Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MMENE MAVUTO ONSE ADZATHERE

Ufumu wa Mulungu Ukamadzalamulira “Padzakhala Mtendere Wochuluka”

Ufumu wa Mulungu Ukamadzalamulira “Padzakhala Mtendere Wochuluka”

Posachedwapa Ufumu wa Mulungu womwe takhala tikuyembekezera kwa nthawi yaitali, udzabweretsa mtendere padziko lonse lapansi. Mogwirizana ndi zimene Mulungu anatilonjeza pa Salimo 72:7, padzikoli “padzakhala mtendere wochuluka.” Koma kodi ufumuwu udzayamba liti kulamulira? Kodi padzachitika zotani kuti Ufumuwo uyambe kulamulira? Nanga tidzapindula bwanji ndi ulamuliro umenewo?

KODI UFUMU WA MULUNGU UDZABWERA LITI?

Baibulo linaneneratu zinthu zingapo zomwe zidzachitike monga “chizindikiro” chosonyeza kuti Ufumu wa Mulungu watsala pang’ono kubwera. Zinthuzi ndi monga nkhondo za mayiko, njala, matenda, zivomezi komanso kuchuluka kwa anthu osamvera malamulo.​—Mateyu 24:3, 7, 12; Luka 21:11; Chivumbulutso 6:2-8.

Ulosi wina unanena kuti: “masiku otsiriza adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta. Pakuti anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, . . . osamvera makolo, osayamika, osakhulupirika, osakonda achibale awo, osafuna kugwirizana ndi anzawo, onenera anzawo zoipa, osadziletsa, oopsa, osakonda zabwino, . . . odzitukumula ndiponso onyada, okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu.” (2 Timoteyo 3:1-4) Ndi zoona kuti kwa zaka zambiri anthu ena akhala akusonyeza makhalidwe amenewa. Koma panopa ndi mmene anthu ambiri alili.

Maulosiwa anayamba kukwaniritsidwa m’chaka cha 1914. Ngakhale anthu olemba mbiri, akatswiri a nkhani za ndale komanso olemba mabuku amatsimikiza kuti zinthu zinasintha kwambiri kuyambira m’chakachi. Mwachitsanzo, Peter Munch yemwe ndi katswiri wolemba mbiri ku Denmark analemba kuti: “Kungoyambira pomwe nkhondo yoyamba inamenyedwa mu 1914, zinthu zinasintha kwambiri m’mbiri ya anthu. Zinangokhala ngati tachoka m’nyengo imene chilichonse chinkaoneka kuti chili m’chimake, n’kulowa m’nyengo ya mavuto okhaokha, chidani komanso yomwe kulikonse anthu amangoona kuti si otetezeka.”

Komabe zomwe zikuchitikazi zikusonyeza kuti zinthu zikhala bwino kutsogoloku. Zikutithandizanso kudziwa kuti posachedwa Ufumu uyamba kulamulira dziko lapansili. Ndipotu Yesu atafotokoza za mavutowa, ananenanso za chinthu china chosangalatsa chomwe chidzakhale mbali ya chizindikirochi. Iye anati: “Uthenga wabwino uwu wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”​—Mateyu 24:14.

Uthenga wabwino umenewu ndi umene a Mboni za Yehova amalalikira. Ndipo magazini yawo yodziwika kwambiri ili ndi mutu wakuti Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova. Nthawi zambiri magazini ya Nsanja ya Olonda imafotokoza zinthu zochititsa chidwi zomwe Ufumu wa Mulungu udzachitire anthu padzikoli.

MMENE UFUMU WA MULUNGU UDZAYAMBIRE KULAMULIRA

Mfundo 4 zotsatirazi zikusonyeza zimene zidzachitike:

  1. Ufumuwu sudzalamulira pogwiritsira ntchito anthu andale a padzikoli.

  2. Olamulira andale, pofunitsitsa kukhalabe pa maudindo awo, adzakana ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu.​—Salimo 2:2-9.

  3. Ufumu wa Mulungu sudzalekerera koma udzawononga maboma andale omwe amafuna kuti azingolamulirabe anthu. (Danieli 2:44; Chivumbulutso 19:17-21) Mabomawa adzawonongedwa pankhondo yomaliza, yomwe imatchedwa Aramagedo.​—Chivumbulutso 16:14, 16.

  4. Onse amene amamvera mokhulupirika Ufumu wa Mulungu, adzapulumuka pa nkhondo ya Aramagedo ndipo adzalowa m’dziko latsopano. Iwowa ndi amene adzapange gulu lomwe Baibulo limati “khamu lalikulu.” Ndipo anthuwa alipo mamiliyoni.​—Chivumbulutso 7:9, 10, 13, 14.

KODI ANTHU ADZAPINDULA BWANJI UFUMU UKAMADZALAMULIRA?

Kuti munthu adzakhale nzika ya Ufumu wa Mulungu ayenera kuphunzitsidwa kaye. N’chifukwa chake Yesu popemphera ananena kuti: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.”​—Yohane 17:3.

Anthu akafika podziwa bwino Yehova Mulungu n’kumamuona kuti ndi weniweni, amapindula m’njira zambiri. Tiyeni tingokambiranako njira ziwiri: Yoyamba, amakhala ndi chikhulupiriro cholimba mwa Mulungu. Ndipo chikhulupiriro chimenechi, chomwe chimabwera chifukwa cha umboni womwe apeza, chimawathandiza kutsimikizira kuti Ufumu wa Mulungu ndi weniweni komanso kuti uyamba kulamulira posachedwa. (Aheberi 11:1) Chachiwiri, amayamba kukonda kwambiri Mulungu ndi anthu ena. Kukonda Mulungu kumawachititsa kuti azimumvera ndi mtima wonse. Pomwe kukonda anthu ena, kumawachititsa kutsatira mfundo yofunika kwambiri imene Yesu anaphunzitsa yakuti: “Zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muwachitire zomwezo.”​—Luka 6:31.

Monga mmene bambo amene amakonda ana ake amachitira, Mlengi wathu nayenso amatifunira zabwino. Amafuna tidzapeze moyo womwe Baibulo limatchula kuti “moyo weniweniwo.” (1 Timoteyo 6:19) Moyo umene tikukhala panopa si ‘moyo weniweni.’ Tikutero chifukwa anthu ambiri akukumana ndi mavuto aakulu ndipo zimakhalanso zovuta kuti apeze zinthu zofunika. Kuti mudziwe mmene “moyo weniweniwo” udzakhalire, tiyeni tikambirane zinthu zina zosangalatsa zomwe Ufumu wa Mulungu udzachitire nzika zake.

Ufumu ukadzayamba kulamulira, anthu adzakhala otetezeka komanso adzakhala ndi chakudya chambiri