Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ana amachita zinthu mwachikondi akamaona zimene makolo awo amachita

ZOMWE ZIKUCHITIKA POLIMBANA NDI MAVUTO

Maphunziro Okhudza Makhalidwe Abwino

Maphunziro Okhudza Makhalidwe Abwino

Anyamata ena omwe anali paulendo wa sukulu, anadzudzulidwa chifukwa chochitira mnyamata mnzawo nkhanza zokhudza kugonana. Anyamata onsewo anali a pasukulu inayake yapamwamba ku Canada. Zimenezi zitachitika mtolankhani wa nyuzipepala ina dzina lake Leonard Stern analemba kuti: “Maphunziro, ngakhale atakhala a m’sukulu zapamwamba komanso kukhala ndi moyo wapamwamba sizikuthandiza achinyamata kuti asamachite makhalidwe oipa.”​—Ottawa Citizen.

Stern ananenanso kuti: “Ena akhoza kuona kuti cholinga chachikulu cha makolo ndi kuphunzitsa ana awo kuti akhale ndi makhalidwe abwino. Koma zoona n’zakuti makolo ambiri amangofuna kuti ana awo azikhoza bwino kusukulu komanso kuti adzapeze ntchito zabwino n’kumalandira ndalama zambiri.”

Kunena zoona maphunziro a kusukulu ndi ofunika. Komatu maphunziro amenewa ngakhale atakhala apamwamba, sangathandize munthu kuti asakhale ndi maganizo oipa. Ndiye kodi tingapeze kuti maphunziro amene angathandize anthu kukhala ndi makhalidwe abwino?

MAPHUNZIRO OTHANDIZA ANTHU KUKHALA NDI MAKHALIDWE ABWINO KOMANSO KUKHALA PA UBWENZI NDI MULUNGU

Baibulo lili ngati galasi loyang’anira. Tikamaliwerenga timatha kuona bwino zofooka zathu ndi zinthu zina zimene tikulephera kuchita. (Yakobo 1:23-25) Koma sikuti Baibulo limangotithandiza kudziwa zofooka zathu, limatithandizanso kusintha kuti tikhale ndi makhalidwe abwino omwe angatithandize kukhala mwamtendere ndi anthu ena. Makhalidwe amenewa akuphatikizapo ubwino, kukoma mtima, kuleza mtima, kudziletsa komanso chikondi. Ndipo Baibulo limanena kuti chikondi “chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu kwambiri.” (Akolose 3:14) N’chifukwa chiyani tingati chikondi ndi khalidwe lofunika kwambiri? Tiyeni tikambirane zimene Baibulo limanena zokhudza khalidweli.

  • “Chikondi n’choleza mtima ndiponso n’chokoma mtima. Chikondi sichichita nsanje, sichidzitama, sichidzikuza [chifukwa cha kunyada], sichichita zosayenera, sichisamala zofuna zake zokha, sichikwiya. Sichisunga zifukwa. Sichikondwera ndi zosalungama [zinthu zoipa], koma chimakondwera ndi choonadi. Chimakwirira zinthu zonse, . . . chimapirira zinthu zonse. Chikondi sichitha.”​—1 Akor. 13:4-8.

  • “Chikondi sichilimbikitsa munthu kuchitira zoipa mnzake.”​—Aroma 13:10.

  • “Koposa zonse, khalani okondana kwambiri, pakuti chikondi chimakwirira machimo ochuluka.”​—1 Petulo 4:8.

Tonsefe timakhala omasuka komanso timamva kuti ndife otetezeka tikakhala pakati pa anthu omwe amatikonda. Timamva choncho chifukwa timadziwa kuti anzathuwo amatifunira zabwino ndipo sangafune kutikhumudwitsa mwadala.

Munthu amene amakonda ena, amalolera kudzimana zinthu zina komanso kusintha zomwe amachita chifukwa chofuna kuthandiza anthu ena. Mwachitsanzo bambo ena omwe tangowapatsa dzina lakuti a George ankafunitsitsa kuti azicheza ndi mdzukulu wawo. Koma vuto linali loti iwowo ankasuta fodya kwambiri ndipo bambo ake a mwanayo sankafuna kuti agogo akewo azimunyamula kwinaku akusuta fodya. Ndiye kodi a George anatani? Ngakhale kuti anakhala akusuta fodya kwa zaka 50, anasankha kusiya kusutako chifukwa cha mdzukulu wawoyo. Umenewutu ndi umboni woti chikondi ndi champhamvu kwambiri.

Baibulo limatithandiza kukhala ndi makhalidwe abwino monga ubwino, kukoma mtima, komanso chikondi

Chikondi ndi khalidwe limene timachita kuphunzira. Makolo ali ndi udindo waukulu wophunzitsa ana awo mmene angasonyezere khalidweli. Pajatu makolo amathandiza ana awo akavulala, akadwala komanso amawadyetsa ndi kuwateteza. Makolo abwino amaphunzitsa ana awo komanso amapeza nthawi yocheza nawo. Amalangizanso ana awo zomwe zimaphatikizapo kuwathandiza kusiyanitsa zoyenera ndi zosayenera. Makolo abwino amayesetsanso kuti ana awo aziphunzira makhalidwe abwino poona zimene iwowo akuchita.

N’zomvetsa chisoni kuti makolo ena amalephera kukwaniritsa udindo wawo. Kodi zimenezi zikusonyeza kuti ana awo sangadzakhale anthu abwino? Ayi sitingatero. Chifukwa pali achikulire ena omwe anakulira m’mabanja amene sankawaphunzitsa makhalidwe abwino koma anasintha kwambiri. Panopa ndi anthu odalirika komanso amachita zinthu moganizira ena. Monga mmene tionere m’nkhani yotsatirayi, ambiri mwa iwo ndi oti anthu ena sankaganizira kuti angasinthe.