Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Madokotala akafuna kuthandiza munthu amafunika kudziwa kaye chomwe chikuyambitsa vutolo

CHIFUKWA CHAKE TIKULEPHERA KUTHANA NDI MAVUTO

Kudziwa Chimene Chikuyambitsa Mavuto

Kudziwa Chimene Chikuyambitsa Mavuto

Kodi mukuganiza kuti anthu angathedi kuthetsa mavuto ambirimbiri omwe amatichititsa kuti tizikhala osatetezeka komanso omwe akuchititsa dzikoli kukhala pangozi? Kuti mavuto athe mpofunika kulimbana ndi chimene chimawayambitsa.

Kuti timvetse zimenezi tiyeni tiyerekezere ndi zimene zinachitikira munthu wina dzina lake Tom, yemwe anadwala kwambiri mpaka kumwalira. Kodi vuto linali chiyani? Dokotala amene anamuthandiza chakumapeto kwa moyo wake, analemba kuti, “Tom atangoyamba kudwala, palibe anayesa kufufuza chomwe chinayambitsa vuto lake.” Zikuoneka kuti madokotala amene ankamuthandiza vutoli litangoyamba, ankangomupatsa mankhwala ochepetsa ululu.

Kodi sitinganene kuti zimenezi ndi zomwe anthu akuchita polimbana ndi mavuto adzikoli? Mwachitsanzo, polimbana ndi uchigawenga boma limakhazikitsa malamulo, kutchera makamera komanso kupereka mphamvu kwa apolisi kuti azithana ndi anthu ophwanya malamulo. Ngakhale kuti njirazi zimaoneka zothandiza, sizithetsa chimene chimayambitsa vutoli. Ndipotu anthu amasonyeza khalidwe linalake potengera zimene amaganiza, kukhulupirira komanso zimene amakonda.

Daniel amakhala m’dziko lina la ku South America. M’dzikoli zinthu sizikuyenda bwino pa nkhani ya zachuma. Iye anati: “Poyamba zinthu zinali bwino kwambiri. Kunalibe mbava zoopseza ndi mfuti. Koma pano kulikonse anthu amakhala mwamantha. Mavuto a zachuma atipangitsa kuona kuti anthu ambiri ndi adyera komanso saona moyo ndi katundu wa anzawo kukhala zofunika.”

Munthu wina yemwe tangomupatsa dzina loti Elias, anathawa nkhondo ku Middle East ndipo patapita nthawi anaphunzira Baibulo. Iye anati: “Achinyamata ambiri mumzinda womwe ndinkakhala, ankalimbikitsidwa ndi makolo awo, atsogoleri andale komanso achipembedzo kuti azimenya nawo nkhondo ndipo akatero azidzapatsidwa ulemu kwambiri. Zimenezi ndi zomwenso achinyamata a mbali inayo ankauzidwa. Izi zinandipangitsa kuona kuti kukhulupirira anthu kulibe phindu.”

Baibulo linanena molondola kuti:

  • “Maganizo a anthu amakhala oipa kuyambira pa ubwana wawo.”​—Genesis 8:21.

  • “Mtima ndi wonyenga kwambiri kuposa china chilichonse ndipo ungathe kuchita china chilichonse choipa. Ndani angaudziwe?”—Yeremiya 17:9.

  • “Maganizo oipa, za kupha anthu, za chigololo, za dama, za kuba, maumboni onama . . . zimachokera mumtima.”​—Mateyu 15:19.

Anthufe tikulephera kuthetsa zizolowezi zoipa zomwe zimachititsa ena kuti azivulaza anzawo. Monga mmene taonera m’nkhani yapitayi, anthu akupitiriza kukhala ndi zizolowezi zoipa. (2 Timoteyo 3:1-5) Zimenezi zikuchitika ngakhale kuti panopa anthu akudziwa zinthu zambiri komanso pali njira zambiri zimene amagwiritsa ntchito pofuna kulankhulana. Ndiye n’chifukwa chiyani tikulephera kupangitsa dzikoli kukhala malo otetezeka? Kodi kapena tikungolimbikira mtunda wopanda madzi?

KODI TIKULIMBANA NDI ZINTHU ZOSATHEKA?

Ngakhale pakanapezeka njira yothetsera zizolowezi zoipa zimene anthu amakhala nazo, sitikanakwanitsabe kupangitsa dzikoli kukhala malo otetezeka kwa onse. Tikutero chifukwa chakuti mwachibadwa tili ndi malire ochitira zinthu.

Mfundo yosavuta kumva ndi imene ili pa Yeremiya 10:23, pomwe pamati: “Munthu amene akuyenda alibe ulamuliro wowongolera mapazi ake.” Inde, anthufe sitinalengedwe m’njira yoti tizidzilamulira. Monga mmene zilili kuti sitinalengedwe kuti tizikhala m’madzi, sitinalengedwenso kuti tizilamulirana.

Monga mmene zilili kuti sitinalengedwe kuti tizikhala m’madzi, sitinalengedwenso kuti tizilamulirana

Taganizirani izi: Kodi anthu ambiri amamva bwanji wina akamawauza mfundo zoti aziyendera? Kodi amasangalala akamauzidwa zochita pa nkhani yochotsa mimba, kupereka chilango komanso mmene angaphunzitsire ana awo? Zimenezi ndi zina mwa nkhani zimene zimachititsa kuti anthu azigawikana. Choncho zomwe Baibulo limanena ndi zomveka ndithu ngakhale kuti ambiri zimawavuta kuvomereza. Mwachidule, tinganene kuti sitinapatsidwe mphamvu kapena udindo wolamulira anthu ena. Ndiye kodi ndi ndani amene angatithandize pa mavuto amene timakumana nawo?

Mulungu yekha ndi amene angatithandize. Pajatu iye ndi amene anatilenga. Ndipotu sanatiiwale ngati mmene anthu ena amaganizira. Baibulo limasonyeza kuti Mulungu amatikonda kwambiri. Tikamawerenga ndi kumvetsa mfundo za m’Baibulo m’pamenenso timamvetsa bwino mmene anatilengera komanso zimene zinachitika kuti tizivutika. N’chifukwa chake katswiri wina wa nzeru za anthu wa ku Germany analemba kuti, “anthu komanso maboma sanaphunzirepo kanthu pa zimene zinachitika m’mbuyomu kapenanso kusintha zochita zawo.”

MFUNDO ZA M’BAIBULO ZIMATITETEZA

Nthawi ina Yesu ananena kuti “nzeru imatsimikizirika kuti ndi yolungama chifukwa cha zotsatira zake.” (Luka 7:35) Chitsanzo cha nzeru zimenezi chikupezeka palemba la Yesaya 2:22, lomwe limati: “Kuti zinthu zikuyendereni bwino, musadalire munthu wochokera kufumbi.” Malangizo anzeru amenewa angatiteteze kuti tisamapusitsidwe ndi malonjezo abodza. Kenneth amakhala mumzinda wina wa ku North America womwe kumachitika zipolowe. Iye anati: “Nthawi zambiri andale amatilonjeza kuti asintha zinthu koma sakwanitsa. Kulephera kwawo ndi umboni woti zimene Baibulo limanena ndi zoona.”

Daniel amene tamutchula kale uja ananenanso kuti: “Tsiku lililonse ndimaona umboni wosonyeza kuti anthu sitingathedi kudzilamulira . . . Kukhala ndi ndalama kubanki kapena kupanga zinthu zodzakuthandiza ukadzakalamba, si ndiye kuti basi udzakhala wotetezeka. Ndaonapo anthu ambiri atapanga zonsezi komabe n’kukumana ndi zokhumudwitsa.”

Sikuti mfundo za m’Baibulo zimangotiteteza kuti tisapusitsidwe ndi malonjezo abodza. Zimatithandizanso kukhala ndi chiyembekezo monga mmene tionere m’nkhani zotsatira.