KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?
Gulo Wakhungu Lodabwitsa Kwambiri
KU Australia kuli mtundu winawake wa agulo akhungu lodabwitsa kwambiri. Khungu lake ndi lamingaminga ndipo limayamwa madzi omwe amapezeka mumchenga wachinyezi kapena munkhungu. Madziwo akafika pa khunguli, amayenda mpaka kukafika kukamwa kwake. Kodi zimenezi zimatheka bwanji?
Taganizirani izi: Khungu la guloyu lili ndi mamba. Asayansi ena akuganiza kuti mame kapena madzi akafika m’mambawa, amayenda n’kugwera m’timipata tokhala ngati tingalande. Madziwa amayenda m’tingalandeti mpaka kukafika kukamwa kwa guloyu.
Guloyu amatha kumwa madzi pongogunda madziwo ndi miyendo kapena mchira wake. Komanso amatha kuyamwa madzi pongogunditsa mimba yake pa zinthu zachinyezi. Kodi chinsinsi chake chagona pati?
Akatswiri ena anafufuza zambiri za guloyu ndipo anatulukira chinsinsi chake. Chimene chimachitika n’choti, tingalande todutsa madzi tija timalumikizana ndi tina tating’ono kwambiri tokhala ngati mapaipi. Zimenezi zimapangitsa kuti madziwo azikwera kumtunda mpaka kukafika kukamwa kwa guloyu. Khungu la guloyu limayamwa madzi ngati mmene imachitira siponji.
Pulezidenti wa bungwe lina lofufuza njira zopangira zinthu zamakono potengera zinthu za m’chilengedwe, dzina lake Janine Benyus, ananena kuti potengera zimene khungu la guloyu limachita, akatswiri akhoza kupanga zipangizo zoyamwa madzi kuchokera mu nkhungu. Anati zipangizozi zikhoza kumaziziritsa m’nyumba komanso kumapanga madzi akumwa.
Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti khungu la guloyu lizitha kuyamwa madzi modabwitsa chonchi kapena pali winawake amene analilenga?