N’chifukwa Chiyani Timavutika, Kukalamba Komanso Kufa?
Mlengi wathu amationa kuti ndife ana ake. Choncho amafuna kuti tisamavutike. Komabe timakumana ndi mavuto ambiri. N’chifukwa chiyani zili choncho?
Makolo Athu Oyambirira Ndi Amene Anachititsa Kuti Tizivutika
‘Uchimo unalowa m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzera mwa uchimo, imfayo n’kufalikira kwa anthu onse.’—AROMA 5:12.
Mulungu analenga makolo athu oyambirira, Adamu ndi Hava, ali ndi maganizo komanso matupi angwiro. Anawapatsa malo abwino kwambiri oti azikhalamo otchedwa munda wa Edeni. Anawauza kuti azidya zipatso za mitengo yonse imene inali m’mundamo, kupatulapo zipatso za mtengo umodzi. Komabe, Adamu ndi Hava anasankha kuti adye zipatso za mumtengo woletsedwawo, ndipo limeneli linali tchimo. (Genesis 2:15-17; 3:1-19) Chifukwa chakuti sanamvere, Mulungu anawathamangitsa m’mundamo, ndipo moyo wawo unakhala wovuta kwambiri. Patapita nthawi anakhala ndi ana, ndipo moyo wa anawo unakhalanso wovuta kwambiri. Onse anayamba kukalamba komanso kufa. (Genesis 3:23; 5:5) Timadwala, kukalamba komanso kufa chifukwa tinachokera ku banja loyambirira limenelo.
Mizimu Yoipa Imachititsanso Kuti Tizivutika
“Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.”—1 YOHANE 5:19.
“Woipayo” amene akutchulidwa pa lembali ndi Satana. Iye ndi mngelo amene anapandukira Mulungu. (Yohane 8:44; Chivumbulutso 12:9) Patapita nthawi, angelo enanso anakhala ku mbali ya Satana. Iwo amatchedwa kuti ziwanda. Mizimu yoipa imeneyi imagwiritsa ntchito mphamvu imene ili nazo kuti isocheretse anthu n’cholinga choti asiye kumvera Mlengi. Imalimbikitsa anthu ambiri kuchita zinthu zoipa. (Salimo 106:35-38; 1 Timoteyo 4:1) Satana ndi ziwanda zake amasangalala akamachititsa kuti anthu azivutika.
Nthawi Zina Timavutika Chifukwa cha Zosankha Zathu
“Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.”—AGALATIYA 6:7.
Timakumana ndi mavuto osiyanasiyana chifukwa tinatengera uchimo kwa makolo athu oyambirira komanso tikukhala m’dziko limene akulilamulira ndi Satana. Koma nthawi zina anthu amadzibweretsera okha mavuto. Motani? Akachita zinthu zoipa kapena akasankha zinthu mopanda nzeru nthawi zambiri amakumana ndi mavuto. Koma ngati anthu akuchita zinthu zabwino amakololanso zinthu zabwino. Mwachitsanzo, bambo yemwe ndi oona mtima, amene amagwira ntchito mwakhama komanso amakonda banja lake, amapeza zinthu zabwino zambiri komanso banja lake limakhala losangalala. Koma bambo amene amakonda kutchova njuga, kumwa mowa kwambiri kapena ndi waulesi akhoza kudzisaukitsa komanso kusaukitsa banja lake. Choncho tikamamvera Mlengi wathu timasonyeza kuti ndife anzeru. Iye amafuna kuti tizikolola zinthu zabwino zambiri, kuphatikizapo “mtendere wochuluka.”—Salimo 119:165.
Tikukhala ‘M’masiku Otsiriza’
“Masiku otsiriza . . . , anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, . . . osamvera makolo, . . . osadziletsa, oopsa, osakonda zabwino.”—2 TIMOTEYO 3:1-5.
Monga mmene lembali likunenera, zimenezi n’zomwe anthu akuchita masiku ano. Makhalidwe awo amapereka umboni wokwanira wosonyeza kuti tikukhala ‘m’masiku otsiriza’ a dziko loipali. Malemba ananeneratunso kuti tidzazindikira kuti tikukhala m’masiku otsiriza tikadzaona nkhondo, njala, zivomezi zamphamvu komanso miliri. (Mateyu 24:3, 7, 8; Luka 21:10, 11) Zinthu zonsezi ndi zimene zimachititsa kuti tizivutika komanso kufa.