NKHANI YA PACHIKUTO
Maselo Athu Ali Ngati Laibulale
MU 1953, James Watson ndi Francis Crick analemba zinthu zina zimene anatulukira m’maselo. Iwo anatulukira zinthu za mu DNA zokhala ngati ulusi ndipo nkhani imeneyi ndi yaikulu kwambiri kwa asayansi. * Mu zinthu zimenezi munalembedwa malangizo ambirimbiri moti maselo athu ali ngati laibulale. N’chifukwa chiyani m’maselo muli malangizowa? Nanga anachokera kuti?
N’CHIFUKWA CHIYANI M’MASELO MULI MALANGIZO?
Mwina munadzifunsapo kuti, Kodi njere imasintha bwanji n’kukhala
mtengo? Kapena kodi zimatheka bwanji kuti munthu abadwe n’kumafanana ndi makolo ake? Izi zimachitika chifukwa cha malangizo a mu DNA.Pafupifupi maselo onse ali ndi DNA yomwe imaoneka ngati makwerero opotoka. DNA ya m’maselo onse a munthu ikanakhala makwerero enieni ndiye kuti ikanakhala ndi zopondapo zokwana 3 biliyoni. Pali zinthu 4 zimene zimapanga makwererowa ndipo chopondapo chilichonse chimakhala ndi ziwiri. Mwachidule zinthu 4 zimenezi amangozitchula kuti A, C, G ndi T. * Mu 1957, Francis Crick ananena kuti zopondapozi zimasanjidwa m’njira yoti zizipereka malangizo. Ndiyeno mu m’ma 1960, asayansi anayamba kumvetsa malangizowa.
Zinthu ngati zithunzi, nyimbo kapena mawu zikhoza kusungidwa m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, munthu akhoza kusunga zinthu zimenezi pa kompyuta n’kumaziona kapena kumvera. Maselo amasunga zinthu pogwiritsa ntchito DNA. Maselo akamagawikana komanso zinthu zikamaswana kapena kuberekana, DNA ndiponso malangizo ake amapita m’maselo atsopano.
Kodi maselo amagwiritsa ntchito bwanji malangizo a mu DNA? Tingayerekezere zimene zimachitika ndi zimene munthu amachita pophika zinthu zosiyanasiyana. Iye amatsatira bwinobwino njira imene anaphunzitsidwa kuti zinthuzo zipse bwino. N’chimodzimodzi ndi DNA. Malangizo ake amatsatiridwa bwinobwino kuti kanthu kakang’ono kasinthe n’kukhala chinthu china monga nyama kapena chomera. Koma n’zodabwitsa kuti izi zimangochitika popanda winawake kuzigwiragwira.
Malangizo a muselo ya kachilombo kosaoneka ndi maso kotchedwa bakiteriya akhoza kudzaza buku la masamba 1,000
Kodi mu DNA mumakhala malangizo ochuluka bwanji? Wasayansi wina wa ku Germany, dzina lake Bernd-Olaf Küppers, anafotokoza kuchuluka kwa malangizo amene amapezeka muselo ya kachilombo kosaoneka ndi maso kotchedwa bakiteriya. Iye ananena kuti malangizowa atati alembedwe m’buku, ndiye kuti buku lake likhoza kukhala la masamba 1,000. M’pake kuti wasayansi wina dzina lake David Deamer analemba kuti moyo ndi wodabwitsa kwambiri chifukwa zinthu zambirimbiri zimasungidwa m’tinthu ting’onoting’ono. Nanga maselo onse a munthu amasunga malangizo ochuluka bwanji? Küppers ananenanso kuti malangizo ake akhoza kukwana m’mabuku akuluakulu masauzande ambiri.
Malangizowo amangosungidwa muselo mpaka pamene maselo atsopano akufunika kapena pamene mwana akupangika.“MALANGIZOWO ANALEMBEDWA MOMVEKA BWINO”
Küppers ananena kuti malangizo a mu DNA amalembedwa mofanana ndi mmene anthu amalembera mabuku. Ndiyeno zili ngati kuti mu DNA muli malamulo a chilankhulo amene amayenera kutsatiridwa.
Thupi likamakula limatsatira malangizowo ndipo izi zimathandiza kuti maselo ena akhale a mafupa, ena a minyewa, ena a khungu ndiponso ena a ziwalo zosiyanasiyana. Pa nkhani imeneyi, wasayansi wina dzina lake Richard Dawkins analemba kuti malangizo a mu DNA amasanjidwa ngati mmene timasanjira zilembo kuti anthu athe kuziwerenga bwinobwino. N’zosangalatsa kuti malangizowa analembedwa m’njira yoti anthufe tikhoza kuwamvetsa.
Popemphera kwa Yehova, Mfumu Davide ananena kuti: “Maso anu anandiona pamene ndinali mluza, ndipo ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’buku lanu.” (Salimo 139:16) N’zoona kuti Davide ananena zinthuzi mwandakatulo koma mfundo yake ndi yolondola. N’chimodzimodzi ndi mfundo zina zonse za m’Baibulo zimene anthu analemba motsogoleredwa ndi Yehova. Sanalembe motsatira maganizo a anthu kapena nthano zakalekale.—2 Samueli 23:1, 2; 2 Timoteyo 3:16.
KODI MALANGIZOWO ANACHOKERA KUTI?
Nthawi zambiri, zinthu zimene asayansi amatulukira zimatsegula mwayi woti enanso atulukire zina. Ndi mmene zinakhaliranso ndi nkhani ya DNA. Asayansi atatulukira zoti DNA imakhala ndi malangizo, anthu ena ankadzifunsa kuti, ‘Kodi malangizowo anachokera kuti?’ Kuyankha funsoli n’kovuta chifukwa chakuti palibe munthu aliyense amene anaona DNA yoyambirira ikupangidwa. Ndiyeno tisanayankhe funsoli tiyeni tione zinthu zina zimene anthu ena anapeza.
-
Mpaka pano anthu samvetsa tanthauzo la zilembozo koma amadziwa kuti pali winawake amene anazilemba.
-
Patangopita zaka zochepa kuchokera pamene Watson ndi Crick anatulukira za DNA, anthu ena anazindikira kuti pali mauthenga enaake ochokera m’mlengalenga. Ndiyeno asayansi ena awiri anaganiza zoti ayambe kufufuza amene anatumiza mauthengawo. Apa m’pamene anthu anayamba kufufuza ngati m’mlengalengamo muli enaake anzeru.
Apa mfundo ndi yakuti anthu amadziwa kuti ngati penapake palembedwa zinthu, ndiye kuti pali winawake amene anazilemba ngakhale kuti sanamuone akuzilemba. Amaonanso kuti ngati pali uthenga winawake, pali wina amene anautumiza. Koma chodabwitsa n’chakuti anthu akaona malangizo amene amapezeka mu DNA safuna kuvomereza mfundoyi ndipo amangoti zinachitika zokha. Kodi munthu wanzeru zake komanso wasayansi weniweni anganene kuti izi zinangochitikadi zokha? Asayansi ena odziwika bwino amati sizinachitike zokha. Ena mwa asayansiwo ndi Dr. Gene Hwang ndi Pulofesa Yan-Der Hsuuw. * Taonani zimene ananena:
Dr. Gene Hwang amagwira ntchito yochita kafukufuku wa zimene zimachititsa kuti ana azitengera makolo awo. Poyamba ankakhulupirira kuti zamoyo zinasintha kuchokera ku zinthu zina koma atafufuza anasintha maganizo. Iye anauza olemba Galamukani! kuti: “Ndatulukira zinthu zambiri zokhudza moyo ndipo ndazindikira kuti Mlengi ndi wanzeru zosaneneka.”
Pulofesa Yan-Der Hsuuw wa kuyunivesite ya ku Taiwan amachita kafukufuku wa ana amene sanabadwe. Iye ankakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina koma nayenso atafufuza anasintha maganizo. Iye ananena kuti: “Kuti ziwalo za thupi zipangike, maselo amagawikana n’kupanga maselo oyenera, pamalo oyenera ndiponso pa nthawi yoyenera. Malangizo a mu DNA ndi amene amachititsa zonsezi. Padzikoli palibe katswiri amene angalembe malangizo ngati amenewa. Ndikaganizira
zonsezi ndimaona kuti Mulungu ndi amene analenga zamoyo.”KUDZIWA KUMENE MALANGIZO A MU DNA ANACHOKERA N’KOFUNIKA
Kudziwa kumene malangizowa anachokera n’kofunika kwambiri. Tikutero chifukwa chakuti ngati Mulungu ndi amene analenga zamoyo ndiye kuti ndi wofunika kumulemekeza. (Chivumbulutso 4:11) Ngati tinalengedwadi ndi Mulungu, ndiye kuti pali chifukwa chimene anatilengera. Koma ngati tinangosintha kuchokera ku zinthu zina ndiye kuti moyo wathu ulibe tsogolo lililonse. *
Munthu aliyense amafuna kupeza mayankho a mafunso osiyanasiyana. Wasayansi wina dzina lake Viktor Frankl anati: “Munthu aliyense amakhala ndi mtima wofuna kudziwa zinthu ndipo mtima umenewu ndi umene umamulimbikitsa kuchita zambiri.” M’mawu ena tingati anthufe timafunika kudziwa za Mlengi wa zinthu zonse yemwe ndi Mulungu. Koma kodi Mulungu amene anatilengayo amatithandiza kupeza mayankho a mafunso athu?
Yesu anayankha funsoli ponena kuti: “Munthu sangakhale ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu onse otuluka pakamwa pa Yehova.” (Mateyu 4:4) Mawu a Mulungu ali m’Baibulo ndipo lathandiza anthu ambiri kupeza mayankho a mafunso awo komanso kudziwa zinthu zabwino zimene zidzachitike m’tsogolo. (1 Atesalonika 2:13) Inunso mukaphunzira Baibulo mukhoza kupeza mayankho a mafunso anu komanso kukhala ndi chiyembekezo.
^ ndime 3 Asayansi awiriwa anangopitiriza kufufuza zinthu zimene ena anatulukira zokhudza DNA.—Onani bokosi lakuti, “ Kodi DNA Inatulukiridwa Liti?”
^ ndime 6 Zilembo za A, C, G ndi T zimaimira adenine, cytosine, guanine ndi thymine.
^ ndime 18 Zinthu zina zimene asayansi ananena zili pa webusaiti yathu ya jw.org/ny. Pitani pamene palembedwa kuti MABUKU/LAIBULALE YA PA INTANETI n’kulemba mawu oti “kucheza ndi wasayansi” pamalo akuti Fufuzani.
^ ndime 22 Mayankho a mafunso okhudza chilengedwe akupezeka m’kabuku kachingelezi kakuti The Origin of Life—Five Questions Worth Asking ndiponso kakuti Was Life Created? Timabukuti timapezekanso pa webusaiti yathu ya www.pr418.com.