Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MAVUTO AMENE TIKUKUMANA NAWO

Zomwe Zikuchititsa Kuti Tikhale Osatetezeka

Zomwe Zikuchititsa Kuti Tikhale Osatetezeka

Lipoti lina loona za mmene chuma chikuyendera padziko lonse linati: “Ngakhale kuti masiku ano anthu apita patsogolo pa nkhani ya sayansi, luso la zopangapanga, komanso kayendetsedwe ka chuma, panopa ndi pomwe zinthu zafika poipa kwambiri pa nkhani zachuma, ndale komanso kuwonongeka kwa chilengedwe.”​—The Global Risks Report 2018, World Economic Forum.

N’CHIFUKWA CHIYANI AKATSWIRI AMBIRI AKUDERA NKHAWA ZA TSOGOLO LATHU KOMANSO LA DZIKOLI? TIYENI TIKAMBIRANE MAVUTO ENA AMENE TIMAKUMANA NAWO.

  • UCHIGAWENGA WA PA INTANETI: Nyuzipepala ina inati, “Masiku ano kugwiritsa ntchito intaneti n’koopsa. Anthu ena amagwiritsa ntchito intaneti pofuna kuchitira nkhanza anzawo, kugwiririra ana, kulimbikitsa zachiwawa komanso kuba zinthu za pamakompyuta a anthu ena. Milandu yambiri panopa ndi yokhudza kugwiritsa ntchito mwakuba zinthu zachinsinsi za anthu ena. . . . Zinthu zambiri zankhanza zimene anthu amachita zimasonyezedwanso pa intaneti.”​—The Australian.

  • MAVUTO A ZACHUMA: Malinga ndi lipoti laposachedwapa la bungwe la Oxfam, anthu 8 olemera kwambiri padziko lonse ali ndi chuma chofanana ndi chomwe hafu ya anthu onse padzikoli ali nacho. Lipotilo linati, “Kusayenda bwino kwa chuma kwachititsa kuti olemera azingolemererabe ndiponso kuti osauka azingosaukirabe. Ndipo ambiri amene akuvutika ndi umphawiwu ndi akazi.” Ena ali ndi mantha kuti zimenezi zikhoza kudzachititsa kuti anthu adzachite zionetsero zosonyeza kukwiya.

  • KUZUNZIDWA KWA ANTHU KOMANSO NKHONDO: Lipoti la mu 2018 la nthambi ya bungwe la United Nations yoona za anthu othawa kwawo linati: “Panopo kuli anthu ambiri amene anathawa kwawo kuposa mmene zinalili m’mbuyomu.” Anthu oposa 68 miliyoni anakakamizika kuthawa kwawo chifukwa cha nkhondo kapena kuzunzidwa. Lipotili linatinso, “Pa masekondi awiri aliwonse, munthu m’modzi amakakamizika kuthawa kwawo.”

  • KUWONONGEKA KWA CHILENGEDWE: Lipoti lina linati, “Mitundu yambiri ya zinyama komanso zomera ikutha mofulumira. Mpweya komanso nyanja zikupitirizabe kuwonongeka ndipo izi zachititsa kuti moyo wa anthu ukhale pangozi.” (The Global Risks Report 2018) Chiwerengero cha tizilombo tomwe timathandiza kuti mbewu zibereke chayamba kuchepa m’mayiko ambiri, choncho asayansi akuona kuti zinthu zachilengedwe zikhoza kutheratu. Nazonso zomera zam’madzi zikutha. Iwo akuganiza kuti pafupifupi hafu ya zomerazi inafa zaka 30 zapitazo.

Koma kodi pali chimene tingachite kuti anthu komanso zinthu za padzikoli zikhale zotetezeka? Ambiri amaona kuti zimenezi zingatheke ngati anthu ataphunzitsidwa. Koma kodi ndi maphunziro otani amene angathandize pa nkhaniyi? Nkhani zotsatirazi ziyankha mafunso amenewa.