Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

ZOCHITIKA PADZIKOLI

Nkhani Zokhudza Mabanja

Nkhani Zokhudza Mabanja

Masiku ano mabanja akukumana ndi mavuto ambiri. Komatu m’Baibulo muli malangizo othandiza kuti mabanja aziyenda bwino.

Africa

Bungwe Loona za Umoyo Padziko Lonse limanena kuti amayi ayenera kuyamba kuyamwitsa ana awo pasanathe ola limodzi mwanayo atangobadwa. Limanenanso kuti ayenera kupitiriza kuyamwitsa mwanayo mwakathithi kwa miyezi 6. Ngakhale kuti bungweli limalimbikitsa zimenezi, nthambi ina ya bungwe la UNICEF yoona za chakudya chopatsa thanzi inanena kuti amalonda akuchititsa anthu kuganiza kuti “mkaka wochita kugula ndi wabwino kwambiri kuposa mkaka wa m’mawere.”

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Munthu amene sadziwa zinthu amakhulupirira mawu alionse, koma wochenjera amaganizira za mmene akuyendera.”—Miyambo 14:15.

Canada

Akatswiri ena a mumzinda wa Montreal atachita kafukufuku, anapeza kuti ana amene makolo awo amangowapanikiza ndi malamulo okhwima koma osawasonyeza chikondi, akhoza kudzakhala onenepa kwambiri. Ananena kuti pafupifupi ana 30 pa 100 alionse omwe ali ndi makolo oterewa adzakhala ndi vuto lonenepa kwambiri poyerekeza ndi ana omwe makolo awo amapeza nthawi yowalangiza komanso kuwasonyeza kuti amawakonda.

KODI MUKUDZIWA? Baibulo linapereka kalekale malangizo othandiza makolo kulera bwino ana awo.—Akolose 3:21.

Netherlands

Kafukufuku wina amene anachitika m’dzikoli, anasonyeza kuti mabanja amene makolo onse awiri amagwira ntchito, ndipo amagawa bwino nthawi yochita zinthu zakuntchito komanso zapakhomo, amacheza bwino ndi ana awo. Lipotilo linasonyeza kuti izi ndi zosiyana kwambiri ndi makolo omwe sagawa bwino nthawi yawo. Mwachitsanzo, linanena kuti makolo amene amalandira mafoni akuntchito pa nthawi imene ali kunyumba, amalephera kupeza nthawi yocheza ndi ana awo.

TAGANIZIRANI IZI: “Chilichonse chili ndi nthawi yake.”—Mlaliki 3:1.