Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

BOMA LIMENE LIDZATHETSE MAVUTO

“Ndipo Mtendere Sudzatha”

“Ndipo Mtendere Sudzatha”

Bungwe la United Nations likulimbikitsa anthu padziko lonse kuti akhale ogwirizana pa chilichonse chimene chikuchitika padzikoli monga kuteteza chilengedwe komanso kuonetsetsa kuti ufulu wa munthu aliyense ukulemekezedwa. N’chifukwa chiyani bungweli likuchita zimenezi? A Maher Nasser omwe ndi mkulu mu ofesi ya zofalitsa nkhani m’bungweli, anafotokoza kuti: “Kulikonse kuli mavuto a kusintha kwa nyengo, kuphwanya malamulo, kusiyana pakati pa anthu olemera ndi osauka, mikangano yosatha, kuthawa kwa anthu m’madera awo, zauchigawenga komanso matenda opatsirana.”​—UN Chronicle.

Anthu enanso akhala akulimbikitsa zoti dziko lonse lapansi likhale ndi boma limodzi. Ena mwa anthuwa anali a Dante (1265-1321) a ku Italy komanso a Albert Einstein (1879-1955) a ku Germany. A Dante, anali katswiri wa zandale, kaganizidwe ka anthu komanso wolemba ndakatulo. Iwo ankaona kuti mtendere sungatheke ngati anthu ali ogawanika pa nkhani zandale. Ndipo anabwereza mawu a Yesu Khristu akuti: “Ufumu uliwonse wogawanika umatha.”​—Luka 11:17.

Pambuyo pa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse yomwe panaphulitsidwa mabomba awiri a nyukiliya, a Albert Einstein omwenso anali katswiri wa za sayansi, analembera kalata bungwe la United Nations. M’kalatayo yomwe inaikidwanso mu nyuzipepala, iwo anati: “Bungwe la United Nations liyenera kuchita zinthu mwachangu pokhazikitsa mfundo zothandiza kuti padzikoli pakhale mtendere. Liyeneranso kukhazikitsa mwamsanga mfundo zothandiza kuti pa dziko lonse tikhale ndi boma limodzi.”

Koma kodi pali amene anganene motsimikiza kuti akuluakulu a bomalo sakanachita zakatangale, kugwiritsa ntchito molakwika udindo wawo ndiponso kuchitira anthu nkhanza? Kapena akanachita zinthu ngati mmene olamulira ambiri amachitira? Kuganizira mafunsowa kukutikumbutsa zimene a Lord Acton omwe ndi katswiri wolemba mbiri wa ku Britain, ananena. Iwo anati: “Udindo umachititsa munthu kuyamba zachinyengo ndipo udindowo ukamakula, zachinyengo nazonso zimawonjezeka.”

Komabe kuti anthu tonse tikhale pamtendere weniweni, tiyenera kukhala ogwirizana. Koma kodi zimenezi zingadzathekedi kapena angokhala maloto chabe? Baibulo limanena kuti zimenezo ndi zotheka ndipo zidzachitikadi. Kodi zidzachitika bwanji? Boma lokhazikitsidwa ndi anthu andale omwe amachita zachinyengo silingakwanitse kuchita zimenezi. Koma zidzatheka ndi boma limene Mulungu adzakhazikitse. Bomali likadzayamba kulamulira, zidzaonekeratu kuti Mulungu yekha ndi amene ali ndi ufulu wolamulira. Koma kodi boma limeneli ndi liti? Baibulo limatchula bomali kuti “Ufumu wa Mulungu.”​—Luka 4:43.

“UFUMU WANU UBWERE”

Yesu ankanena za Ufumu wa Mulungu pamene anati: “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike . . . pansi pano.” (Mateyu 6:9, 10) Choncho Ufumu wa Mulungu udzaonetsetsa kuti chifuniro cha Mulungu chikuchitika padziko lapansili. Chifuniro cha Mulungu sichingafanane ndi cha anthu odzikonda komanso ongofuna udindo.

Ufumu wa Mulungu umadziwikanso kuti “Ufumu wakumwamba.” (Mateyu 5:3) Zili choncho chifukwa ufumuwu ukamadzalamulira dziko lapansi, uzidzalamulira kuchokera kumwamba. Zimenezi zikusonyeza kuti anthu sadzafunikanso kupereka ndalama za misonkho poyendetsa bomali. Zidzakhala zosangalatsatu kwambiri nthawi imeneyo.

Mawu akuti “ufumu,” akusonyeza kuti Ufumu wa Mulungu ndi boma lolamulidwa ndi mfumu. Mulungu anapatsa Yesu Khristu udindo wolamulira ngati mfumu. Ponena za Yesu, Baibulo limati:

  • “Paphewa pake padzakhala ulamuliro. . . Ulamuliro wake . . . udzafika kutali ndipo mtendere sudzatha.”​—Yesaya 9:6, 7.

  • “Anamupatsa ulamuliro, ulemerero, ndi ufumu kuti anthu a mitundu yosiyanasiyana, olankhula zinenero zosiyanasiyana azimutumikira. Ulamuliro wake . . . sudzatha.”​—Danieli 7:14.

  • “Ufumu wa dziko wakhala ufumu wa Ambuye wathu [Mulungu] ndi wa Khristu wake.”—Chivumbulutso 11:15.

Pokwaniritsa zimene zili m’pemphero lachitsanzo la Yesu, Ufumu wa Mulungu udzachititsa kuti chifuniro cha Mulungu chiyambe kuchitika padziko lapansili. Pa nthawiyo anthu onse adzaphunzira kusamalira dzikoli kuti lidzakhalenso Paradaiso komanso kuti lidzadzaze ndi zinthu zamoyo ngati poyamba.

Koposa zonse, Ufumu wa Mulungu udzaphunzitsa nzika zake mfundo zofanana ndipo sikudzakhalanso kugawikana. Lemba la Yesaya 11:9 limati: “Sizidzavulazana kapena kuwonongana . . . chifukwa dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa Yehova ngati mmene madzi amadzazira nyanja.”

Zimene bungwe la United Nations limafuna zoti anthu onse padzikoli azikhala mwamtendere komanso mogwirizana, zidzatheka ndi Ufumu wa Mulungu. Ponena za anthuwo lemba la Salimo 37:11 limati: “Adzasangalala ndi mtendere wochuluka.” Pa nthawiyo mawu akuti “kuphwanya malamulo,” “kuonongeka kwa chilengedwe,” “umphawi” komanso “nkhondo” adzaiwalika. Koma kodi Ufumu wa Mulunguwu udzayamba liti kulamulira? Kodi padzachitika zotani kuti Ufumuwo uyambe kulamulira? Nanga tidzapindula bwanji ndi ulamuliro umenewo? Tikambirana zimenezi m’nkhani yotsatira.