NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MUMATANI MUKAKUMANA NDI MAVUTO?
Vuto Limene Limakhalapo: Kukhala Wosasangalala
KODI nthawi zambiri mumakhala okhumudwa kapena okwiya? Ngati ndi choncho, mukhoza kulephera kuchita zinthu zofunika kwambiri. Ndiyeno kodi mungatani? *
CHITSANZO CHA M’BAIBULO: DAVIDE
Nthawi zina Mfumu Davide ankada nkhawa kapena kumva chisoni. Kodi n’chiyani chinkamuthandiza? Iye ankasiya mavuto ake m’manja mwa Mulungu. (1 Samueli 24:12, 15) Davide ankalembanso mmene ankamvera mumtima mwake. Iye anali ndi chikhulupiriro ndipo ankakonda kupemphera. *
ZIMENE GREGORY AMACHITA
M’nkhani yoyamba ija tanena kuti Gregory amavutika kwambiri ndi nkhawa. Iye anati: “Vuto langa loda nkhawa linafika poipa kwambiri.” Kodi n’chiyani chinamuthandiza pa vuto lake? Gregory anati: “Ndinalola kuthandizidwa ndi mkazi wanga komanso anzanga. Ndinapitanso kuchipatala ndipo anandithandiza kumvetsa bwino vuto langali. Ndiyeno nditasintha zochita pa moyo wanga, ndinayamba kupezako bwino. Nthawi zina ndimavutikabe koma ndimazindikira chimene chayambitsa ndipo ndimadziwa zimene zingandithandize.”
“Mtima wosangalala ndiwo mankhwala ochiritsa.”—Miyambo 17:22
ZIMENE MUNGACHITE
Ngati mumakhala osasangalala, yesani izi:
-
Muzilemba mmene mukumvera mumtima mwanu.
-
Muzifotokozera m’bale wanu kapena mnzanu zimene zikukuvutani.
-
Muzikhala pansi n’kuona ngati palidi chifukwa chokhalira osasangalala. Mwachitsanzo, ngati mukudziona kuti ndinu wolephera, mungadzifunse kuti: ‘Kodi pali umboni wakuti ndinedi wolephera?’
Mfundo Yofunika: Nthawi zambiri timakhumudwa kapena kuda nkhawa chifukwa cha mmene tikuonera vuto lathu osati chifukwa cha vuto lenilenilo.
^ ndime 3 Nthawi zina mavuto amene tatchulawa amabwera chifukwa cha matenda moti mungafunike kupita kuchipatala. Koma Galamukani! siuza anthu zochita pa nkhani zoterezi. Aliyense ayenera kusankha yekha zochita pambuyo poganizira bwino nkhanizi.
^ ndime 5 Masalimo ambiri a m’Baibulo anali mapemphero amene Davide analemba.
^ ndime 13 Kuti mudziwe zambiri, onani nkhani zoyambirira mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 2015 ya mutu wakuti “N’chiyani Chingatithandize Tikakhala ndi Nkhawa?”