MUNGATANI KUTI MUZIKHALA WOSANGALALA?
Kukhala ndi Chiyembekezo
“Ndikuganizira zokupatsani mtendere osati masoka, kuti mukhale ndi chiyembekezo chabwino ndiponso tsogolo labwino.”—Yeremiya 29:11.
“CHIYEMBEKEZO N’CHOFUNIKA KWAMBIRI PA MOYO WATHU WAUZIMU.” Linatero buku lina. Bukulo linanenanso kuti: “Munthu akakhala ndi chiyembekezo sadziona kuti ali yekhayekha, sadziona ngati wachabechabe komanso sakhala ndi mantha.”—Hope in the Age of Anxiety.
Baibulo limasonyeza kuti anthufe timafunika kukhala ndi chiyembekezo. Komabe limatichenjezanso kuti tisamayembekezere zinthu zosatheka. Lemba la Salimo 146:3 limati: “Musamakhulupirire anthu olemekezeka, kapena mwana wa munthu wina aliyense wochokera kufumbi amene alibe chipulumutso.” M’malo modalira anthu kuti athetse mavuto athu, tingasonyeze kuti ndife oganiza bwino tikamakhulupirira Mlengi wathu amene ali ndi mphamvu zokwaniritsa zonse zimene anatilonjeza. Tiyeni tione zimene analonjeza:
ZOIPA ZONSE ZIDZATHA NDIPO OLUNGAMA ADZAKHALA PA MTENDERE MPAKA KALEKALE. Lemba la Salimo 37:10, 11 limanena kuti: “Patsala kanthawi kochepa, woipa sadzakhalakonso . . . Koma anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, Ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.” Ndipo vesi 29 limapitiriza kuti “olungama . . . adzakhala” padziko lapansi “kwamuyaya.”
SIKUDZAKHALANSO NKHONDO. Baibulo limati: “Yehova . . . akuletsa nkhondo mpaka kumalekezero a dziko lapansi. Wathyola uta ndi kuduladula mkondo. Ndipo watentha magaleta pamoto.”—Salimo 46:8, 9.
SIKUDZAKHALANSO MATENDA, KUVUTIKA KAPENA IMFA. Baibulo limati: “Chihema cha Mulungu chili pakati pa anthu . . . Adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”—Chivumbulutso 21:3, 4.
KUDZAKHALA CHAKUDYA CHOKWANIRA KWA ALIYENSE. Baibulo limanena kuti: “Padziko lapansi padzakhala tirigu wambiri. Pamwamba pa mapiri padzakhala tirigu wochuluka.”—Salimo 72:16.
UFUMU WA KHRISTU NDI BOMA LACHILUNGAMO LOMWE LIDZALAMULIRE DZIKOLI. Baibulo limati: “[Yesu Khristu] anamupatsa ulamuliro, ulemerero, ndi ufumu kuti anthu a mitundu yosiyanasiyana, olankhula zinenero zosiyanasiyana azimutumikira. Ulamuliro wake udzakhalapo mpaka kalekale ndipo sudzatha. Ufumu wake sudzawonongedwa.”—Danieli 7:14.
Kodi tingatsimikize bwanji kuti zimenezi zidzachitikadi? Yesu ali padziko lapansi anasonyeza kuti ndi woyeneradi kukhala Mfumu chifukwa anachiritsa odwala, anapereka chakudya kwa osauka komanso anaukitsa akufa. Yesu anaphunzitsanso mfundo zofunika kwambiri zothandiza kuti anthu adzakhale mwamtendere komanso mogwirizana mpaka kalekale. Yesu ananeneratunso zomwe zidzachitike m’tsogolo kuphatikizaponso zizindikiro zosonyeza kuti tikukhala m’masiku otsiriza.
MAVUTOWA ADZATHA POSACHEDWA
Yesu sananene kuti masiku otsiriza adzadziwika ndi zinthu ngati mtendere ndi chitetezo. Koma ananena zinthu zosiyana kwambiri ndi zimenezi. Anatchula zinthu zingapo zomwe zidzakhale ngati, “chizindikiro . . . cha mapeto a nthawi ino.” Zinthu zake ndi nkhondo za m’mayiko, kuchepa kwa chakudya, miliri komanso zivomerezi zikuluzikulu. (Mateyu 24:3, 7; Luka 21:10, 11; Chivumbulutso 6:3-8) Yesu ananenanso kuti: “Chifukwa cha kuwonjezeka kwa kusamvera malamulo, chikondi cha anthu ambiri chidzazirala.”—Mateyu 24:12.
Wolemba Baibulo wina anasonyeza kuti kuzirala kapena kuti kuchepa kwa chikondi kudzaonekera m’njira zingapo. Mwachitsanzo pa 2 Timoteyo 3:1-5 timawerenga kuti ‘m’masiku otsiriza,’ anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, okonda zosangalatsa, odzikweza komanso oopsa. M’mabanja simudzakhala chikondi ndipo ana adzakhala osamvera makolo. Atsogoleri achipembedzo achinyengo adzakhala paliponse.
Mavuto amene akuchitikawa ndi umboni wakuti tikukhala m’masiku otsiriza. Akusonyezanso kuti Ufumu watsala pang’ono kubweretsa madalitso padzikoli. Yesu ananenanso zinthu zabwino zimene zidzachitike m’masiku otsiriza. Ananena kuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”—Mateyu 24:14.
Uthenga wabwinowu umachenjeza anthu ochita zoipa. Umaperekanso chiyembekezo kwa anthu ochita zolungama ndipo umawatsimikizira kuti madalitso omwe Mulungu analonjeza akwaniritsidwa posachedwa. Kodi mukufuna kudziwa zambiri za madalitso amenewa? Ngati ndi choncho, pitani kuseri kwa magaziniyi.