KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?
Nyerere Yokhala ndi Zinthu Zoiteteza ku Dzuwa
M’CHIPULULU cha Sahara mumapezeka nyerere zamtundu winawake zomwe zimatha kukhala m’malo otentha kwambiri omwe nyama zina sizingakhale. Masana, nyama zina zimene zimadya nyerere zamtunduwu zikabisala chifukwa cha dzuwa loswa mtengo, nyererezi zimapeza mwayi wotuluka ku una n’kumakafufuza zakudya. Zina mwa zakudyazi zimakhala tizilombo tomwe tafa ndi kutentha.
Taganizirani izi: Nyerereyi imatha kukhala pamalo otentha kwambiri chifukwa ili ndi cheya pamwamba komanso m’mbali mwa thupi lake koma kumimba kwake n’kopanda cheya. Cheyachi (1, 2), chimapangitsa kuti nyerereyi izioneka ya siliva. Cheya chilichonse chinapangidwa ngati kachubu kakang’ono kwambiri kokhala ndi mbali zitatu (3). Mbali ziwiri zam’mwamba zimakhala ndi timizere tating’ono kwambiri pomwe mbali yam’munsi imakhala yosalala. Izi zimathandiza nyerereyi m’njira ziwiri. Choyamba, cheyachi chimaiteteza ku cheza cha dzuwa. Chachiwiri, chimathandiza kuti isamatenthedwe kwambiri ndi zinthu zotentha zimene zaizungulira. Komanso popeza kumimba kwake n’kopanda cheya, khungu lakumimbako limatha kubweza kutentha kumene kukuchokera mumchenga. *
Nyerereyi singathe kukhala ndi moyo ngati thupi lake litatentha madigiri oposa 53.6. Koma chifukwa cha mmene inapangidwira, thupi lakeli silitentha kuposa pamenepa ngakhale kunja kutatentha kwambiri. Akatswiri akuyesetsa kuti apange zinthu zoziziritsira nyumba komanso zinthu zina popanda kugwiritsa ntchito mafani kapena zipangizo zina potengera mmene thupi lanyerereyi linapangidwira.
Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti nyerereyi ikhale ndi zinthu zoiteteza ku dzuwa, kapena pali winawake amene anailenga chonchi?
^ ndime 4 Pali zinthu zinanso zimene zimathandiza nyerereyi kukhala m’malo otentha kwambiri. Ili ndi mapulotini apadera m’thupi mwake amene sasungunuka akatenthedwa kwambiri. Ilinso ndi miyendo yaitali yomwe imaithandiza kuti isamayandikane ndi mchenga wotentha komanso kuti izithamanga kwambiri. Chinthu chinanso chimene chimaithandiza n’chakuti imatha kulondola una wake mosavuta ndiponso mwamsanga isanapserere ndi dzuwa.