Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUNGATANI KUTI MUZIKHALA WOSANGALALA?

Kukhala Wathanzi Komanso Wopirira

Kukhala Wathanzi Komanso Wopirira

MATENDA AAKULU KOMANSO KULUMALA ZINGACHITITSE KUTI MUNTHU ASAMASANGALALE. Bambo wina dzina lake Ulf, poyamba anali wathanzi komanso wamphamvu. Koma nthawi ina bamboyu analumala ndipo ananena kuti: “Ndinakhumudwa kwambiri. Ndinkangomva kuti ndilibiretunso mphamvu ndipo palibenso chimene ndingachite.”

Zimene zinachitikira a Ulf zikutithandiza kukumbukira kuti nthawi iliyonse zinthu zikhoza kusintha pa moyo wathu. Komabe pali zinthu zina zomwe tingachite kuti tidziteteze ku matenda. Koma bwanji ngati tikumadwaladwala? Kodi ndiye kuti basi sitingakhalenso osangalala? Ayi, n’zothekabe kukhala osangalala ngakhale tikukumana ndi mavuto. Koma choyamba, tiyeni tione mfundo zina zomwe zingatithandize kukhala ndi moyo wathanzi.

‘MUSAMACHITE ZINTHU MOPITIRIRA MALIRE.’ (1 Timoteyo 3:2, 11) Nthawi zambiri kudya kapena kumwa mopitirira malire kumabweretsa mavuto aakulu pathupi lathu ndipo zimachititsanso kuti tiziwononga ndalama. Baibulo limanena kuti: “Usakhale pakati pa anthu omwa vinyo kwambiri, ndiponso pakati pa anthu odya nyama mosusuka. Chifukwa chidakwa ndiponso munthu wosusuka adzasauka.”​—Miyambo 23:20, 21.

MUSAMACHITE ZINTHU ZOMWE ZINGAIPITSE THUPI LANU. Baibulo limanena kuti: “Tiyeni tidziyeretse ndipo tichotse chinthu chilichonse choipitsa thupi kapena mzimu.” (2 Akorinto 7:1) Munthu amaipitsa thupi lake akamadya kapena kusuta fodya, kumwa mowa mwauchidakwa kapenanso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Mwachitsanzo, pa nkhani ya kusuta, bungwe lina la ku United States linanena kuti: “Munthu amene amasuta, akhoza kudwala, kulumala ndipo mtima, mapapo komanso pafupifupi ziwalo zina zonse za m’thupi lake zimawonongeka.”​—U.S. Centers for Disease Control and Prevention.

MUZIONA KUTI THUPI KOMANSO MOYO WANU NDI ZAMTENGO WAPATALI. Baibulo limanena kuti: “Chifukwa cha iye [Mulungu] tili ndi moyo, timayenda ndipo tilipo.” (Machitidwe 17:28) Kuzindikira mfundo imeneyi kungatithandize kuti tizipewa kuchita zinthu zomwe zingaike moyo wathu pangozi, kaya tikugwira ntchito, tikuyendetsa galimoto kapenanso kuchita masewera olimbitsa thupi. Ndipo pangakhale phindu lanji ngati munthu atachita zosangalatsa zinazake kwa kanthawi kochepa koma n’kulumala kwa moyo wake wonse?

MUSAMAGANIZIRE KWAMBIRI ZINTHU ZOFOOKETSA. Zimene mumaganiza zimakhudzanso mmene thupi lanu limagwirira ntchito. Choncho muzipewa kukhala ndi nkhawa kwambiri, kukwiya mopitirira malire, nsanje komanso kuganizira zinthu zofooketsa. Pa Salimo 37:8 Baibulo limati: “Usapse mtima ndipo pewa kukwiya.” Komanso limanena kuti: “Musamade nkhawa za tsiku lotsatira, chifukwa tsiku lotsatira lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso.”​—Mateyu 6:34.

MUZIGANIZIRA ZINTHU ZOLIMBIKITSA. Lemba la Miyambo 14:30 limati: “Mtima wodekha ndiwo moyo wa munthu.” Ndipo Baibulo limanenanso kuti: “Mtima wosangalala ndiwo mankhwala ochiritsa.” (Miyambo 17:22) Mawuwa ndi ogwirizana ndi zimene madokotala amanena. Mwachitsanzo, dokotala wina wa ku Scotland ananena kuti: “Munthu amene nthawi zambiri amakhala wosangalala, sadwaladwala ndipo zimenezi n’zosiyana kwambiri ndi anthu amene sakhala osangalala.”

MUZIKHALA WOPIRIRA. Mofanana ndi a Ulf omwe tawatchula poyamba aja, nthawi zina tingakumane ndi vuto loti palibenso zomwe tingachite ndipo timangofunika kupirira. Ndipotu timafunika kupeza njira zabwino zotithandiza kuti tipirire. Anthu ena akakumana ndi mavuto amangokhalira kudandaula ndipo zimenezi zimangowonjezera mavutowo. Paja lemba la Miyambo 24:10 limanena kuti: “Ukafooka pa tsiku la masautso, mphamvu zako zidzakhala zochepa.”

Komabe ena akasokonezeka maganizo amayesetsa kupeza njira zowathandiza kuti ayambirenso kukhala osangalala. Zimenezi ndi zomwenso a Ulf anachita. Iwo ananena kuti atapempha Yehova kuti awathandize komanso kuganizira mfundo zolimbikitsa za m’Baibulo, anayamba kuona kuti zinthu zayamba kuwayendera bwino ndipo anasiya kuganizira kwambiri za mavuto awo. Komanso mofanana ndi mmene zimakhalira ndi munthu amene wakumana ndi mayesero aakulu, a Ulf anaphunzira kuchitira ena chifundo. Ndipo khalidweli limawathandiza kuti aziuzanso ena za uthenga wolimbikitsa wa m’Baibulo.

Bambo enanso dzina lawo a Steve anakumanapo ndi mavuto aakulu. Ali ndi zaka 15 anagwa mumtengo n’kuvulala kwambiri moti ziwalo zawo kuchokera m’khosi mpaka m’miyendo sizinkagwira ntchito. Koma atafika zaka 18, manja awo anayambiranso kugwira ntchito. Kenako anapita kuyunivesite kumene anakayamba kumwa mankhwala osokoneza bongo, mowa komanso kuchita zachiwerewere. A Steve ankaona kuti alibenso tsogolo. Koma atayamba kuphunzira Baibulo anazindikira kuti moyo ndi wofunika kwambiri ndipo anayamba kusintha makhalidwe awo oipa. A Steve ananena kuti: “Panopa sindimadzionanso ngati wachabechabe. Ndili ndi mtendere wamumtima, ndimakhala wosangalala komanso ndili ndi moyo wokhutira.”

Zimene a Steve komanso a Ulf ananena zikutikumbutsa mawu amene timawawerenga pa Salimo 19:7, 8 akuti: “Chilamulo cha Yehova ndi changwiro, chimabwezeretsa moyo. . . . Malamulo ochokera kwa Yehova ndi olungama, amasangalatsa mtima. Chilamulo cha Yehova ndi choyera, chimatsegula maso.”