Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

GALAMUKANI! Na. 1 2024 | Kodi Ulemu Unapita Kuti?

Masiku ano anthu aulemu akusowa, ndipo ena amachita kudabwa akaona wina akuchita zinthu mwaulemu.

Mwachitsanzo, anthu ambiri sasonyeza ulemu kwa anzawo, makolo awo, achikulire ngakhalenso kwa apolisi, mabwana awo ndi aphunzitsi. Kuwonjezera pamenepo, anthu amalemba komanso kulankhula mawu achipongwe okhudza anthu ena pa intaneti. Nkhani ina imene inalembedwa m’magazini inayake (Harvard Business Review) inanena kuti “n’zoonadi kuti anthu ambiri” ndi opanda ulemu. Inanenanso kuti anthu “akupereka malipoti oti ena awachitira zinthu zamwano ndipo akhala akupereka malipoti amenewa kwa kanthawi ndithu tsopano.”

 

Kulemekeza Ena

Onani chifukwa chake tiyenera kulemekeza anthu ena komanso zimene tingachite kuti tiziwalemekeza.

Kulemekeza Moyo

Onani malangizo a m’Baibulo a mmene tingasonyezere kuti timalemekeza moyo wathu komanso wa anthu ena.

Kulemekezana M’banja

Banja lililonse likhoza kukhala losangalala ngati aliyense m’banjamo akulemekeza mnzake.

Kudzilemekeza

Kuphunzira Baibulo kungathandize anthu kuti azidzilemekeza komanso asinthe moyo wawo.

Kodi Ulemu Unapita Kuti?

Werengani nkhani zokhudza ulemu zomwe zili m’magaziniyi komanso zimene a Mboni za Yehova akuchita pothandiza anthu a m’dera lawo kuti azisonyeza ulemu.