MUNGATANI KUTI MUZIKHALA WOSANGALALA?
Kukhululuka
“NDILI MWANA, M’BANJA MWATHU ANTHU ANKATUKWANA KOMANSO KULALATA.” Anatero mayi wina dzina lake Patricia. Mayiyu ananenanso kuti: “Nditakula, zinkandivutabe kukhululukira munthu wina. Wina akandilakwira, ndinkangoziganirabe kwa masiku angapo mpaka kumalephera kugona.” Munthu amene amakhalira kukwiya komanso kusunga zifukwa, sakhala wosangalala komanso sakhala wathanzi. Akatswiri anapeza kuti anthu omwe zimawavuta kukhululukira anzawo . . .
-
Amasowa ocheza nawo chifukwa anthu ena amawapewa akazindikira kuti akakhumudwa nkhani yake siitherapo
-
Sachedwa kukhumudwa, amakhala ankhawa ndipo amavutika maganizo
-
Amangoganizira zinthu zomwe zalakwika ndipo sakhala osangalala
-
Amaona kuti sangathe kutsatira mfundo za m’Malemba
-
Amakhala ndi vuto la maganizo, amavutika ndi matenda monga a mtima, kuthamanga kwa magazi, kuphwanya kwathupi, nyamakazi komanso kupweteka kwa mutu *
KODI KUKHULULUKA N’KUTANI? Kukhululuka kumatanthauza kuiwala zimene munthu wina watilakwira komanso kusakhala ndi maganizo aliwonse ofuna kubwezera. Koma sikutanthauza kulekerera zinthu zoipa, kuchepetsa nkhani kapena kungoziona ngati sizinachitike. Komabe, munthu akaganizira mofatsa za nkhaniyo m‘pamene amasankha kukhululukira munthu wina. Amachita zimenezi ndi cholinga cholimbikitsa mtendere komanso kukhalabe pa ubwenzi ndi mnzakeyo.
Munthu amene amakhululukira ena amasonyeza kuti ali ndi mtima womvetsa. Amakhululuka chifukwa chodziwa kuti tonse timalakwitsa m’zolankhula zathu komanso zochita. (Aroma 3:23) Ndipo Baibulo limatilimbikitsa kuti: “Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira za mnzake.”—Akolose 3:13.
Choncho ndi pomveka kunena kuti kukhululukira ena ndi njira imodzi yosonyezera kuti timakonda anzathu. Paja chikondi “chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu kwambiri kuposa chinthu china chilichonse.” (Akolose 3:14) Mogwirizana ndi zomwe zinalembedwa pawebusaiti ya Mayo Clinic, tikamakhululukira anzathu . . .
-
Timakhala bwino ndi anzathu, timachitira chifundo komanso kukonda anthu omwe atilakwira
-
Timakhala ndi maganizo abwino komanso timakhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu
-
Sitikhala ndi nkhawa, kuvutika maganizo komanso sitikhala okwiya
-
Sitikhala ndi matenda ovutika maganizo
MUSAMADZIIMBE MLANDU. Magazini ina inanena kuti zimakhala zovuta kuti tiiwale zomwe tinalakwitsa komabe kuchita zimenezi n’kothandiza kuti tikhale athanzi komanso oganiza bwino. (Disability & Rehabilitation) Koma kodi mungatani kuti musamadziimbe mlandu pa zomwe munalakwitsa?
-
Musamayembekezere kuti nthawi zonse muzingochita zinthu bwinobwino osalakwitsapo. Koma muzikumbukira kuti tonse timalakwitsa zinthu zina.—Mlaliki 7:20
-
Mukalakwitsa zinthu, muziphunzirapo kanthu kuti musadzabwerezenso nthawi ina
-
Muzikhala wodekha chifukwa sizingatheke kuti lero ndi lero mukonze zomwe mumalakwitsa komanso kusintha zomwe munazolowera.—Aefeso 4:23, 24
-
Muzigwirizana ndi anthu abwino omwe angamakulimbikitseni komanso kukuuzani zinthu moona mtima.—Miyambo 13:20
-
Mukakhumudwitsa winawake, muzivomereza kuti mwalakwitsa ndipo muzimupepesa mofulumira. Mukamakhala mwamtendere ndi anthu ena, mumakhalanso ndi mtendere wa mumtima.—Mateyu 5:23, 24
MFUNDO ZA M’BAIBULO NDI ZOTHANDIZA KWAMBIRI
Patricia amene tamutchula kumayambiriro kwa nkhaniyi ataphunzira Baibulo, anayamba kukhululukira anthu ena. Iye ananena kuti: “Panopa ndinasiya kumangokhala wokwiya. Sindivutikanso maganizo komanso sindisowetsa anthu ena mtendere. Mfundo za m’Baibulo zimasonyeza kuti Mulungu amatikonda ndipo amatifunira zabwino.”
Mwamuna wina dzina lake Ron, panopa amasangalala chifukwa chotsatira mfundo za m’Baibulo. Iye ananena kuti: “Anthu ena akandikhumudwitsa, ndimatha kuugwira mtima. Koma sindingakakamize ena kuti nawonso aziugwira mtima akakhumudwa. Ndimadziwa kuti ngati ndikufuna kukhala pamtendere ndi anthu, sindiyenera kusunga zifukwa. Ndinayamba kuona kuti mtendere ndi kusunga zifukwa siziyenderana. Sindingathe kukhala wamtendere koma nditasungiranso anthu ena zifukwa. Panopa ndimasangalala ndipo sindimadziimbanso mlandu.”
^ ndime 8 Kuchokera: Pawebusaiti ya Mayo Clinic ndi ya Johns Hopkins Medicine komanso m’magazini ya Social Psychiatry and Psychiatric Epidemiology.