizira nkhaniyi asanasankhe zochita.—Malaki 2:16; Mateyu 19:3-6.
“Ine ndikukuuzani kuti aliyense wothetsa ukwati ndi mkazi wake, osati chifukwa cha dama, amamuchititsa chigololo akakwatiwanso, ndipo aliyense wokwatira mkazi wosiyidwayo nayenso wachita chigololo.”—Mateyu 5:32.
Kodi munthu amene wachita chigololo sangakhululukidwe?
ZIMENE BAIBULO LIMANENA
Baibulo limanena kuti Mulungu amachitira chifundo anthu amene alapa n’kusiya kuchita zoipa monga chigololo. Choncho Mulungu akhoza kukhululukira munthu yemwe wachita chigololo. (Machitidwe 3:19; Agalatiya 5:19-21) Baibulo limanenanso za anthu omwe poyamba ankachita chigololo, koma kenako anasiya n’kuyamba kutumikira Mulungu.—1 Akorinto 6:9-11.
Mulungu anachitiranso chifundo Davide, yemwe anali mfumu ya Isiraeli. Davide anachita chigololo ndi mkazi wa msilikali wake. (2 Samueli 11:2-4) Baibulo limati “zimene Davide anachitazi zinamuipira kwambiri Yehova.” (2 Samueli 11:27) Koma Davide atadzudzulidwa, analapa ndipo Mulungu anamukhululukira. Komabe anakumana ndi mavuto chifukwa cha tchimo lakelo. (2 Samueli 12:13, 14) Mpake kuti Solomo, yemwe anali mfumu yanzeru anati: “Aliyense wochita chigololo . . . alibe nzeru mumtima mwake.”—Miyambo 6:32.
ZIMENE MUNGACHITE
Ngati mwachita chigololo, muyenera kupempha Mulungu komanso mwamuna kapena mkazi wanu kuti akukhululukireni. (Salimo 51:1-5) Muyenera kumadana ndi chigololo ngati mmene Mulungu amachitira. (Salimo 97:10) Kuti zimenezi zitheke, muzipewa kuonera zolaula, kuganizira nkhani zogonana, kukopana komanso chilichonse chomwe chingachititse kuti muyambe kukhumbira munthu yemwe si mkazi kapena mwamuna wanu.—Mateyu 5:27, 28; Yakobo 1:14, 15.
Ngati mwamuna kapena mkazi wanu wachita chigololo, muyenera kudziwa kuti Mulungu akumvetsa mmene mukumvera. (Malaki 2:13, 14) Mupempheni kuti akulimbikitseni komanso kukutsogolerani kuti mudziwe zoyenera kuchita ndipo iye “adzakuchirikizani.” (Salimo 55:22) Ngati mwasankha kukhululukira mnzanuyo, nonse muyenera kuyesetsa kulimbitsanso ukwati wanu.—Aefeso 4:32.
Davide atazindikira kulakwa kwake n’kulapa, mneneri Natani anamuuza kuti: “Yehova wakukhululukira tchimo lako.”—2 Samueli 12:13.