NKHANI YA PACHIKUTO | KODI N’ZOTHEKA KUKHALA NDI BANJA LOSANGALALA?
Kodi Mungatani Kuti Muzigwirizana Ndi Anthu a M’banja Lanu?
KODI mukuganiza kuti Baibulo lingatithandize kuti tizigwirizana ndi anthu a m’banja lathu? Tiyeni tione zimene anthu ena ananena komanso mfundo za m’Baibulo zimene zingakuthandizeni.
MFUNDO ZA M’BAIBULO ZOMWE ZINGAKUTHANDIZENI KUKHALA MWAMTENDERE M’BANJA
MUZICHITA ZINTHU MOGANIZIRANA.
“Musachite chilichonse ndi mtima wokonda mikangano kapena wodzikuza, koma modzichepetsa, ndi kuona ena kukhala okuposani. Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.”
—Afilipi 2:3, 4.
Mayi wina yemwe wakhala m’banja zaka 19 anati: “Ndimaona kuti banja limayenda bwino kwambiri ukamaona kuti mwamuna kapena mkazi wako ndiye wofunika kwambiri kuposa iweyo ndi anthu ena.”
MUZIMVETSERA MWATCHERU MNZANUYO AKAMAYANKHULA.
“Pitiriza kuwakumbutsa kuti . . . asakhale aukali. Koma akhale ololera, ndi ofatsa kwa anthu onse.”
—Tito 3:1, 2.
Mayi wina yemwe wakhala m’banja zaka 20 anati: “Sizivuta kuthetsa nkhani, anthu okwatirana akamayankhulana mwaulemu. Choncho mnzanu akamayankhula ndi bwino kumvetsera mwatcheru ngakhale zitakhala kuti simukugwirizana nazo.”
MUZIKHALA OLEZA MTIMA KOMANSO ODEKHA.
“Kuleza mtima kumanyengerera mtsogoleri wa asilikali, ndipo lilime lofatsa likhoza kuthyola fupa.”
—Miyambo 25:15.
Mayi wina yemwe wakhala m’banja zaka 27 anati: “Palibe banja limene silikumana ndi mavuto. Koma zimangodalira kuti awiriwo amatani akakumana ndi mavutowo. Choncho ngati nonse mutakhala oleza mtima, sizivuta kuthetsa nkhani.”
MUSAMANENE MAWU ACHIPONGWE KAPENA KUMENYA MNZANUYO NGAKHALE MUTAPSA MTIMA.
“Koma tsopano zonsezo muzitaye kutali ndi inu. Mutaye mkwiyo, kupsa mtima, kuipa, ndi mawu achipongwe, ndipo pakamwa panu pasatuluke nkhani zotukwana.”
—Akolose 3:8.
Mayi wina yemwe wakhala m’banja zaka 20 anati: “Mwamuna wanga amandisangalatsa kwambiri chifukwa ndi wougwira mtima. Ngakhale akhumudwe, sandikalipira kapena kunena mawu achipongwe.”
MUZIKHULULUKIRANA KOMANSO KUTHETSA NKHANI MWAMSANGA.
“Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira za mnzake. Monga Yehova anakukhululukirani ndi mtima wonse, inunso teroni.”
—Akolose 3:13.
Mayi wina yemwe wakhala m’banja zaka 34 anati: “Munthu akapsa mtima, zimakhala zosavuta kuyankhula kapena kuchita zinthu zomwe zingakhumudwitse mnzake. Choncho zinthu zimakhala bwino ngati mumakhululukirana. Ndimaona kuti banja silingayende bwino ngati anthu amakonda kusungirana zifukwa.”
MUZICHITIRANA ZABWINO.
“Khalani opatsa ndipo inunso anthu adzakupatsani. Adzakhuthulira m’matumba anu muyezo wabwino, wotsendereka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Pakuti muyezo umene mukuyezera ena, iwonso adzakuyezerani womwewo.”
—Luka 6:38.
Mayi wina yemwe wakhala m’banja zaka 44 anati: “Mwamuna wanga amadziwa zimene ndimakonda moti amakonda kundipatsa timphatso. Ndiye zikatere ndimaganizira zimene nanenso ndingachite kuti ndimusangalatse. Zimenezi zimathandiza kuti tizikhala osangalala.”
MUZICHITA ZINTHU ZOMWE ZINGATHANDIZE KUTI MUZIGWIRIZANA
Anthu amene atchulidwa pamwambawa ndi ena mwa anthu amene Baibulo lawathandiza kuti azikhala mwamtendere ndi anthu a m’banja lawo. * Anthuwa amayesetsa kuchita mbali yawo ngakhale kuti anthu ena a m’banja lawo ndi ovuta. Zimenezi zimawathandiza kuti azikhala osangalala chifukwa Baibulo limati: “Olimbikitsa mtendere amasangalala.”
^ ndime 24 Kuti mudziwe mfundo zina zomwe zingathandize kuti banja lanu lizikhala losangalala, werengani mutu 14 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Bukuli ndi lofalitsidwa ndi a Mboni za Yehova ndipo likupezeka pa webusaiti ya www.pr418.com/ny. Pa webusaitiyi palinso nkhani zina zothandiza mabanja. Pitani pamene palembedwa kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > MALANGIZO OTHANDIZA BANJA LONSE.