Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Ntchito

Ntchito

Ngakhale kuti Baibulo linalembedwa kalekale, mfundo zake n’zothandiza nthawi zonse. Zimene limanena pa nkhani ya ntchito zingatithandize kwambiri masiku ano.

Kodi tiyenera kuiona bwanji ntchito?

ZIMENE ENA AMANENA:

Masiku ano anthu ambiri amanena kuti ntchito zikusowa ndiye ukaipeza maganizo ako onse azikhala pa ntchitoyo. Izi zachititsa kuti ena azidzipanikiza mpaka kufika ponyalanyaza banja lawo kapenanso kudwala kumene.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA:

Baibulo limatilimbikitsa kukhala anthu akhama osati aulesi. (Miyambo 6:6-11; 13:4) Koma pa nthawi imodzimodziyo sililimbikitsa anthu kudzipanikiza ndi ntchito. Limanena kuti ndi bwino kupeza kanthawi kopuma. Lemba la Mlaliki 4:6 limati: “Kupuma pang’ono kuli bwino kuposa kugwira ntchito mwakhama ndi kuthamangitsa mphepo.” Choncho si bwino kumangoti kakaka ku ntchito mpaka kuiwala banja lako kapena mpaka kufika podwala nayo. Kudzipanikiza chonchi kulibe phindu lililonse.

“Kwa munthu, palibe chabwino kuposa kuti adye, amwe, ndi kusangalatsa mtima wake chifukwa choti wagwira ntchito mwakhama.”Mlaliki 2:24.

Kodi tingasankhe bwanji ntchito?

ZIMENE ENA AMANENA:

Anthu ambiri amaganiza kuti ntchito imakhala yabwino ngati malipiro ake ndi abwino. Maganizo amenewa ndiponso mtima wofuna kupeza msanga ndalama zachititsa anthu ena kuyamba chinyengo kapena kugwira ntchito zosavomerezeka.

Anthu ena amangofuna kugwira ntchito zimene zimawasangalatsa. Amaona kuti ntchito zina ndi zobowa. Choncho amagwira ntchitozi monyinyirika. Akhozanso kukana ntchito zina chifukwa choona kuti anyozeka.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA:

Baibulo limanena kuti tisagwire ntchito iliyonse yachinyengo kapena imene ingapweteketse anthu ena. (Levitiko 19:11, 13; Aroma 13:10) Ntchito zabwino zimathandiza anthu ena ndipo munthu wozigwira amamva bwino mumtima.—1 Petulo 3:16.

Baibulo limaphunzitsanso kuti timagwira ntchito kuti tipeze zofunika osati kuti tizingosangalala. N’zoona kuti tikhoza kusangalala ndi ntchito yathu koma si bwino kuona kuti ndi yofunika kwambiri kuposa chilichonse.

“Bambo anga amakhala bize kwambiri. Iwo ali pa ntchito ndiponso ali ndi udindo mumpingo wa Mboni za Yehova. Koma amayesetsa kupeza mpata wochita zinthu zina. Amagwira ntchito zawo komanso amapeza mpata wocheza ndi ineyo, mchemwali wanga ndiponso amayi anga.”—Alannah.

Mwina tingade nkhawa chifukwa chakuti zinthu zikukwera mtengo koma Baibulo limatilimbikitsa kuti tisamade nkhawa kwambiri. Limati: “Pokhala ndi chakudya, zovala ndi pogona, tikhale okhutira ndi zinthu zimenezi.” (1 Timoteyo 6:8) Izi sizitanthauza kuti tiyenera kudzimana zinthu zina zonse. Koma ndi bwino kugula zinthu zimene tingakwanitse ndiponso zimene tingazisamalire bwinobwino.—Luka 12:15.

ZIMENE MUNGACHITE:

Muyenera kugwira ntchito mwakhama ndipo muziyesetsa kuikonda. Mwina ntchito imene mumagwira sikusangalatsani koma yesetsani kuigwira mwaluso kwambiri. Kugwira ntchito yanu mwakhama ndiponso mwaluso kudzakuthandizani kuti muzisangalala nayo.

Ngakhale kuti kugwira ntchito n’kofunika, tiyeneranso kupeza nthawi yopuma. Kupuma kumakhala kosangalatsa kwambiri ngati tagwira ntchito mwakhama. Komanso tikamapeza zinthu zofunika pa moyo sitimadzikayikira ndipo anthu amatilemekeza.—2 Atesalonika 3:12.

“Musamade nkhawa n’kumanena kuti, ‘Tidya chiyani?’ kapena, ‘Timwa chiyani?’ kapena, ‘Tivala chiyani?’ . . . Atate wanu wakumwamba akudziwa kuti inuyo mumafunikira zinthu zonsezi.”Mateyu 6:31, 32.