Kodi Mumadziwa Zotani Zokhudza a Mboni za Yehova?
Nthawi zambiri mumationa tikulalikira. Mwinanso mumawerenga kapena kumva kwa anthu ena zokhudza ife. Koma kodi inuyo mumadziwa zotani zokhudza a Mboni za Yehova?
KODI MUNGAYANKHE BWANJI?
Taonani ziganizo zili m’munsizi ndipo muchonge zoona kapena zabodza.
ZOONA ZABODZA
-
A Mboni za Yehova ndi Akhristu.
-
A Mboni za Yehova amakhulupirira kuti dzikoli linalengedwa m’masiku 6 enieni, a maola 24.
-
A Mboni za Yehova amakana kulandira chithandizo cha kuchipatala.
-
A Mboni za Yehova amaona kuti Baibulo lonse ndi lofunika.
-
A Mboni za Yehova amagwiritsa ntchito Baibulo lawo lokha.
-
A Mboni za Yehova anasintha Baibulo lawo kuti lizigwirizana ndi zimene amakhulupirira.
-
A Mboni za Yehova amakana kugwira ntchito zothandiza anthu ena.
-
A Mboni za Yehova amanyoza anthu a zipembedzo zina.
Onani masamba otsatirawa kuti mupeze mayankho.
-
1 Petulo 2:21) Komabe pali zina zimene timasiyana ndi Akhristu a zipembedzo zina. Mwachitsanzo, timakhulupirira kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu osati Mulungu Mwana. (Maliko 12:29) Sitikhulupirira kuti munthu akafa mzimu wake umapitirizabe kukhala ndi moyo komanso kuti Mulungu amaotcha anthu kumoto. Sitikhulupiriranso kuti anthu amene ali ndi udindo m’mipingo amayenera kupatsidwa maina aulemu posonyeza kuti ndi apamwamba kuposa ena.—Mlaliki 9:5; Ezekieli 18:4; Mateyu 23:8-10.
1 ZOONA. Timayesetsa kuchita zimene Yesu Khristu ankaphunzitsa ndiponso timatsanzira makhalidwe ake. ( -
2 ZABODZA. N’zoona kuti timakhulupirira kuti Mulungu analenga zinthu zonse. Komabe sitikhulupirira zimene anthu ena amanena zoti Mulungu analenga dzikoli m’masiku 6 enieni, a maola 24. Sitikhulupirira zimenezi chifukwa zimasemphana ndi zimene Baibulo limanena. Mwachitsanzo, mawu akuti ‘tsiku’ m’Baibulo angatanthauze nthawi yaitali ndithu. (Genesis 2:4; Salimo 90:4) Komanso anthu ena omwe amakhulupirira kuti dzikoli linalengedwa m’masiku 6 enieni a maola 24, amati dzikoli langokhalapo kwa zaka masauzande owerengeka chabe. Koma Baibulo limasonyeza kuti Mulungu anali atalenga kale kumwamba ndi dzikoli asanayambe ntchito yokonza dziko kuti pakhale zamoyo. 1
—Genesis 1:1. -
3 ZABODZA. Si zoona kuti timakana kulandira chithandizo chilichonse tikapita kuchipatala. Ndipotu enafe timagwira ntchito zachipatala ngati Luka yemwe anali dokotala. (Akolose 4:14) Komabe timakana kulandira chithandizo chosemphana ndi mfundo za m’Baibulo zomwe timakhulupirira. Mwachitsanzo, timakana kuikidwa magazi chifukwa Baibulo limaletsa kudya kapena kugwiritsa ntchito magazi molakwika.—Machitidwe 15:20, 28, 29.
Ngakhale zili choncho, timayesetsa kupeza chithandizo chabwino kwambiri. Mwachitsanzo, pali njira zina zothandizira a Mboni za Yehova popanda kuwaika magazi zomwenso ena omwe si a Mboni ayamba kuzigwiritsa ntchito. Masiku ano anthu ambiri akadwala amatha kusankha kuti asaikidwe magazi chifukwa choopa matenda opatsirana ndiponso mavuto ena amene amabwera munthu akathiridwa magazi.
-
4 ZOONA. Timakhulupirira kuti Baibulo lonse ‘linauziridwa ndi Mulungu.’ (2 Timoteyo 3:16) Tikamanena kuti Baibulo lonse tikutanthauza Chipangano Chakale ndi Chipangano Chatsopano. Koma mbali zimenezi ifeyo timazitchula kuti Malemba Achiheberi ndiponso Malemba Achigiriki Achikhristu. Timachita zimenezi posafuna kusonyeza kuti mbali ina ya Baibulo ndi yachikale kapena yosafunika.
-
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika likupezeka m’chinenero chathu, timaona kuti ndi bwino kuligwiritsa ntchito chifukwa lili ndi dzina la Mulungu, ndi lolondola komanso lomveka bwino. Koma m’Mabaibulo ena anachotsa dzina la Mulungu lakuti Yehova. Mwachitsanzo, m’mawu oyamba a Baibulo lina anatchula maina a anthu amene anagwira nawo ntchito yokonza Baibulolo. Koma dzina la Mulungu lakuti Yehova linachotsedwamo chonsecho Yehovayo ndiye Mlembi Wamkulu wa Baibulo. Koma mosiyana ndi Mabaibulo ena, Baibulo la Dziko Latsopano lili ndi dzina la Mulungu m’malo onse amene linkapezeka m’mipukutu yoyambirira ya Baibulo. 2
5 ZABODZA. Timagwiritsa ntchito Mabaibulo osiyanasiyana. Koma ngati -
6 ZABODZA. Tikazindikira kuti zimene timakhulupirira zikusiyana pang’ono ndi zimene Baibulo limanena, timasintha mfundo zimene tinkakhulupirirazo. M’mbuyomu tisanayambe kufalitsa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lachingelezi mu 1950, tinkagwiritsa ntchito Mabaibulo ena ndipo zimene tinkakhulupirira zinkakhala zogwirizana ndi Mabaibulowo.
-
7 ZABODZA. Ntchito yathu yolalikira imathandiza anthu ambiri. Mfundo za m’Baibulo zimene timaphunzira ndi anthu zimawathandiza kuti asiye makhalidwe oipa amene anali nawo monga kumwa mowa mwauchidakwa ndi kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. M’mipingo yathu timakhalanso ndi makalasi amene amathandiza anthu ambiri kuphunzira kuwerenga ndi kulemba. Pakachitika ngozi zadzidzidzi timathandiza anthu omwe akhudzidwa ndi ngoziyo kaya akhale a Mboni kapena ayi. Ndipo timayesetsa kuwauza mfundo zomwe zimawalimbikitsa ndi kuwatonthoza. 3
-
8 ZABODZA. Timatsatira malangizo a m’Baibulo akuti “muzilemekeza aliyense,” posatengera chipembedzo chimene ali. (1 Petulo 2:17, Today’s English Version) Mwachitsanzo, ngakhale kuti m’mayiko ena tilimo ambiri sitikakamiza andale kapena opanga malamulo kuti aletse kapena kutseka zipembedzo zina. Ndiponso sitipempha akuluakulu aboma kuti akhazikitse malamulo ogwirizana ndi zimene ife timakhulupirira n’cholinga choti anthu onse aziyendera zimenezo. Koma timayesetsa kulemekeza ufulu wa ena chifukwa n’zimenenso ifeyo timafuna.—Mateyu 7:12.
Mfundo zina za m’nkhaniyi zatengedwa pawebusaiti yathu ya jw.org. Kuti mudziwe zambiri pitani pamene palembedwa kuti ZOKHUDZA IFEYO >MAFUNSO OFUNSIDWA KAWIRIKAWIRI.
^ 1. Pankhani imeneyi timagwirizana ndi zimene asayansi anapeza zomwe zimasonyeza kuti dzikoli lakhalapo zaka mabiliyoni ambiri.
^ 2. Baibulo la Dziko Latsopano ndi losiyananso ndi Mabaibulo ena chifukwa limaperekedwa kwa anthu kwaulere. Zimenezi zikuthandiza kuti anthu ambiri aziwerenga Baibulo m’chinenero chawo. Baibuloli likupezeka m’zinenero 130 ndipo mukhoza kuwerenga kapena kulipanga dawunilodi pawebusaiti yathu ya www.pr418.com.
^ 3. Zina mwa ndalama zimene anthu amapereka mwa kufuna kwawo timazigwiritsa ntchito pothandizira anthu omwe akumana ndi ngozi zadzidzidzi. (Machitidwe 11:27-30) Popeza anthu amene amagwira ntchitoyi ndi ongodzipereka, ndalama zimene anthu amaperekazi sizimakhala zolipirira anthu koma zimakhaladi zothandizira anthu amene akhudzidwa ndi mavuto.